1 Yesu wadayendekela kukamba, "Zenedi nikukambilani, pali wina pampano samwalila mbaka yapo sauone Ufumu wa Mnungu ni ujha kwa mbhavu."
2 Pambuyo pa masiku sita, Yesu wadaatenga Petulo ni Yakobo ni Yohana, wadapita nawo ku phili, kumalo kopande wandhu. Pamwepo Yesu wadang'anamuka nghope yake pamaso pawo, 3 njhalu zake zidali zoyelambee, palibe mundhu pajhiko uyo wadakhoza kuzichapa ni kuhala zoyela mbee ngati zijha. 4 Pampajha, oyaluzidwa atatu wajha wadaaona alosi Eliya ni Musa niakamba ni Yesu. 5 Petulo wadamkambila Yesu, "Oyaluza, siikhale bwino ife tikhale pano. Chipano, timange visakasa vitatu, chimojhi chanu, chimojhi cha Musa, ni china cha Eliya." 6 Petulo siwadajhiwe chokamba ndande iye ni achanjake adaopa kupunda. 7 Ndiipo udatulukila mtambo ni kwavinikila wonjhe, ni mvekelo wa Mnungu udaveka kuchokela mujha mumtambo, "Uyu ni mwana wanga wa mmuna uyo nimkonda, mvecheleni." 8 Pampajha yapo adapenya uku ni uku, siadamwone mundhu mwina pamojhi ni anyiiwo, nambho Yesu pe.
9 Ndiipo, Yesu yapo amachika kuphili, wadaakaniza oyaluzidwa wake sadamkambila mundhu waliyonjhe vindhu ivo adaviona, mbaka yapo iye Mwana wa Mundhu siwahyuke. 10 Adagwila lamulo lijha, nambho adajhifunjha, "Kuhyuka mate yake chiyani." 11 Oyaluzidwa wake adamfunjha Yesu, "Ndande yanji oyaluza athauko akamba ifunika Eliya wajhe uti wakali osajhe kilisito?" 12 Yesu wadaayangha, "Yetu, Eliya wakujha uti kuika kilachindu bwino. Ata chimwecho, ndande yanji yalembedwa mmalembo yoyela kuti Mwana wa Mundhu wafunika kuvutika ni kudeleledwa? 13 Nambho nikukambilani, Eliya wathokujha, ni anyiiwo adamchita icho amachifuna ngati umo yadalembedwela mmalembo yoyela."
14 Yesu pamojhi ni oyaluzidwa wake atatu wajha, yapo adafika kwa oyaluzidwa wina adaliona gulu lalikulu la wandhu ni oyaluza athauko akumojhi amathochuchana nao. 15 Pampajha, lijha gulu la wandhu lidaona, wonjhe adazizwa kupunda, ni adamthamangila ni kumlonjela. 16 Yesu wadaafunjha oyaluzidwa wake, "Bwanji, mchuchana nao chiyani?" 17 Mundhu mmojhi kuchokela mgulu la wandhu, wadamuyangha Yesu, "Oyaluza, nakupelekelani mwana wanga kwanu, wali ni chiwanda icho chamchita wakhale bubu. 18 Ndhawi yaliyonjhe yapo chimzamwa chimtaya panjhi ni kumchita wachoke ni matovu mkamwa, ni kutafuna mano yake, ni watouma thupi lake. Nidaapembha oyaluzidwa wako amchoche chiwanda chimenecho, nambho siadakhoze."
19 Yesu wadaakambila, "Anyiimwe mbadwa ulibe chikhulupililo, sinikhale ni anyiimwe mbaka siku liti? Sinikulimbileni mtima mbaka siku lanji? Majhanayoni pano mwana mmeneyo." 20 Chimwecho adampeleka kwa Yesu yujha wadali ni chiwanda.
Pampajha, chijha chiwanda yapo chidamwona Yesu, chidamchita wakhale ni njili, wadangwa panjhi, wadawalauka ni kuchocha matovu mkamwa. 21 Yesu wadamfunjha tate wayujha mwana, "Bwanji, utenda uwu wampata kuyambila siku lanji?" wadamuyangha, "Kuyambila yapo wadali mwana. 22 Ninyengo za mbili chiwanda chimenecho chimgwecha pamoto ni pamajhi, kuti chimphe. Nambho, ngati mkhoza kuchita chindhu, tilengele lisungu, utithangatile!" 23 Yesu wadamkambila, "Ngati uli ni chikhulupililo, yonjhe yakhozeka kwa uyo wakhulupilila." 24 Pampajha, tate wa yujha mwana wadalila kwa mvekelo, "Nikhulupilila! Nambho chikhulupililo changa chaching'ono, nithangatileni kuti nikhoze kukhulupilila."
