1 Yapo lidatha Siku lo Pumulila, Maliya wa ku Magidala ni Maliya maye wa Yakobo ni Salome, adagula mafuta yonunghila, adapita kulinyeka thupi la Yesu. 2 Ndiipo umawamawa, siku la Jhumapili, adapita ku chiliza. 3 Yapo adali mnjila adafunjhana, "Yani siwatigunghulichile mwala pakhomo la chiliza?" 4 Yapo adawandikila kufika adapenya, adaona mwala ujha wasendezedwa patali ni khomo la chiliza. 5 Chimwecho adalowa pachiliza, adamuona mnyamata uyo wadavala viwalo voyela, wakhala bendeka la kwene la chijha chiliza, anyiiwo adajhujhumuka kupunda.
6 Mnyamata mmeneyo wadaakambila, "Simdajhujhumuka. Mumfunafuna Yesu wa ku Nazaleti uyo wadapachikidwa pamtanda. Wahyuka, balibepo pano. Penyani pamalo yapo adamgoneka. 7 Chipano pitani mkaakambile oyaluzidwa popande kumyawalila Petulo, ‘Yesu wakuchogolelani ku Galilaya, kumeneko simumuone ngati umo wadakukambilani.’ "
8 Ndiipo adatuluka kubwalo kwa chiliza uku ni adatendhemela kwa mandha, adazizwa ni kuthamanga. Siadamkambile mundhu waliyonjhe chindhu chijha pakuti amaopa kupunda.
9 Yesu yapo wadahyuka umawamawa siku la Jhumapili, wadamtulukila uti Maliya wa kumujhi wa ku Magidala, uyo Yesu wadamchocha viwanda saba. 10 Maliya wa ku Magidala wadapita kwaakambila anyiwajha amalila ni kuimba zaya. 11 Yapo adavela kuti Maliya wa ku Magidala wamwona Yesu wahyuka, siadakhulupilile.
12 Pambuyo Yesu wadaatulukila oyaluzidwa awili uku wali ni nghope ina. Oyaluzidwa achameneo amatopita kumunda. 13 Yapo adamjhiwa, adabwela ni kupita kwaakambila achanjao, nambho anyiiwo siadakhulupilile.
14 Pambuyo Yesu wadatulukila oyaluzidwa khumi ni mmojhi yapo amadya chakudya. Yesu wadaanyindila ndande ya kulimba kwa mitima yao, ni ndande yakusiya kwaakhulupilila anyiwajha adamuona yapo wadahyuka. 15 Chimwecho wadaakambila, "Pitani kujhiko lonjhe la panjhi, mkalalikile wandhu wonjhe Uthenga Wabwino. 16 Mundhu waliyonjhe uyo wakhulupilila ni kubatizidwa, siwaomboledwe, nambho mundhu uyo wakana kukhulupilila siwalamulidwe. 17 Vizindikilo ivi sivikhale pamojhi ni anyiiwo siakhulupilile. Satumile mbhavu za jhina langa kuchocha viwanda ni kukamba kwa mkambo wina. 18 Akagwila njoka kapina kumwa chalichonjhe chili ni sumu sichawenga. Siwaikile manja wandhu wodwala, nawo saalame."
19 Ambuye Yesu yapo adamaliza kukamba ni oyaluzidwa wawo, adatengedwa kupita kumwamba, adakhala kubendeka la kwene la Mnungu. 20 Ndiipo oyaluzidwa wajha adapita kummalo yonjhe kwa lalikila wandhu Uthenga wa Bwino. Ambuye Yesu adachita njhito pamojhi ni anyiiwo ni kuchimikiza uthenga umenewo kwa vizindikilo ivo vidalingana Uthenga umenewo.