Publicidade

Marcos 15

Yesu wapelekedwa pachogolo pa Pilato

1 Umawamawa, ajhukulu wakulu adachita msonghano ni achogoleli, ni oyaluza thauko, adalamula kumpeleka Yesu kwa Pilato, iye wadali mchogoleli uyo wadachoka ku Loma. Chimwecho adammanga ni kumpeleka kwa Pilato. 2 Pilato wadamfunjha Yesu, "Bwanji iwe nde Mfumu wa ayahudi?"

Yesu wadayangha, "Yetu ngati umo iwe ukambila."

3 Ajhukulu wakulu adampacha Yesu mlandu kwa vindhu vambili. 4 Pilato wadamfunjhanjho Yesu, "Bwanji siuyangha chalichonjhe? Vechela umo akupachila mlandu kwa vindhu vambili." 5 Nambho Yesu siwadayanghe mawu, chimwecho Pilato wadazizwa.

Yesu walamulidwa kuphedwa

6 Kila pwando la Pasaka, pilato wadali ni chikalidwe cha kummasulila mundhu mmojhi wa mndende uyo wamafunika ni wandhu. 7 Nyengo imeneyo, kudali ni mundhu mmojhi wamatanidwa Balaba, wadamangidwa pamojhi ni olakwa wina yawo adachita fujho ni kupha. 8 Gulu la wandhu ambili adamchata Pilato ni kumpembha wachitile ngati mujha chili chikhalidwe chake. 9 Pilato wadaafunjha, "Bwanji, mfuna nimsiilile mfumu wa a Yahudi?" 10 Pilato wadakamba chimwecho ndande wadajhiwa kuti wakulu a jhukulu, ampeleka Yesu kwakiye ndande amamuonela njhanje.

11 Nambho wakulu a jhukulu adaakhwilizila wandhu ampembhe Pilato wamsiil bile Balaba. 12 Pilato wadalifujhanjho, gulu la wandhu, "Chipano mfuna nimchite chiyani mundhu uyu mumtana Mfumu wa a Yahudi?" 13 Wadhu wonjhe adakwezanjho mvekelo, "Mpachike pamtanda." 14 Nambho pilato waadafunjha, "Bwanji, walakwa chiyani?"

Nambho anyiiwo adaendekela kubula pokoso kwa mbhavu za mbili, "Mpachike pamtanda."

15 Pilato wadafuna kulikondwelecha gulu la wandhu, chimwecho wadamsiilila Balaba wachoke mndende. Pamenepo wadalamula Yesu wabulidwe mikwapulo, ndiipo ampachike pamtanda.

Asikali amdelela Yesu

16 Ndiipo anyiwajha asikali adamtenga Yesu adapitanayo kukhomo kwa Pilato, nyumba imeneyo idatanidwa Plaitolio. Mmenemo adakomana asikali ni achanjao wonjhe. 17 Adamveka Yesu njhalu ya chifumu, adamkonjela nghata ya minga ni kumveka kumutu. 18 Ndiipo adayamba kumlonjela, "Moni Mfumu wa a Yahudi!" 19 Adambula ni mkwapulo kumutu, adamlavulila malovu, adamgwadila ni kumlambila. 20 Ndiipo yapo adamaliza kumdelela, adamvula ijha njhalu ya chifumu, ni kumveka njhalu zake. Ndiipo adamchocha kubwalo ni kumpachika pamtanda.

Yesu wapachikidwa pamtanda

21 Yapo adali mnjila, adapezana ni mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Simoni, mundhu wa ku Kilene, tate wao Alekizanda ni Lufo. Mundhu mmeneyo wamachokela kumunda wamatopita kumjhini, asikali adamkakamiza wautenge mtanda wa Yesu. 22 Ndiipo, adampeleka Yesu mbaka kumalo kumatanidwa Goligota, mate yake, "Pamalo pa fuvu la mutu." 23 Adampacha Yesu divai iyo adasingizana ni mnghwala uwo utanidwa manemane, nambho iye wadakana kuimwa. 24 Ndiipo, adampachika Yesu pamtanda, ni kugawana njhalu zake kwa kuzibulila ghudughudu, kuti ajhiwe ghudughudu silimgwele ya ni kuti watenge njhalu. 25 Idali saa tatu umawa yapo adampachika Yesu pamtanda. 26 Ni mlandu wake udalembedwa chimwechi, "Mfumu wa a Yahudi." 27 Chinchijha Yesu wadapachikidwa pamojhi ni olanda awili pamitanda, mwina kujhanja lake la kwene ni mwina ku jhanja lake la kumanjele. 28 Pamenepo yadakwana Malembo Yoyela yayo yalembedwa, "Wadaikidwa pamojhi ni olanda."

