Publicidade

2 Coríntios 1

1 Ine Poolo, nachitidwa kukhala mtumwi wa Kilisito Yesu kwa chikondi cha Mnungu, nili ni mbale Timoseo.

Tikulembelani anyiimwe muli mugulu la wandhu amkhulupililia Kilisito la ku Kolinso pamojhi ni wandhu Amnungu onjhe ali kumujhi wa Akaya. 2 Tikupembhelani ubwino ni mtendele, kwa Mbuye wathu Yesu Kilisito.

Poolo wamuyamika Mnungu

3 Watamandidwe Mnungu ni Tate wa Mbuye wathu Yesu Kilisito, Tate uyo wali ni lisungu ni Mnungu watithila mtima. 4 Iye watithila mtima pa kulaga kwathu konjhe, dala nafe tathile mtima wina yawo alaga, pakwathila mtima ngati umo Mnungu watithilila ife mtima. 5 Ngati umo tipundila kupata mavuto ndande ya kumkhulupilila Kilisito, ni mtundu umweo nde umo tipundila kuthilidwa mtima. 6 Tikalaga nde kuti ndande ya kuthilidwa mtima ni uomboli wanu. Tikathilidwa mtima, ndande ya kukuthilani mtima anyiimwe ni kukuthangatilani kuti mpate mbhavu ya kulimbila mtima pa mavuto yamweyajha tivutika ife. 7 Chikhulupililo icho tilinacho ndande ya anyiimwe ni chachikulu, tijhiwa kuti ngati umo tigwilizana pa mavuto yathu, chinchijha sitigwilizane kuthilana mtima uko tikulandila kwa Mnungu.

8 Achabale okondedwa, tifuna tikujhiwicheni kulaga uko kudatipata kujhiko la Asia, kulaga kumeneko kudatilemelela kupitilila, mbaka tidafa mtima kuendekela kukhala amoyo. 9 Timaganiza kuti tidali ngati wandhu adalamulidwa kumwalila, dala sitidajhikhulupilila tachinawefe, nambho timkhulupilile Mnungu uyo wahyukicha wandhu. 10 Iye wadatiombola ife dala tiyendekele kukhala amoyo, siwaendekelenjho kutiombola, tamkhulupilila kuti siwaendekelenjho kutiombola, 11 anyiimwe namwe mkatithangatila ife kutipembhela. Chimwecho mwawi uwo sitijhiupata kuchokana ni mapembhelo ya wandhu ambili, zikhale ndande ya wandhu ambili kumuyamika Mnungu kupunda ndande yathu.

Poolo wang'anamula ulendo wake

12 Ife tijhidamila chindhu chimojhi, mitima yathu itichochela umboni kuti takhala pano pajhiko hasa pamgwilizano wanu ni ife, pa kujhichicha ni kukhulupilika kuchokela kwa Mnungu. Sitidachogozedwe ni hekima ya mundhu, nambho ni ubwino wa Mnungu. 13 Ife tikulembelani vindhu ivo mkhoza kuvisoma ni kuvananavo. Nikhulupilila kuti simuvane navo bwinobwino, 14 pakuti mbaka chipano mwativana ife kwapang'onope. Chimwecho pasiku lijha siwajhenjho Ambuye wathu Yesu simujhidamile ife ngati umo ife tijhidamila anyiimwe.

15 Nane uku niliokhulupilila chimwecho, nimafuna nijhe huti kwanu dala mpatenjho mwawi. 16 Nidapanga kukuendelani nikakhala ni ulendo wopita kumujhi wa Makedonia ni ndhawi yobwela, dala mnipache mthandizo pa ulendo wanga wopita kujhiko la Yudea. 17 Bwanji, mganiza kuti yapo napanga chimwecho nakhala ong'anamuka ng'anamuka? Kapina bwanji, mganiza kuti nipanga ngati umo achitila wandhu ko kamba "Etu" ni "Notho" kwa ndhawi imojhi? 18 Nambho ngati Mnungu umo wali wokhulupilika, chipano mawu yathu kwanu yasakhala, "Etu" ni "Notho" kwa ndhawi imojhi. 19 Pakuti Kilisito Yesu, Mwana wa Mnungu uyo tidamlalikila kwanu ine, Silvano ni Timoseo, siwadali wa, "Etu" ni "Notho" kwa ndhawi imojhi, nambho kwaiye sikuzonjhe ni "Etu." 20 Pakuti yayo wakamba Mnungu kuti siwachite sikuzonjhe yakhala "Etu" ndiponjho kwa iye "Etu" yathu ikambidwa kwa kupitila Yesu Kilisito kwa kumtamanda Mnungu. 21 Ndiipo Mnungu mwene nde uyo watichita ife tikhale nganganga pamojhi namwe kwa kulunjana ni Kilisito Yesu, nde watisangha, 22 nde uyo wadatiika chizindikilo chilangiza kuti ife niwandhu wake ni kutipacha Mzimu mmitima mwathu, kutichimikizila kuti siwatipache vindhu vonjhe ivo watiikila.

23 Mnungu nde uyo wajhiwa yayo nikamba niyazene! Ine sinidafikenjho ku Kolinso ndande ya kukulengelani lisingu. 24 Sitifuna tikukakamizeni pakukhulupilila kwanu, ife tijhiwa kuti anyiimwe muli nganganga pa chikhulupi chanu. Icho tifunika nikuchita njhito pamojhi namwe dala mkondwele.

Veja também

Publicidade
2 Coríntios
Ver todos os capítulos de 2 Coríntios
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-