1 Chipano kukhala Muyahudi kuthangatila chiyani? Kapina kuchita mdulidwe kuthangatila chiyani? 2 Zenedi, kukhala Muyahudi kuthangatila kupunda. Poyambila Mnungu wadapacha Ayahudi Uthenga wake. 3 Nambho siikhale bwanji ngati akumojhi wake sadakhulupilile? Bwanji, chindhu chimenecho sichichoche kukhulupilika kwa Mnungu? 4 Notho! Mnungu wakhala wokhulupilikape, ata ngati kila mundhu ni wamthila. Ngati umo yalembedwa mamalembo ya Mnungu,
"Ndhawi zonjhe yapo mkamba, mawu yanu ni uzene,
ni Pamalamulo, imwe mkhoza."
5 Wandhu akhoza kufunjha kuti voipa vathu vilangiza kuti Mnungu wakamba uzene, Bwanji, tikambe kuti walakwila kutilanga? 6 Notho! Ngati Mnungu siwadakakhala wauzene, wadakakhoza bwanji kulilamula jhiko?
7 Wandhu akhoza kukamba, ngati kosa khulupilile kwatu kwachita wandhu wina aone kuti Mnungu ni wazene, chipano Mnungu siwafunika kutitana ife kuti woyomwa, ni siwafunika kunilanga! 8 Kumeneko ni sawa ni kukamba kuti, "Tiyeni tiyendekele kuchita voipa kuti tipate vabwino!" Wandhu wina atinamizila ata ife kuti tiyaluza chimwecho. Wandhu yawo akamba chimwecho salangidwe kwa voipa vawo!
9 Tikambe chiyani chipano? Bwanji, ife Ayahudi tili bwino kupitilila wina? Notho! Pakuti nathokamba poyamba, kuti Ayahudi ni wandhu amaiko yina wonjhe ali panjhi pa ulamulilo wa machimo. 10 Ngati umo yalembeledwa Mmalembo ya Mnungu,
"Palibe ata mundhu mmojhi uyo wachita yayo yamkwadilicha Mnungu!
11 Palibe mundhu waliyonjhe uyo wamlambila Mnungu, ni palibe mundhu uyo wamfunafuna Mnungu.
12 Wandhu wonjhe amsiya Mnungu,
palibe uyo wachita ivo vifunika kwa Mnungu,
palibe ata mmojhi.
13 Makamwa yawo yajhala mawu yoipa,
Malilime yao yajhala unami,
Mkamwa mwao yachoka mau yayo yali ni sumu ngati ya njoka.
14 Makamwa yao yajhala mawu ya kwalesa wandhu wina ni mawu yayo yapweteka.
15 Wandhu amenewo ayangukila kupita kupha wandhu,
16 paliponjhe yapo akhala ni wandhu, awananga ni kwaavutiticha wina.
17 Ayiiwo saajhiwa kukhala ni wandhu wina kwa mtendele,
18 samulemekeza Mnungu ata pang'ono."
19 Tijhiwa kuti thauko lili ndande ya wandhu ali panjhi pa thauko limeneno, ni sakhoza kukhala ni chilichonjhe cho namizila. Ni jhiko lonjhe lili panjhi pa lamulo la Mnungu. 20 Pakuti palibe mundhu waliyonjhe siwavomelezeke kuti ni wokhulupilika pachogolo pa Mnungu, kwa kuligwila thauko, njhito ya thauko ni kumlangizape mundhu kuti wachita machimo.
21 Nambho chipano njila ya kwachita wandhu avomelezeke kwa Mnungu ili padanga, popande kukhulupilila thauko, osati ngati umo lidakambila thauko la Musa ni malembo ya alosi a Mnungu vonjhe vikambilila chindhu chimenecho. 22 Mnungu waavomela wandhu kuti ni woyela kwa njila ya chikhulupi chao kwa Yesu Kilisito, Mnungu wachita chimwecho kwa wonjhe akhulupilila, siwapatula Ayahudi ni wandhu yawo osati Ayahudi. 23 Wandhu wonjhe achita machimo, palibe uyo wali wabwino ni wonjhe ataiza kulemekezedwa ni Mnungu. 24 Nambho kwa mbhaso ya ubwino wa Mnungu, wandhu wonjhe avomelezedwa kuti ni abwino pachogolo pa Mnungu kwa njila ya Yesu Kilisito uyo wadaombola. 25 Mnungu wadamchocha Yesu kuti, kwa mwazi wake wakhale njila ya kwachochela wandhu machimo yao kwa kumkhulupilila. Wadachita chimwecho dala wakhoze kulangiza kuti iye ni woyela. Kale Mnungu wadalimbila mtima popande kwaalanga machimo yao, 26 Nambho saino wayachucha machimo ya wandhu, kuti wakhoze kulangiza ubwino wake. Wachita chimwecho, dala walangize kuvomelezeka kwake ndhawi ino, iye wavomela wandhu wajha amkhulupilila Yesu.
27 Chipano tikhoza kujhidama chiyani? Palibe chojhidamila! Ndande ife sitiwelengedwa kukhala wovomelezeka pachogolo pa Mnungu nambho kwa kumkhulupilila Yesu. 28 Pakuti, tiona kuti Mnungu wawelengedwa kukhala woyela kwa njila yomkhulupilila Yesu, nambho osati kwa kuchita umo lifunila Thauko. 29 Bwanji, Mnungu ni Mnungu wa Ayahudipe kapina ni Mnungu wa maiko yonjhe? Notho, ni Mnungu wa amaiko yonjhe, nawonjho ni Mnungu wao. 30 Mnungu ni mmojhi, naye siwachite Ayahudi kukhala abwino kwa kumkhulupilila iye, ni wandhu amaiko yina kwa kumkhulupilila. 31 Bwanji, yapo tisisitiza chikhulupi, bwanji, mate yake thauko ili lilibe phindu? Notho! Nambho tikakhala ni chikhulupi sikwaniliche yonjhe yayo yaagizidwa ni Thauko.