1 "Msadalamula wandhu wina, chimwecho namwe simulamulidwa ni Mnungu, 2 pakuti umo mwaalamulila wina, ni anyiimwe simlamulidwe chimwecho, ni chimchijha umo mujhichocha kuvechela mawu nde chimwecho Mnungu siwakuchiteni mulijhiwe. 3 Ndande yanji upenya chikoko chali mdiso mwamnjako, nambho umwene wake ulemekela kuliona phesi ilo lili mdiso lako? 4 Kapena ukhoza bwanji kumkambila njako, ‘Mbale, lindila nikuchoche chikoko mdiso mwako,’ niyapo wamwene wake ulinalo phesi ilo lili mdiso mwako? 5 Iwe gunghuli! Chocha uti phesi lili mdiso mwako ni pamenenepo ndeyapo siupenye bwino ni kukhoza kuchocha chikoko chili mdiso mwa mnjako."
6 "Msadapacha agalu vindhu voyela saakubweleni ni kukulumani anyiimwe, ni msadaziponyela nguluwe vindhu va mtengo wa ukulu vitanidwa lulu savibwele ni kuvipondela."
7 "Pembhani, namwe simpachidwe, funafunani namwe simupate, gogodani chicheko namwe simuchakulidwe. 8 Pakuti mundhu waliyonjhe uyo wampembha Mnungu siwapachidwe ni uyo wafunafuna siwapheze, ni uyo wagogoda chicheko siwachakulidwe. 9 Bwanji, kuli waliyonjhe pakati panu uyo mwana wake wakapembha bumunda siwamninghe mwala? 10 Kapina, wakampembha njhomba wampacha njoka? 11 Ngati anyiimwe woipa mujhiwa kwaapacha wana wanu vindhu vabwino, uzene Atate wanu akumwamba siwaapache vabwino anyiwajha ampembha."
12 "Mujha mfuna kuchitilidwa anyiimwe ni wandhu, namwenjho mwaachitile wandhu wina chimwecho. Ndande thauko la Musa ni vikalakala va alosi vikambilila chindhu ichi."
13 "Lowani kupitila khomo lowonda. Pakuti khomo ilo lichogoza kumalo kwa wandhu akufa ni lopanuka, ni wandhu alowela khomo limenelo ni ambili. 14 Nambho khomo ilo lichogoza ku umoyo ni laling'ono ni lowonda wandhu wochepa ndeyawo akhoza kuiona njila imeneyo."
15 "Mkhale maso ni alosi amthila. Anyiiwo akujha kwanu ngati mbelele kubwalo, nambho kwamkati alingana ni mibinji iyo ikujha kukuhundukilani. 16 Simwaajhiwe kwa vichito vao. Bwanji, wandhu akucha masuku pa mtengo wa minga, kapina mpelesa pa ndhujha? Notho! 17 Chinchijha, mtengo wabwino upacha vipacho vabwino, ni mtengo woipa upacha vipacho voipa. 18 Mtengo wabwino siukhoza kupacha vipacho voipa, chinchijha mtengo woipa siukhoza kupacha vipacho vabwino. 19 Kila mtengo uwo siubala vipacho vabwino siudulidwe ni kuponyedwa mmoto. 20 Chimwecho, simwaajhiwe alosi amthila kwa vichito vao."
21 "Osati kila uyo wanitana, ‘Ambuye, Ambuye,’ siwalowe muufumu wa kumwamba, nambho niwajhape achita vijha afuna Atate wanga ali kumwamba. 22 Ambili saanikambile siku limenelo la lamulo, ‘Ambuye, Ambuye! Kwa jhina lanu tidaalalikila wandhu uthenga wa Mnungu, ni kwa jhina lanu tidatopola viwanda ni kuchita vodabwicha vambili.’ 23 Pamwepo sinaakambile, ‘Notho, Sinikujhiwani anyimwe, chokani kwanga anyimwe wandhu woipa!’"
24 "Mundhu waliyonjhe wavela mawu yanga ni kuyachita, walingana ni mundhu wa njelu, wadamanga nyumba yake pa mwala waukulu. 25 Vula ikanya, michinje ikajhala, mbhepo yaikulu ikapula ni kuibula nyumba ijha. Nambho siidagwe ndande msingi wake udamangidwa pa mwala waukulu."
26 "Nambho waliyonjhe wavela mawu yanga popande kuyachita, mmeneyo walingana ni mundhu sabwabwa uyo wadamanga nyumba yake pamchenga. 27 Vula ikanya, michinjhe ikajhala ni mbhepo ikapula ni kuitingiza ijha nyumba, nayo siigwe kwa mdidi waukulu!"
28 Yesu yapo wadamaliza kukamba yaya, gulu la wandhu lidadabwa kupunda umo wamayaluzila. 29 Wamayaluza ngati mundhu uyo wali ni ulamuli, osati ngati oyaluza wao a thauko.