1 Yesu wadachoka pamenepo ni kupita ku mujhi wa ku Nazaleti kumalo uku wadakulila, ni oyaluzidwa wake adamchata. 2 Siku lo Pumulila yapo lidafika, wadayamba kuyaluza mnyumba yokomanilana Ayahudi. Wandhu ambili yawo adamvela adazizwa kupunda ni adajhifunjha, "Bwanji, wayapata kuti mayaluzo yaya? Ekima yanji walinayo mbaka wachita vindu vodabwicha? 3 Uyu osati yujha wosepa mitengo, mwana wa Maliya ni achabale wake ni achi yakobo, ni Yusufu ni Yuda ni Simoni? Bwanji, achalongo wake siali pano ni ife?" Nianyiiwo adaipila kupunda ni, adamkana kumkhulupilila.
4 Yesu wadaakambila, "Alosi alemekezedwa kumalo konjhe, nambho saalemekezedwa ni wandhu amnyumba zawo, ni mmijhi yawo ni kwa achaabale wao."
5 Yesu siwadafune kuchita vodabwicha kumeneko, nambho wadaaikila manja odwala ochepa ni kwalamicha. 6 Yesu wadazizwa kupunda ndande ya kosakhulupilile kwawo.
Yesu wamaviyendela vijhivjhi vapafupi ni pajha, niwaayaluza wandhu. 7 Wadaatana wajha oyaluzidwa khumi ni awili, wadapacha ulamulilo wotopola viwanda, ni kwaatuma awiliawili. 8 Wadaalamula, "Simdatenga chindhu chalichonjhe ndande ya ulendo, nambho mtenge mpulupe. Simdatenga chakudya kapina thumba, kapina ndalama pachilolo. 9 Valani malapasi, nambho msidatenga njhalu zo ng'anamula." 10 Chinchijha wadaakambila, "Panyumba paliponjhe yapo siakulandileni, mkhale pamenemo mbaka yapo simuchoke. 11 Pamalo paliponjhe, wandhu yapo saakane kukulandilani ni kukuvechelani, chokani pamalo pamenepo ni kukung'undha lifumbi ilo lakhalila mmyendo mwanu kulangiza kuti asangha kukana kuulandila Uthenga wa Mnungu." 12 Chimwecho, adachoka, ni kupita kwaalalikila wandhu alape. 13 Amaachocha wandhu viwanda vambili, ni adaanyeka mafuta odwala ambili, ni kwalamicha.
14 Ndiipo, mfumu Helode wadavela nghani zimenezo zonjhe, pakuti Yesu wadajhiwika kumalo konjhe. Wandhu wonjhe adakamba, "Yohana Mbatizi wahyuka, wali ni mbhavu zochita vodabwicha ndande ni mlosi." 15 Nambho wandhu wina adakamba, "Uyu ni mlosi Eliya." Wina adakamba "Uyu ni mmojhi wa alosi akale."
16 Nambho Helode yapo wadapata nghani zimenezo, wadakamba, "Uyu ni Yohana Mbatizi, uyo nidamdula mutu, wahyuka."
17 Helode mwene wake wadalamula Yohana wagwilidwe, waikidwe mndende. Helode wadachita chimwecho ndande ya Helodia uyo wadamkwata, wamkazi mmeneyo wadali wamkazi wa Filipo mphwake wa Helode. 18 Helode wadamchitila chimwecho Yohana ndande wadamkambila, "Osati bwino iwe kumkwata wamkazi wa mphwako!"
19 Pamenepo Helodia wadamuipila kupunda Yohana, wamafuna kumpha, nambho siwadakhoze, 20 ndande Helode wamamlonda. Helode wamamuopa Yohana pakuti wadajhiwa kuti wadali mundhu wabwino pamaso pa Mnungu, chimwecho wamamsunga. Helode wamakonda kumvechela Yohana, ingakhale wamavutika kupunda yapo wamamaliza kumvechela.
21 Siku limojhi Helodia wadapata malo ya kumpha Yohana pa phwando lakubadwa kwa Helode. Helode wadaachitila phwando lalikulu mbowa zake, wakuluakulu asikali ni achogoleli aku jhiko la Galilaya. 22 Mwali wa Helodia yapo wadalowa pamalo pajha amachitila pwando, wadavina, wadamkondwelecha kupunda Helode ni alendo wake. Chimwecho mfumu Helode wadamkambila yujha mwali, "Pembha chalichonjhe icho ufuna, nane sinikupache." 23 Wadalumbila, "Sinikupache chilichonjhe icho siunipembhe, ine sinikupache, ata ngati nusu ya ufumu wanga sinikupache."
24 Pamenepo yujha mwali wadachoka, ni kupita kwafunjha maye wake, "Nipembhe chiyani?"
Nawo wajha amake adamuyangha "Pembha mutu wa Yohana Mbatizi." 25 Yujha mwali wadathamanga mbaka kwa mfumu nikumpembha, "Nipembha mnipache saino muliselo mutu wa Yohana Mbatizi."
