1 Abale, nifuna mjhiwe nghani za ubwino wa Mnungu uwo apachidwa magulu ya wandhu amkhulupilila Kilisito aku Makedonia. 2 Okhulupila akumeneko adaesedwa kupunda ni kuvutika, nambho kukondwela kwao kudali kwa kukulu, amathangatila kupunda, ingakhale adali osauka kupunda. 3 Zenedi nikukambilani kuti adali othangatila kuchokana ni umo amakhozela ni kupitilila umo amakhozela. Palibe mundhu uyo wadakambila nambho adachocha kwa kufuna achinawene, 4 adatipembha kupunda kuti tichite njhito nawo yakwathangatila wandhu a Mnungu akujhiko la ku Yelusalemu. 5 Adachita njhito kupitilila umo timaganizila! Adajhichocha achinawene kwa Ambuye, ndiipo adajhichochanjho achinawene kwa ife, ngati Mnungu umo wamafunila. 6 Chimwecho tidampembha kupunda Tito pakuti nde uyo wadayambicha njhito iyi, kuikwanilicha njhito iyi yachikondi pakati panu. 7 Anyiimwe muli ni kila kandhu, chikhulupi, ukhozi okamba, kujhiwa, kuchita vabwino kupunda ni chikondi chanu kwathu. Chimwecho tifuna mkhale othangatila pa njhito iyi ya chikondi.
8 Sinikukamizani, nambho nilangiza umo wina achitila njhito yothangatila dala nijhiwe chikondi chanu umo chili cha uzene. 9 Anyiimwe muujhiwa umo Ambuye wathu Yesu Kilisito wapacha ubwino wake, ingakhale adali ni kila kandhu, adajhichita osauka ndande yanu, dala kuchokana ni kusauka kwao akuchiteni opata. 10 Kwa nghani ya chindhu ichi nikuuzani kuti, ifunika muyakwaniliche yajha mudayamba chaka chapita. Mdali oyamba asati kwa kuchochape nambho mdali ni mtima wofuna kuchocha. 11 Chipano kwanilichani njhito iyi ya kuchocha kwa mtima ngati umo mudali ni khumbilo lalikulu yapo mudayamba, jhichocheni kuchokana ni kukhoza kwanu. 12 Ikakhala mundhu wali ni mtima ochocha, Mnungu siwalandile chijha wakhoza kuchocha, asati kopenya icho walibe. 13 Khumbilo langa asati kuti wina athangatilike nyengo anyiimwe mvutika, nambho ifunika pakhale ni kulingana. 14 Kwa ndhawi ino pakuti muli ni vindhu va mbili vathangatile kukwanilicha vofunika vao, dala anyiiwo nao yapo sakhale navo vambili, akuthangatileni anyiimwe pa zofunikila zanu, pamenepo mwaonjhe simulingane, 15 ngati umo yalembedwa mumalembo ya Mnungu,
"Uyo wadakusa vambili siwadapitilile,
ni yujha wadakusa pang'ono siwadachepekeledwe chindhu."
16 Nimuyamika Mnungu wampacha Tito mtima ngati uwo nilinawo ine othangatila wandhu. 17 Siwada vomelepe pembho lathu, nambho chimchijha wadafuna kupunda kukuthangatilani, mbaka wadalamula mwenewake kujha kwanu. 18 Pamojhi niiye Tito, namtuma mbale mmojhi uyo walemekezeka ni mumagulu yonjhe ya wandhu amkhulupilila Kilisito pa njhito yake ya kuuzila Uthenga Wabwino 19 Asati chimwechope iye wasanghidwa ni magulu ya wandhu amkhulupilila Kilisito wakhale mnjathu paulendo opeleka jhembe izo zachochedwa kwa mtima, njhito iyo tichita ndande ya Ulemelelo wa Ambuye dala kulangiza maganizo yathu yabwino.
20 Sitifuna mundhu watidandaulile kuchokana ni kuimilila kwathu mbhaso iyi ya kuthangatila wina. 21 Maganizo yathu nikuchitabwino asati pachogolo pa Ambuyepe, chimchijha tionekane ni wandhu.
22 Chimwecho nimtuma mbale wathu mwina pamojhi ni anyiiwo uyo watichimikizila kwa njila zambili kuti wali ni mtima othangatila wandhu, ata chimwecho wakhala ni mtima kupunda othangatila wandhu ndande wakukhulupililani kupunda anyiimwe. 23 Tito ni mnjanga, tichita njhito pamojhi ndande yanu, nambho anyiyawa achabale wathu wina yawo akujha pamojhi naye, achameneo ni athenga wa magulu ya wandhu amkhulupilila Kilisito, nawo ampacha ulemelelo Kilisito. 24 Chimwecho alangizeni wandhu anyiwa chikondi chanu dala magulu wandhu amkhulupilila Kilisito, yajhiwe kuti tikamba uzene yapo tijhidamila kukhalapo wanu.