1 Ndipo, okondedwa wanga, pakuti tili ni yayo Mnungu watikambila kuti siwatipache, chimwecho tijhieleche mmitima yathu ni chilichonjhe icho chikhoza kudecha matupi yathu ni mizimu yathu, tikhale oyela ni kumlambila Mnungu.
2 Tipembha mtikonde mmitima yanu! Sitidamlakwile mundhu waliyonjhe, sitida mdyele mumndhu waliyonjhe kapina kumnyenga mundhu waliyonjhe. 3 Sinikamba vindhu ivi kwa kumlanga mundhu, ngati umonidakambila mmayambo anyiimwe muli mmitima yathu ata kwa kufa pamojhi kapina kwa kukhala pamojhi. 4 Nili wopilila yapo nikamba namwe, niona ufulu waukulu kwanu! Kwakulaga kwathu tathilidwa mtima ni kukondwa kupunda.
5 Ata yapo tidafika ku Makedonia, sitidakhoze kupumulila. Kila kumalo tidazingizilidwa ni kukhaikila, kubwalo kudali ndewo, mmitima yathu kudali ni mandha. 6 Nambho Mnungu uyo wathila mtima anyiyao afa mtima, wadatithila mtima kwa kujha kwake Tito. 7 Asati kujha kwa Tito pe, nambho kwa mtima uwo mudampacha. Watifotokozela khumbilo lanu lakuniona, umo muli ni chisoni, ni umo mfunila kuni teteza. Chindhu ichi chikondwecha kupunda.
8 Ingakhale kalata yanga nakupachani chisoni, ine sinikhaula. Ata ngati nidakakhaula niona kalata imeneyo idakupachani chisoni kwa ndhawi yochepape. 9 Chipano nikondwa, asati ndande nakupachani chisoni, nambho ndande chisoni chanu chakuchitani mulape. Mwapachidwa chisoni ngati Mnungu umo wafunila, dala simdapatidwa ni choipa chilichonjhe kupitila ife. 10 Chimwecho chisoni icho chichokana ni umo wafunila Mnungu chichita wandhu asiye machimo ni kuomboledwa, ni sichachita wandhu akaule. Nambho chisoni icho chichokana ni jhiko chipeleka nyifa. 11 Chipano mwaona chisoni icho chiyambichidwa ni Mnungu umo chapelekela phindhu kwanu yokhala wandhu abidii, juhudi iyo mwichita kujhiteteza, kupweteka kwanu, mandha yanu, chikondi chanu, kumbilo lanu lochochocha chilango icho chifunika. Kwa yamaeneyo yonjhe mlangiza kuti mlibe cholakwa pa chindhu ichi.
12 Chimwecho ingakhale nidalemba ijha kalata siidali ndande ya mundhu uyo walakwila kapina ndande yamundhu uyo walakwilidwa. Nidalemba dala bidii yanu ionekane padanga kwa Mnungu kwa umo mudachitila ndande yathu 13 Ndiipo ife tidathilidwaa mtima kupunda.
Sitidathilidwe mtima pe, ni Tito wakondwela kupunda ndande kwa chikondwelo icho wadali nacho nambho kuchokana ni umo mdaukondwelecha mtima wake. 14 Ine najhielekela kwa Tito ndande yanu, nianyiimwe simudani lengeche mwano. Takukambilani uzene ni kujha kukuelekelani anyiimwe pachogolo pa Tito kwa khala uzene okhaokha. 15 Chikondi chake kwanu chichuluka yapo wakumbukila, umo muli tayali kuvomela ni umo mudamlandila kwa mandha ni kutendhemela. 16 Nikondwela kupunda ndande chipano nikhoza kukukhulupililani anyiimwe kwa kila kandhu.