26 Mfumu wadaona chisoni kupunda, nambho siwadakhoze kukana, ndande wadalumbila pachogolo pa alendo wake. 27 Pampajha mfumu wadamkambila asikali wajhe nawo mutu wa Yohana Mbatizi mliselo. Asikali uyo wadapita mndende, wadamdula mutu Yohana. 28 Ndiipo yujha asikali wadajhanawo mutu mliselo ni kumpacha mwali, ni iye mwali wadapacha amake. 29 Oyaluzidwa a Yohana yapo adavela nghani imeneyo, adapita kulitenga thupi la Yohana ni kulizika.
30 Anyiwajha atumwi adabwela kuchokela uko adatumidwa, ni adasonghana pachogolo pa Yesu, niadamkambila yonjhe yayo adayachita ni yajha amayaluza. 31 Yesu wadaakambila, "Tiyeni ife tekha pamalo yapo palibe wandhu, kuti tikapumulile pang'ono." Wadakamba chimwecho ndande kudali ni wandhu ambili kupunda yawo amajha pamenepo ni kuchoka, mbaka Yesu ni oyaluzidwa wake siamakhoze kupata ndhawi ya kudya chakudya ndande ya kwatumikila. 32 Ndiipo, adachoka okha kwa boti ni kupita kumalo yapo padalibe wandhu.
33 Nambho wandhu ambili yapo wadaona niachoka, adajhiwa uko apita. Chimwecho, wandhu ambili adachokela mmijhi yosiyanasiyana, adathamanga ni kwachogolela kufika. 34 Yesu yapo wadachika mboti, wadaliona gulu lalikulu la wandhu, wadaalengela lisungu ndande adali ngati mbelele zilibe owesa. Chimwecho wadayamba kwayaluza vindhu vambili. 35 Ujhulo yapo udajha, oyaluzidwa adamchata Yesu, adamkambila, "Pamalo pano ni paphululu, ni jhuwa litobila. 36 Waakambile wandhu apite mminda ni mvijhijhi va pafupi akajhigulile chakudya." 37 Nambho Yesu wadaakambila, "Mwachinawene wake mwapache chakudya." Ni anyiiyo adamfunjha, "Bwanji, tipite kugula mabumunda ya dinali miyambili ni kwapacha wandhu adye?" 38 Yesu waadafunjha, "Mli ni mabumunda yangati? Pitani mkapenye, mkaiwelenge." Yapo adawelenga, adamkambila, "Yalipo mabumunda yasano ni njhomba ziwili."
39 Ndiipo, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, waakambile wandhu akhale magulu mgulu pamachamba yayawisi. 40 Chimwecho adakhala magulu ya wandhu miya ni ya wandhu amsini. 41 Ndiipo, Yesu wadayatenga yajha mabumunda yasano ni zijha njhomba ziwili, wadapenya kumwamba, wadamuyamika Mnungu, ndiipo wadayadula yajha mabumunda. Wadaapacha oyaluzidwa wake kuti wagawile wandhu. Chinchijha wadagawila wandhu zijha njhomba ziwili. 42 Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. 43 Ndiipo oyaluzidwa wake adatondola vidufya va mabumunda ni njhomba ivo vidakhalila, ni adajhaza miseche khumi ni iwili. 44 Wachimunape yawo adadya yajha mabumunda adali ngati elufu zisano.
45 Pamwepo Yesu wadaalamula oyaluzidwa wake akwele mboti, amchogolele kupita ku kuchidya kwa nyanja mbaka Ku Betisaida, iye wamalilaila gulu la wandhu. 46 Yapo wadamaliza kwalaila wandhu, wadapita kuphili kupembhela. 47 Usiku yapo udalowa, lijha boti lidali pakatikati pa nyanja, Yesu wadali yokha pamtunda. 48 Ndiipo, Yesu wadaaona oyaluzidwa wake niavutika kwa kupalasa nghafi, ndande mbhepo imaabula kwa mbhavu. Mmalengakucha, Yesu wadayendela oyaluzidwa wake uku niwayenda pamwamba pa majhi, wamafuna kwapitilila. 49 Yapo adamwona ni wayenda pamwamba pa majhi, amaganizila udali mzilimu, adabula pokhoso. 50 Pakuti wonjhe adamwona, ni adaopa. Yesu wadaakambila, "Jhitileni mtima! Ni ine! Msadaopa!" 51 Ndiipo wadakwela mboti umo adali woyaluzidwa, ni mbhepo idasiya, oyaluzidwa wake adazizwa kupunda, 52 adali akali osajhiwe vodabwicha va mabumunda, ndande mitima yao idali yopapatala kukhulupilila.
53 Adayomboka nyanja ni kufika mjhiko la Genesaleti, ni kutaya ndondowe. 54 Yapo adachika mboti, pampajha wandhu adamjhiwa Yesu. 55 Ndiipo, kwa chisanga adazungulila mjhiko lonjhe, adayamba kwatenga wodwala pa vitala vawo, ni kwapeleka kumalo kujha adavela Yesu walipo. 56 Mmalo yonjhe yayo Yesu wamapita, mmijhi ni mvijhijhi kapina mmalo yonjhe. Wandhu amaika odwala paliwala, adampembha ata ngati amgwile njhalu zake, niwonjhe yawo adagafya njhonga ya njhalu yake adalama.