Publicidade

Mateus 4

Yesu wayesedwa

1 Ndiipo Mzimu Woyela udamchogoza Yesu mbaka kuphululu kuti waesedwe ni Satana. 2 Yesu wadamanga masiku alubaini usiku ni usana ndiipo wadavela njala. 3 Ndiipo woyesa wadamchata, Wadamkambila, "Ikakhala iwe Mwana wa Mnungu, Lamula myala iyi ikhale mabumunda."

4 Yesu wadamuyangha, "Yalembedwa, ‘Mundhu siwakhala wa moyo kwa bumundape, Nambho kwa kila malembo yoyela yakambidwa ni Mnungu.’"

5 Ndiipo Woyesa wadamtenga Yesu mbaka ku Yelusalemu mujhi woyela. Wadamkweza mbaka pamwamba kupunda pa chindupa la nyumba ya Mnungu. 6 Wadamkambila, "Ngati iwe ni Mwana wa Mnungu jhitaye panjhi. Pakuti yalembedwa,

‘Mnungu siwakutumile atumiki wake akumwamba

saakutenge mmanja mwao

kuti siudajhikhuwala mwendo wako pa mwala.’"

7 Yesu wadayangha, "Chinchijha yalembedwa, ‘Usadamuyesa Ambuye Mnungu wako.’"

8 Ndiipo Woyesa wadamtenganjho Yesu mbaka pa mwamba pa phili la litali. Wadamlangiza ufumu wonjhe wa jhiko ni ufulu wajhiko. 9 Wadamkambila, "Vindhu vonjhevi sinikupache ngati siunigwadile ni kunilambila."

10 Yesu wadamkambila, "Chokapo yapa iwe Woyesa! Yalembedwa mmalembo ya Mnungu, ‘Waalambile Ambuye Mnungu wako ni kwaatumikila iwo okha.’"

11 Ndiipo Woyesa wadamleka Yesu ni atumiki a kumwamba adajha kumtumikila.

Yesu wayamba njhito yake kumujhi wa Galilaya

12 Yesu yapo wadavela kuti Yohana waikidwa mndende wadapita kumujhi wa Galilaya. 13 Wadachoka ku Nazaleti wadapita kukhala kumujhi wa Kapelinaumu mujhi uli pafupi ni nyanja ya Galilaya mumalile ya mayiko ya Zabuloni ni Nafutali. 14 Chindhu ichi chidachitika kuti chikwanile chijha chidakambidwa ni mlosi Isaya,

15 "Jhiko la Zebuloni ni jhiko la Nafutali

kunjila ipita mnyanja kuchijya la mchinje Yolodani,

Mgalilaya mjhiko ilo akhala wandhu yawo osati Ayahudi!

16 Wandhu yawo adakhala mumdima aliona dangalila lalikulu.

Wandhu yawo amakhala mujhiko la mchitunjhi cha nyifa dangalila lawalila."

17 Kuchokela nyengo imeneyo Yesu wadayamba kulalikila niwakamba, "Siyani kuchita machimo pakuti ufumu wa kumwamba wawandikila!"

Yesu waatana alovi anayi

18 Yesu yapo wamaenda mphepete mwa nyanja ya Galilaya wadaona abale awili, Simoni uyo wamatanidwa Petulo ni Anduleya. Amavuwa njhomba mnyanja kwa makoka yawo. 19 Yesu wadaakambila, "Majhani nichateni! Nane sinikuchiteni mukhale opeleka wandhu kwa Mnungu." 20 Pampajha adayasiya makoka yao niadamchata.

21 Yapo wadapita pachogolo wadaaona abale wina awili, Yakobo ni Yohana wana a Zebedayo. Anyiiwo adali mkati mwa boti pamojhi ni atatewao a Zebedayo amatambasula makoka yao. Yesu wadaatana. 22 Pampajha adalisiya boti ni atate wao ni kumchata Yesu.

Yesu wayaluza ni kwaalamicha wandhu

23 Yesu wadaendela malo yonjhe ya Galilaya. Wadayaluza mnyumba yokomanilana Ayahudi ni wadalalikila uthenga wa Ufumu wa Mnungu. Wadalamicha kila mtundu wa matenda ni mavuto yonjhe. 24 Nghani zake zidayenela madela yonjhe ya Siliya. Chimwecho wandhu adaampelekela wodwala wonjhe ni anyiyawo amavutika ni kila mtundu wa matenda ni ozamwa ni viwanda ni anjilinjili ni ovulala. Nayo wadalamicha wonjhe. 25 Magulu yambili ya wandhu kuchokela mujhiko la Galilaya ni Dekapoli ni Yelusalemu ni Yudea ni chijya la mchinje Yolodani yadamchata Yesu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-