Publicidade

Mateus 26

Upandu wa kumpha Yesu

1 Yesu yapo wadamaliza kuyaluza yonjhe, wadaakambila oyaluzidwa wake, 2 "Ngati umo mjhiwila kuti pambuyo pa masiku yawili sikukhale pwando la Pasaka, ni Mwana wa Mundhu siwapelekedwe kwa adani wake kuti wapachikidwe pamtanda."

3 Ndiipo ajhukulu wakulu ni wakulu a wandhu adakomana pamojhi mnyumba ya milandhu wa Mjhukulu Wamkulu uyo watanidwa Kayafa, 4 adakambilana upandu wa kumgwilila Yesu kwa chisisi kuti amphe. 5 Anyiiwo adakambilana, "Siifunika tichite chimwechi ndhawi ya phwando la Pasaka, wamdhu siadachita mkanganjili pakati pa wandhu."

Yesu wapungulilidwa mafuta ku mujhi wa Besania

6 Yesu wadali ku Besania mnyumba mwa Simoni uyo wadali ni makate. 7 Yesu yapo wamadya, wadajha wamkazi mmojhi uyo wadasenjhela njhupa ya mafuta yonunghila ya mtengo waukulu, wadayapungulila pamutu pa Yesu. 8 Oyaluzidwa wake yapo adaona chimwecho adakwiya, adafunjhana, "Ndande chiani wayawananga chimwechi mafuta yaya? 9 Mafuta yonunghila yaya yadakakhoza kugulichidwa kwa mtengo waukulu ni ndalama kwaapacha osauka!"

10 Yesu wadajhiwa icho amakamba, wadaakambila, "Ndande yanji mumchaucha wamkaziyu? Uyu wamkazi wanichitila chindhu chabwino kupunda. 11 Osauka simukhale nawo masiku yonjhe, nambho ine simukhala nane masiku yonjhe. 12 Yapo wanipungulila mafuta yaya pathupi, wachita chimwecho dala kukonjekela kuzikidwa kwanga. 13 Zenedi nikukambilani, kulikonjhe uko kulalikidwa uthenga wabwino, chindhu ichi wachichita wamkazi huyu sichilalikilidwe kwa kumkumbukila iye."

Yuda wavomela kumng'anamuka Yesu

14 Ndiipo mmojhi wa anyiwajha oyaluzidwa khumi ni awili, uyo wamatanidwa Yuda isikaliote wadapita kwa wakulu a jhukulu, 15 wadaafunjha, "Simunipache ndalama zingati nikamng'anamuka Yesu kwanu?" Chimwecho adamuwelengela magelenjha selasini ni kumpacha. 16 Kuyambila pamenepo Yuda wamafunafuna mtundu wabwino wa kumng'anamuka Yesu.

Yesu wakudya chakudya cha Pasaka pamojhi ni oyaluzidwa wake

17 Msiku loyamba la pwando la mabumunda yayo yalibe amila, oyaluzidwa adajha kwa Yesu ni kumfunjha, "Ufuna tikakukonjekele kuti chakudya cha pwando la Pasaka?"

18 Yesu wadaayangha, "Pitani mmujhi kwa wammuna mmojhi, mukamkambile, ‘Oyaluza akamba, saa yanga yafika, ine ni oyaluzidwa wanga sitidye chakudya cha Pasaka mnyumba yako.’ "

19 Oyaluzidwa adachita ngati umo Yesu wadaakambila, adakonja chakudya cha pwando la Pasaka.

20 Yapo udafika ujhulo, Yesu ni oyaluzidwa wake khumi ni awili adakhala kudya chakudya. 21 Yapo amadya, Yesu wadaakambila, "Zenedi nikukambilani, mmojhi wanu siwaning'anamuke."

22 Oyaluzidwa wake adavachisoni kupunda, adayamba kumfunjha mmojhimmojhi, "Ambuye, bwanji, ni ine?"

23 Yesu wadayangha, "Mundhu mmojhi uyo wasunjha bumunda lake mmbale pamojhi ni ine, nde uyo siwaning'anamuke. 24 Mwana wa Mundhu siwamwalile ngati mujha idalembeledwela mu malembo. Nambho siwavutike mundhu yujha wamng'anamuka Mwana wa Mundhu! Idakakhala mbasa kwa mundhu mmeneyo kuti siwadakabadwa."

25 Ndiipo Yuda, yujha wamng'anamuka, wadakamba, "Oyaluza, nde ine kani?"

Yesu wadamuyangha, "Yetu, nde iwe ngati umo wakambila."

