1 Yesu wadaendekela kukamba nawo kwa chifani. Wadakambila, 2 "Ufumu wa kumwamba ulingana ni Mfumu mmojhi uyo wadamkonjela mwana wake wammuna chakudya cha ukwati. 3 Wadaatuma mbowa zake wakaatane yao wadalalika ajhe ku ukwati nambho adakana kujha. 4 Ndiipo wadaatuma mbowa wina, wadaakambila, ‘Akambileni anyiwajha alalikidwa, naphika chakudya, ng'ombe zanga za mbhongho zazikuluzikulu ni ng'ombe za zing'ono zing'ono zonona zachinjidwa, kila kandhu kali tayali. Majhani mudye!’ 5 Nambho wandhu wajha adalalikidwa adadelela, kila mmojhi wadachokapo kupita kunjhito yake, mwina kumunda wake ni mwina kumalonda yake. 6 Wina adaagwila mbowa wake, wadaabula ni kwaipha. 7 Mfumu mmeneyo wadakwiya kupunda, chimwecho wadaatuma asikali wake wakaaphe wandhu wajha wadaapha mbowa zake ni kuipyeleza mijhi yao. 8 Ndiipo wadaatana mbowa zake ni kwaakambila, ‘Phwando la ukwati lali tayali, nambho anyiyao naalalika siadakwanile kujha kuphwando. 9 Chimwecho pitani mmikwakwa ya mijhi ni walionjhe uyo simumuone, mlalikeni wajhe kupwando la ukwati.’ 10 Mbowa wajha adapita mnjila za mmikwakwa, wadatana wandhu wonjhe yawo adadulichana, oyipa ni abwino. Phwando lidajhala alendo. Mnyumba mujha mdachitikila ukwati mdajhala alendo."
11 "Mfumu yapo wadalowa mkati wadapenya alendo wake, wadaona muli mundhu siwadavale njhalu ya ukwati. 12 Mfumu wadamfunjha, ‘Bwenji, walowa bwanji malo yano popande kuvala njhalu ya ukwati?’ Nambho mundhu yujha siwadayanghe. 13 Pamenepo mfumu wadaakambila mbowa ‘Mmangeni myendo ni mmanjha mkamponye kubwalo kumdima. Kumeneko siwalile ni kubukutula mano.’"
14 Yesu wadamaliza kwa kukamba, "Wandhu yawo alalikidwa ni ambili, nambho yawo asanghidwa ni ochepa."
15 Ndiipo Afalisayo adachoka ni adafunafuna njila ya kumgwila Yesu kwa mawu yake. 16 Adaatuma oyaluzidwa wao pamojhi ni wandhu agulu la Helode. Adakamba, "Oyaluza, tijhiwa kuti iwe ni mzene ni uyaluza mau la Amnungu kwa uzene, ndande siuopa ukulu wa mundhu. 17 Tikambile chipano, uona bwanji ife tifunika kulipa msongho kwa mfumu wa ku Loma kapina notho?"
18 Nambho Yesu wadajhiwa voipa vao wadakamba, "Agunghuli anyiimwe, ndande yanji munichela? 19 Nilangizeni gelenjha la ndalama iyo mlipila msongho!"
Anyiiwo adampelekela gelenjha la ndalama. 20 Ndiipo Yesu wadafunjha, "Bwanji, nghope ni jhina ili ni vayani?"
21 Adamuyangha, "Va mfumu wa ku Loma,"
Pamwepo Yesu wadakambila, "Va mfumu wa ku Loma mpacheni mfumu wa ku Loma ni va Amnungu mpacheni Mnungu."
22 Yapo adavela chimwecho adadabwa, chimwecho adamsiya ni kuchoka.
23 Siku limwelo akumojhi wa Asadukayo, yawo akamba, palibe kuhyuka kwa wandhu, adampitila Yesu, adamkambila, 24 "Oyaluza, Musa wadakamba ngati mundhu wammuna wamwalila popande kusiya mwana, mbale wake wamkwate wamkazi wafedwa ni mmunake kuti wambalile mbalewake wana. 25 Pano pathu padali ni abale saba. Oyamba wadakwata ni kumwalila, ndande wadalibe mwana, mpwake wadalowa chokolo wamkazi mmeneyo. 26 Chindhu chimchijha chidamchitikila mbale wa kawili ni waka tatu mbaka wa saba. 27 Pothela wamkazi mmeneyo nayo wadamwalila. 28 Akahyuka wamkazi siwakhale wayani pakuti wonjhe saba adamkwata."
29 Yesu wadayangha wajha Asadukayo, "Mwasokelela anyiimwe, pakuti simujhiwa malembo yoyela kapina mbhavu za Mnungu. 30 Wandhu yapo ahyuka palibe kukwata kapena kukwatiwa, siakhale ngati mtumiki wa kumwamba. 31 Pa nghani za kuhyuka, simdajhiwe chijha wadakukambilani Mnungu? Wadaakambila, 32 ‘Ine nde Mnungu wa Ibulahimu ni Mnungu wa Isaka ni Mnungu wa Yakobo.’ Chimwecho, Mnungu osati Mnungu wa wandhu omwalila, nambho ni Mnungu wa wandhu amoyo."
33 Gulu la wandhu yapo lidavela mawu yameneyo lidazizwa mayaluzo yake.
34 Afalisayo yapo adavela Yesu waachita masadukayo akhale chete, adakomana pamojhi. 35 Mmojhi wao wa oyaluza thauko wadamfunjha Yesu kwa kumchela, 36 "Oyaluza, pamathauko yonjhe thauko liti lili lalikulu?"
37 Yesu wadamuyangha, "Mkonde Ambuye Mnungu wako kwa mtima wako onjhe ni mzimu wako onjhe ni njelu zako zonjhe. 38 Ili nde lamulo lalikulu ni loyamba. 39 Lamulo la kawili lilingana ni ili, ‘Mkonde mnjako ngati umo ujhikondela umwene wake.’ 40 Pamathuko yonjhe ni mayaluzo ya alosi, yonjhe yachokana ni malamulo yaya yawili."
41 Afalisayo wajha yapo adali akomana pamojhi pampajha, Yesu wadaafunjha, 42 wadaakambila, "Bwanji, anyiimwe mganiza kuti Kilisito muomboli ni mwana wa yani?"
Adamuyangha, "Wa Daudi,"
43 Yesu wadaafunjha, "Ndande yanji Mzimu Woyela umchogoza Daudi wamtane ‘Mbuye?’ pakuti Daudi wadakamba,
44 ‘Ambuye adaakambila Mmbuye wanga,
Khala jhanja langa la kwene,
mbaka naike adani wako panjhi pa myendo yako mbaka yapo siwakhoze adani wako wonjhe.’
45 Ngati Daudi watana Kilisito, ‘Ambuye,’ ikhala bwanji Kilisito wakhale mwana wa Daudi?"
46 Palibe uyo wadayangha mau. Kuchokela siku limenelo ni kuyendekela palibe uyo wadayesa kumfunjha Yesu.