Publicidade

Marcos 7

Mayaluzo kuusu chikhalidwe cha azee

1 Siku limojhi, Afalisayo ni woyaluza akumojhi athauko yawo adachokela ku Yelusalemu, adasonghana pachogolo pa Yesu. 2 Adaaona akumojhi awoyaluzidwa wake niadya chakudya kwa manja najhisi, pakuti siadasambe bwino manja yawo ngati umo khalidwe la azee limafunila. 3 Pakuti Afalisayo ni Ayahudi ni wandhu wina wonjhe achata makhalidwe ya azee wao. Siakudya popande kusamba mbaka mvigwinghwi va mmanja. 4 Niakachoka ku soko kugula chindhu, siakudya mbaka asambe. Chinchijha adagwila vikhalidwe vina, ngati vochuka vikombe, miphika ni mbale zodyela.

5 Ndiipo Afalisayo ni oyeluza athauko la Musa adamfunjha Yesu, "Ndande yanji oyaluzidwa wako siachata makhalidwe yayo talandila kuchokela kwa azee wathu, nambho anyiiwo akudya popande kusamba mbaka mvigwinghwi va mmanja?" 6 Yesu wadaayangha, "Agunghuli anyiimwe, mlosi Isaya wadakuloselani bwino anyiimwe, yapo wadalemba,

‘Mnungu wakamba, wandhu anyiawa anilimekeza kwa milomo yaope,

nambho mitima yao, ilikutali niine.

7 Ni kunilambila kwawo sikufunika,

pakuti ayaluza mayaluzo ya wandhupe ngati mayaluzo ya Mnungu.’"

8 "Anyiimwe muyasiya malamulo ya Mnungu ni kuchata chikhalidwe cha wandhu."

9 Yesu wadaendekela kukamba, "Anyiimwe mkana mayaluzo ya Mnungu ni kuchata chikhalidwe chanu. 10 Musa wadaagiza, ‘Alemekeze amako ni atate wako,’ ni ‘Mundhu uyo siwaatukane atate wake kapina amake siwafe.’ 11 Nambho anyiimwe muyaluza ngati mundhu uyo wali ni chindhu chakwaathangatila atate wake ni amake, nambho mkamba, ‘Thandizo ilo nidakupachani ni Kolobani’ mate yake chindhu ichi chapatulidwa ndande ya kumchochela Mnungu, 12 kwakuyaluza chimwecho mwachekeleza wandhu, siwadathangatila atate wao kapina amao. 13 Chimwecho, ndeumo mulidelela mawu la Mnungu ndande ya makhalidwe yanu yayo mudayalandila. Ni mchita vindhu vambili va mtundu umeneo."

Vindhu ivo vimchita mundhu siwadavomelezeka kwa Mnungu

14 Yesu wadalitananjho lijha gulu la wandhu, ni kulikambila, "Mnivechele mwaonjhe kuti mjhiwe. 15 Palibe chindhu chilowa mkati mwa mundhu kuchokela kubwalo icho chikhoza kumchita siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu. Nambho icho chichoka mkati mwa mundhu ndeicho chimchita mundhu siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu. 16 Mchate yayo mkambidwa!"

17 Yesu yapo wadalisiya gulu la wandhu ni kulowa mkati, oyaluzidwa wake adamfunjha mate ya ujha mkuluwiko. 18 Yesu wadaakambila, "Bwanji, nianyiimwe namwenjho simjhiwa? Bwanji, simjhiwa kuti icho chimlowa mundhu kuchokela kubwalo, sichikoza kumchita mundhu wakanidwe kumlambila Mnungu? 19 Pakuti sichilowa mumtima, nambho chilowa mmimba, ni pambuyo chituluka kubwalo kwa thupi lake ni kupita kudambo." Kwakukamba chimwecho, Yesu wadavichita vakudya vonjhe vivomelezeke kudyedwa.

20 Wadaendekela kukamba, "Icho chichoka mkati mwa mundhu nde chimchita mundhu siwadavomelezeka kumlambila Mnungu. 21 Pakuti kuchokela mmitima ya wandhu, yachoka maganizo yoipa ni chigololo ni unghungu ni kupha, 22 uhule ni khumbilo lo funa chuma chambili ni voipa ni unami ni kukafula ni khumbilo lofuna chigololo ni mbwinya ni usabwabwa. 23 Voipa vimenevo vichoka mkati mwa wandhu, navo vimchita mundhu siwadavomelezeka kumlambila Mnungu."

Chikhulupililo cha wamkazi mmojhi uyo siwadali Muyahudi

24 Yesu wadachoka pamenepo, nikupita ku mujhi wa Tilo. Kumeneko wadalowa mnyumba imojhi ni siwadafune mundhu wajhiwe, nambho siwadakhoze kujhibisa. 25 Pajha padalipo ni wamkazi mmojhi uyo wadali ni mwali wa chiwanda, yapo wadavela kuti Yesu wali pajha. Wadajha ni kugwada, pachogolo pa myendo ya Yesu. 26 Yapo wadamgwadila wadampembha Yesu wamchoche chiwanda mwali wake, nambho wamkazi mmeneyo wadali osati Muyahudi, uyo wadabadwila ku Foinike mjhiko la Siliya. 27 Yesu wadamkambila, "Asiye wana akhute uti. Pakuti osati bwino kutenga chakudya cha wana ni kwaponyela agalu."

28 Nambho yujha wamkazi wadamyangha, "Ambuye ni chazene icho mwakamba, nambho ata agalu ali panjhi pa meza akudya vakudya ivo vikhalila kwa wana."

29 Yesu wadamkambila wamkazi yujha, "Ndande wayangha bwino, pita kukhomo kwako ni siumpheze mwali wako walama ni chiwanda chamchoka!"

30 Chimwecho wamkazi yujha wadapita kukhomo lake, wadampheza mwana wake wagona pachika, ni chiwanda chathomchoka.

Yesu wamlamicha bubu gondhi

31 Wadachoka mmujhi wa Tilo ni kupita ku Sidoni mbaka ku nyanja ya Galilaya ni kufika pamalo pa Dekapoli, mate yake mijhi khumi. 32 Kumeneko, wandhu adampelekela bubu gondhi kwa Yesu, ni adampembha kupunda wamuikile manja kuti wamlamiche. 33 Yesu wadamchocha yujha bubu gondhi kumbhepete kwa wandhu ni wadamuikila vyala mmakutu, wadalavula malovu ni kuligafya lilime la yujha mundhu. 34 Wadapenya kumwamba, wadapuma kwa mbhavu ni kumkambila, "Efata" mate yake, "Masuka." 35 Pampajha, makutu yake yadamasuka, ni lilime lake nalo lidalenda, wadayamba kukamba bwino. 36 Ndiipo Yesu wadaalamula asadamkambila mundhu waliyonjhe nghani zijha. Nambho umo wadapunda kwaakanizila, nde umo adayendekela kuziyeneza zijha nghani. 37 Wandhu adazizwa kupunda nikukamba, "Wavichita ivi vonjhe bwino, wamkhozecha agondhi kuvela, ni mabubu akambe!"

Veja também

Publicidade
Marcos
Ver todos os capítulos de Marcos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_12-43-22-