Chakudya cha Ambuye

26 Yapo amadya Yesu wadatenga bumunda, wadayamika, wadaubandhula, ni kwapacha oyaluzidwa wake nikukamba, "Tengani mudye, ili nithupi langa."

27 Ndiipo wadatenga chikho, wadayamika Mnungu, ni kwaapacha oyaluzidwa wake niwakamba, "Mwaonjhe mchimwele chikho ichi, 28 uwu nde mwazi wanga uwo uchimikiza chipangano, umwazika ndande ya ambili dala machimo yao yalekeleledwe. 29 Nikukambilani, sinimwanjho divai iyi mbaka siku ilo sinimwe divai yachipano ni anyiimwe mu Ufumu wa Atate wanga."

30 Ndiipo adaimba nyimbo nikupita kuphili la Mizeituni.

Yesu walosa kuti Petulo siwamkane

31 Ndiipo Yesu wadaakambila, "Usiku uno walelo anyiimwe mwaonjhe simunithawe ni kunisiya, pakuti malembo yakamba, ‘Sinimbule owesa, ni mbele sizimwazike.’ 32 Nambho yapo sinihyuke, sinikuchogoleleni kupita ku jhiko la Galilaya."

33 Petulo wadamuyangha, "Ata ngati onjhe siakusiye, ine sinikusiya."

34 Yesu wadamkambila Petulo, "Zene nikukambila, usiku wa lelo, wakali osalile tambala, siunikane katatu."

35 Petulo wadayangha, "Sinikhoza kukukana, ata ngati nikafunika kumwalila pamojhi ni namwe sinikukanani!"

Ni oyaluzidwa wonjhe adakamba chimwecho.

Yesu wapembhela ku busitani ya Getisemane

36 Ndiipo Yesu wadapita pamojhi ni oyaluzidwa wake pa malo yapo pamatanidwa Getisemani, ni iye wadaakambila, "Khalani pano ine nipite yapo kukapembhela."

37 Wadatenga Petulo ni wana awili Azebedayo, wadayamba kuva chizoni ni kulaga mumtima. 38 Kumeneko wadaakambila, "Nili ni chisoni chachikulu mumtima mwanga icho chikhoza kunipha. Khalani pano ni muchezele pamojhi ni ine."

39 Wadapita pachogolo pang'ono, wadagwa panjhi chifufumimba ni kupembhela, "Atate wanga, ngati ikhozeka, nichocheleni chikho ichi cha mavuto! Chipano osati ngati umo nifunila ine, nambho ngati umo mufunila imwe."

40 Ndiipo wadabwela kwa oyaluzidwa wake ni kwaapheza agona, wadamkambila Petulo, "Ikhala bwanji simdakhoze kuchezelela ni ine ata kwa saa imojhipe? 41 Chezelani ni kupembhela kuti msadalowa mu mayeselo. Mtima ufuna kuchita yayo yafunika, nambho thupi lilibe mbhavu."

42 Wadapitanjho kakawili wadapembhela, "Atate wanga, ngati siikhozeka kuchichocha chikho ichi chamavuto, basi mchite umo mfunila." 43 Yapo wadabwela kakawili wadaaphezanjho agonanjho ndande maso yao yadali ni litulo.

44 Chimwecho wadaasiyanjho ni kupita kupembhela kakatatu ni wakamba mau yamweyajha. 45 Ndiipo wadabwela kwa oyaluzidwa wake ni kwakambila, "Bwanji, mkali kugona ni kupumulila? Vechelani, saa yakwana Mwana wa Mundhu siwagwilidwe ni wandhu amachimo. 46 Imani tijhipita. Yujha waning'anamuka watokujha."

Yesu wagwilidwa

47 Yesu yapo wadali wakali kuyendekela kukamba, Yuda mmojhi wa oyaluzidwa wake khumi ni awili, wadajha. Yuda wadachogozana ni gulu lalikulu la wandhu yawo adali ni maupanga ni vibonga, yawo adatumidwa ni waakulu akulu anjhukulu ni wakulu a wandhu. 48 Yuda wadapacha wandhu wajha chizindikilo kuti, "Mundhu uyo sinimlonjhele kwa kumvumbatila nde mmweyo, mgwileni!"

49 Pamenepo Yuda wadajha kwa Yesu ni kumlonjela, "Moni oyaluza," pampajha wadamvumbatila.

50 Yesu wadamkambila, "Iwe bwenji, chita chijha wajha kuchichita."

Ndiipo wandhu wajha adamsendelela Yesu adamgwila ni kummanga.