25 Yesu yapo wadaona gulu la wandhu lichuluka kwa chisanga, wadachinyindila chijha chiwanda, "Iwe chiwanda umchita uyu mundhu kukhala wosakamba ni wosavela, nikulamula mchoke mnyamata uyu ni siudamlowanjho!" 26 Pampajha, chijha chiwanda chidatutuma ni kumgwecha njili ni kumchoka. Mwana yujha wadaoneka ngati wamwalila, ni wandhu ambili adakamba, "Wathomwalila!" 27 Nambho Yesu wadamgwila jhanja mnyamata yujha, wadamthangatila kunyakuka, nayo wadanyakuka.
28 Ndiipo, Yesu yapo wadalowa mnyumba, oyaluzidwa wake adamfunjha paokha, "Ndande yanji ife sitidakhoze kumchocha chiwanda chijha?" 29 Yesu wadaakambila, "Chiwanda ngati ichi sichikoza kuchoka, ingakhale kwa kupembhelape."
30 Yesu ni oyaluzidwa wake adachoka pamenepo, adayendekela ni ulendo kopitila Galilaya. Yesu siwadafune mundhu waliyonjhe wajhiwe uko wali, 31 ndande wamatowayaluza oyaluzidwa wake. Wadaakambila, "Ine Mwana wa Mundhu sinikidwe mmanja mwa wandhu, ni nawo sianimphe, siku la katatu sinihyuke." 32 Nambho oyaluzidwa wake siadajhiwe mate ya mawu yameneyo, ni adaopa kumfunjha.
33 Yesu ni oyaluzidwa wake yapo adafika kumujhi wa Kapelinaumu, adalowa mkati, ni Yesu wadaafunjha oyaluzidwa wake, "Yapo mdali mnjila mmachuchanilana chiyani?" 34 Nambho anyiiwo sadamuyanghe, pakuti amachuchana yani wali niukulu pakati pao.
35 Yesu wadakhala panjhi, ni wadaatana anyiwajha oyaluzidwa wake khumi ni awili ni kwakambila, "Mundhu waliyonjhe wakafuna kukhala woyamba, ifunika wakhale wothela ni wakhale mbowa wa wandhu wonjhe." 36 Ndiipo, wadamtenga mwana wamng'ono, ni kumwimika pakati pao, wadamvumbatila ni kwakambila, 37 "Mundhu waliyonjhe uyo wamlandila mwana wamng'ono ngati uyu ndande yaine wanilandila ine, ni siwanilandila inepe, chinchijha wamlandila Mnungu uyo wanituma."
38 Yahana wadamkambila Yesu, "Oyaluza tamuona mundhu mmojhi ni wachocha chiwanda kwa jhila lanu, tamkaniza ndande siwachoka mgulu lathu." 39 Yesu wadaakambila, "Simdamkaniza mundhu waliyonjhe wachita vodabwicha mwajhina langa. Pamwepo wanikambe kuipa. 40 Mundhu uyo siwachuchana ni ife, wali pamojhi ni ife. 41 Zenedi nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo siwakupacheni chikho cha majhi ya kumwa, ndande ya anyiimwe ni wandhu wake Kilisito, mundhu mmeneyo siwalandile mbhaso yake."
42 "Mundhu waliyonhje uyo siwamchitiche wana yawa anikhulupilila ine achite machimo, idakakhala bwino mundhu mmeneyo wamangwidwe mbhelo ya ikulu pakhosi ni kutaidwa mnyanja yamchele. 43 Ngati jhanja lako likakuchiticha uchite machimo, lidule! Mbasa kulowa mu umoyo wa muyaya popande jhanja limojhi, kusiyana kukhala ni manja yawili ni kulowa mmoto wa muyaya. 44 Mmenemo muli mafuchi yayo siyakufa, ni moto uwaka muyaya. Bibiliya zina za kale zilibe mzele uwu. Chimchijha chindhu ichi balibenjho pa mzele wa 48. 45 Ni mwendo wako ukakuchiticha uchite machimo, udule! Mbasa kulowa mu umoyo wa muyaya ulibe myendo umojhi, kusiyana ni kukhala ni myendo iwili ni kutaidwa mumoto wa muyaya. 46 Mmenemo muli mafuchi yayo siyakufa, ni moto wa muyaya. 47 Ni diso lako likakuchiticha uchite machimo, lizule, mbasa kulowa mu umoyo wa muyaya uku uli ni diso limojhipe, kusiyana kukhala ni maso yonjhe yawili ni kutaidwa mumoto wa muyaya. 48 Mmenemo muli mafuchi yayo siyakufa, ni moto uwo uwaka muyaya."
49 "Mnungu siwampitiche kila mundhu pamavuto yayo yali ngati moto, ni ngati umo wandhu atila mchele mnyama ikali yosabuchidwe. 50 Mchele ni wabwino, nambho ngati ukataiza kukoma kwake, siuthilidwe chiyani kuti ukomenjho? Mkhale ngati mchele uwo ukoma, ni mkhale kwa mtendele ni achanjanu."