29 Wandhu amapita pamalo pamenepo amatingiza mitu yao, adamtukwana niakamba, "Iwe udakamba ukhoza kugomola nyumba ya Mnungu ni kuimanganjho siku zitatu! 30 Chipano ujhiombole wamwene chika pamtandapo!" 31 Chimchijha wakulu wa ajhukulu pamojhi ni oyaluza thauko adampepula Yesu, niakamba, "Wadaombola wandhu ambili nambho siwakhoza kujhiombola mwene! 32 Tiyeni timuone kilisito, Mfumu wa a Isilaeli, chipano wachike kuchokela pamtanda, niife sitimkhulupilile."

Chimchijha wandhu anyiwajha awili adampachikidwa pamojhi ni Yesu adamtukwana.

Yesu wafela pamtanda

33 Yapo idafika saa sita usana, jhiko lonjhe lidavinikilidwa ni mdima, mdima uwo udakhala kwa masaa ya tatu. 34 Saa tisa ujhulo, Yesu wadalila kwa mvekelo waukulu, "Eloi, Eloi, Lema Sabakitani" Mate yake, "Mnungu wanga, Mnungu wanga, ndande yanji mwanisiya?" 35 Wandhu wina adaima pajha yapo adavela chimwecho, adakambilana, "Vechelani, wamtana mlosi Eliya." 36 Mundhu mmojhi wadathamanga, ni kubiza buula mu divai yolujhuka, ni wadaika pamwamba pa mkwapulo, ni wadaiika pakamwa pa Yesu niwakamba, "Tilinde tione ngati mlosi Eliya siwajhe kumchicha pamtanda!" 37 Yesu wadalila kwa mvekelo, ndiipo wadamwalila.

38 Ndiipo panzia ilo lidali pamalo poyela mnyumba ya Mnungu lidang'ambika vidufya viwili kuchokele kumwamba mbaka panjhi. 39 Wamkulu mmojhi wa asikali uyo wadaima pachogholo pa mtanda yapo wadaona umo Yesu wadamwalilila, wadakamba, "Zenedi mundhu huyu wadali Mwana wa Mnungu!"

40 Pamenepo adalipo wachikazi wina amapenya kwa kutali, pakati pao wadalipo ni Malia wa kumujhi wa Magidala, Salome ni Maliya maye wachi Yakobo wang'ono ni Yusufu. 41 Wachikazi achameneo adamchata Yesu yapo wadali ku Galilaya ni kumtumikila. Kudali ni wachikazi wina ambili adajha ku Yelusalemu pamojhi ni iye.

Yesu wazikidwa

42 Ujhulo yapo udawandikila. Pakuti lidali Siku lo konjekela kupumulila, 43 wadajha Yusufu uyo wamachokela ku mujhi wa Alimasaya, mundhu wa bwalo la milandu, wamalemekezeka kupunda wadafika. Mundhu mmeneyo wamalindililila kujha kwa Ufumu wa Mnungu. Chimwecho Yusufu wadampitila Pilato popande kumuopa, wadampembha wampache thupi la Yesu. 44 Pilato wadazizwa yapo wadavela kuti Yesu tayali wathomwalila. Ndiipo, wadamtana wamkulu wa asikali ni kumfunjha ngati Yesu wathomwalila. 45 Pilato yapo wadakambidwa ni yujha wamkulu wa asikali kuti Yesu wathomwalila, wadamvomeleza Yusufu walitenge thupi la Yesu. 46 Yusufu wadaghula sanda, wadalichicha panjhi thupi la Yesu, wadalivilingila sanda. Adaliika pambhanga iyo idakumbidwa pa mwala wolimba. Ndiipo wadaugunghulicha mwala pakhomo pa ijha mbhanga. 47 Malia wa ku Magidala ni Maliya make wa Yusufu adapaona pamalo yapo lidaikidwa thupi la Yesu.

Veja também

Publicidade
Marcos
Ver todos os capítulos de Marcos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-