51 Mmojhi wa wajha adali ni Yesu wadasolomola upanga ni kudula khutu la mbowa wa mjhukulu Wamkulu. 52 Ndiipo Yesu wadamkambila, "Bwezela upanga wako mmalo mwake, pakuti waliyonjhe wakupha kwa upanga, siwaphedwe kwa upanga. 53 Bwanji, simjhiwa kuti nikhoza kwatana Atate wanga anithangatile, ni iwo akhoza kunipelekela magulu khumi ni yawili ya atumiki akumwamba? 54 Nambho, malembo yoyela siyakwanile bwanji yajha yakamba kuti, nde umo ifunikila ichitike?"

55 Ndiipo Yesu wadalikambila lijha gulu, "Bwanji, mwajha ni maupanga ni vibonga kunigwila ine ngati wolanda? Kila siku nidali namwe ni niyaluza mnyumba ya Mnungu, simudanigwile. 56 Ivi vonjhe vachokela kuti vijha valembedwa ni alosi vikwanile."

Ndiipo oyaluzidwa wake wonjhe adamsiya ni kumthawa.

Yesu pachogolo pa bwalo

57 Wajha adamgwila Yesu adampeleka ku nyumba ya mjhukulu wamkulu uyo wamatanidwa Kayafa, pa malo yapo adasonghana oyaluza a thauko pamojhi ni wakulu a wandhu. 58 Petulo wadachata Yesu kwa patali mbaka kwa mjhukulu wamkulu. Wadalowa mkati mwa seli pamojhi ni alonda kuti waone icho sichichokele.

59 Ajhukulu wa wakulu ni bwalo lonjhe, adafunafuna umboni wamthila dala amphe Yesu. 60 Nambho sadakhoze kupata umboni walionjhe, ata ngati wandhu adachocha umboni wambili wamthila. Ndiipo adajha amboni awili, 61 adakamba, "Mundhu uyu wadakamba, ‘Sinikhoze kuibomola Nyumba ya Mnungu ni kuimanganjho pa masiku yatatu.’ "

62 Ndiipo Mkulu wa ajhukulu wadaima ni kumkambila Yesu, "Bwanji, siuyangha chalichonjhe? Bwanji milandu iyo akamba wandhu anyiyawa ya uzene?" 63 Nambho Yesu wadakhala chete. Mkulu wa Ajhukulu wadakamba, "Chipano lumbila mjhina la Mnungu wali wamoyo, utikambile ngati iwe nde Kilisito, Mwana wa Mnungu."

64 Yesu wadamuyangha, "Umo ukambila nde chimwecho! Nambho nikukambilani mwaonjhe, kuyambila chipano simumuone Mwana wa Mundhu wakhala kwene kwa Mnungu Wambhavu, niwajha mmitambo!" 65 Pampajha Mkulu wa ajhukulu wadang'amba njhalu zake kulangiza kuti wakwiya, ni kukamba, "Wakafula! Tifunanjho umboni unjake? Mwachinawene mwavela umo wakhafulila. 66 Anyiimwe muganiza chiyani?"

Anyiiwo adayangha, "Walakwa uyu ni wafunika waphedwe."

67 Ndiipo adamlavulila malovu kumaso ni kumbula. Wina adammenya makofi, 68 adakamba, "Iwe Kilisito, tilosele! Yani uyo wakubula?"

Petulo wamkana Yesu

69 Petulo wadakhala kubwalo kuseli. Mbowa mmojhi wamkazi wadampitila ni kumkambila, "Iwe nawenjho udali pamojhi ni Yesu wa ku Galilaya."

70 Petulo wadakana pamaso pawo onjhe, niwakamba, "Sinichijhiwa icho uchikamba." 71 Yapo wadatuluka kubwalo ni kufika pakhomo, mbowa mwina wamkazi wadamuona, wadaakambila wandhu yawo adali pamenepo, "Mundhu uyu wadali pamojhi ni Yesu wa ku Nazaleti."

72 Petulo wadakangalanjho kwa kulumbila uku ni wakamba, "Sinimjhiwa mundhu mmeneyo!"

73 Pambuyo pang'ono, anyiwajha adali pajha adampitila Petulo wadamkambila, "Zenedi, iwe ni mmojhi wao, pakuti ata kukamba kwako kulangiza kuti iwe uchoka ku Galilaya!"

74 Ndiipo Petulo wadayamba kujhileswa ni kulumbila, "Zenedi sinimjhiwa mundhu uyu!"

Pampajha tambala wadalila. 75 Ndiipo Petulo wadakumbukila mau yajha wadakamba Yesu, "Tambala wakali osalile, siunikane katatu." Wadapita kubwalo, wadalila kwa kubuula.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-