Publicidade

Mateus 19

Nghani yosiyana

1 Yesu yapo wadamaliza kukamba nghani zimenezo, wadachoka kumujhi wa Galilaya ni kupita kumujhi wa Yudea, kuchijya la mchinje Yolodani. 2 Gulu lalikulu la wandhu lidamchata, iye wadaalamicha.

3 Afalisayo akumojhi adamchata Yesu ni kumfunjha kwa kumchela, "Bwanji, thauko limlola waamuna kumsiya mkazake ndande ya cholakwa chilichonjhe?"

4 Yesu wadaayangha, wadakamba, "Bwanji, simudasome Mmalembo Yoyela kuti poyamba Mnungu wadamuumba mundhu wammuna ni wamkazi? 5 Mnungu wadakamba, ‘Pandande iyi mundhu wammuna siwaasiye atate wake ni maye wake ni kulunjana ni mkazake, ni awili yawa siakhale thupi limojhi.’ 6 Chimwecho, anyiiwo osati awilinjho, nambho thupi limojhi. Icho wachilunjanicha Mnungu, mundhu siwadachisiyanicha."

7 Afalisayo adamfunjha, "Ndande yanji Musa wadaagiza wammuna wampache mkazake kalata yosiyana?"

8 Yesu wadaayangha, "Musa wadakulolezani kwasiya achakazanu ndande anyiimwe ni wandhu yawo simuyaluzika, nambho siidali chimwecho yapo Mnungu wadaumba jhiko lapanjhi. 9 Nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo siwamsiye mkazake popande ndande ya chigololo ni kukwata wamkazi mwina, mundhu mmeneyo wachita chigololo."

10 Oyaluzidwa wake adamkambila, "Ngati vindhu ivi vikakhala chimwechi pakati pa wammuna ni wamkazi, mbasa kukhala osakwate."

11 Yesu wadaakambila, "Osati wonjhe akhoza kuyalandila mau yaya, nambho anyiwajha Mnungu waapacha chindhu chimenecho. 12 Kuli vindhu vambili ivo vaachita waachimuna asadakwata. Wina abadwa chimwecho, ni wina achitidwa chimwecho ni wandhu kuti siadakhala ni mbhavu zachimuna. Wina saakwata ndande ya Ufumu wa Mnungu. Mundhu uyo wakhoza kuyalandila mau yaya, wayalandile."

Yesu waapacha mwayi wana wang'onoang'ono

13 Ndiipo wandhu wina adaapeleka wana waang'onoang'ono kwa Yesu kuti wasanjike manja ni kwaapembhela, nambho oyaluzidwa wake adaachekeleza wandhu wajha adaapeleka wana. 14 Yesu wadaakambila, "Alekeni wana waang'onoang'ono ajhe kwaine, msachekeleza, pakuti Ufumu wa kumwamba ni wa wandhu ali ngati wanawa."

15 Ndiipo wadaasanjika manja ni kwaapembhela, ndiipo wadachokapo pa malo pamenepo.

Mnyamata wopata

16 Mundhu mmojhi wadamchata Yesu ni kumfunjha, "Oyaluza, nichite chiyani chabwino kuti nipate umoyo wa wosatha?"

17 Yesu wadamfunjha, "Ndandeyanjii mnifunjha kuusu chindhu chabwino? Palibe mundu uyo wali wabwino nambho mmojhipe. Ukafuna kulowa mu umoyo wamuyaya, gwila thauko la Mnungu."

18 Mundhu yujha wadamfunjha, "Mathauko yati?"

Yesu wadamuyangha, "Usadapha, usadachita chigololo, usadaba, usadakamba mthila, 19 alemekeze atate wako ni maye wako, ni mkonde mnjako ngati umo ujhikondela umwene."

20 Mnyamata yujha opata wadayangha, "Yaya yonjhe nayagwila, bwanji, nachepekela chiyani?"

21 Yesu wadamuyangha, "Ngati ufuna ukhale ngati umo wafunila Mnungu, pita ukaguliche chuma chako chonjhe ni ndalamazo ukaagawile osauka, nawenjho siukhale ni chuma kumwamba, ndiipo unichate."

22 Mnyamatayo yapo wadavela chimwecho, wadabwelela kwao kwa chisoni, pakuti wadali ni chuma chambili.

23 Pamenepo Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Zene nikukambilani, siikhale kolimba kwa mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa kumwamba. 24 Nikukambilaninjho, ikhozeka chinyama icho chitanidwa ngamila kupyola pa ndhoolo kasindano kusiyana ni mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa Mnungu."

25 Oyaluza wake yapo adavela chimwecho adadabwa, adamfunjha, "Chipano ni yani uyo wakhoza kuomboledwa?"

26 Yesu wadaapenyecha ni wadakambila, "Vindhu ivi kwa mundhu sivikhozekana, nambho kwa Mnungu vindhu vonjhe vikhozeka."

27 Ndiipo Petulo wadamuyangha, "Ife tasiya vonjhe ni kukuchata iwe. Bwanji, tipata chiyani?"

28 Yesu wadaakambila, "Uzene nikukambilani, pa jhiko la mpya, Mwana wa Mundhu siwakhale pa mpando wa chifumu wa ulemelelo, anyiimwe mwanichata ine simukhale pamipando khumi ni iwili nimwaalamula mafuko khumi ni yawili ya Izilaeli. 29 Mundhu walionjhe uyo wasiya nyumba yake, kapina achakulu wake kapina mlongo wake kapina atate wake kapina maye wake kapina wana kapina munda ndande ya ine, mmeneyo siwachuluchidwe kambili kwa vijha walinavo ni siwaupate umoyo wamuyaya. 30 Nambho ambili yao ali oyamba saakhale othela ni wajha ali wothela saakhale oyamba."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-