Publicidade

Romanos 9

Mnungu ni wandhu wake Aizilaeli

1 Nikamba uzene okhaokha, ine nalunjana ni kilisito. Mtima wanga uku ni uchogozedwa ni Mzimu wa Mnungu ulangiza kuti sinikamba unami. 2 Nifuna kukamba chimwechi nili ni chisoni chachikulu ni kupwetekedwa kwa kukulu mumtima mwanga, 3 ndande ya achaabale wanga yawo ali a jhiko langa! Ngati chindhu ichi chidakathangatila anyiiwo, nidakavomela kulesedwa ni kupatulidwa ni Kilisito. 4 Achameneo nde wandhu a Kuisilaeli yao Mnungu wadasanghula akhale wana wake, wadaachita akhale pamojhi ni ulemelelo, wadachita chipangano ni anyiiwo, wadapacha thauko lake, kulambila kwa zene ni yajha wadakambila kuti siwapache. 5 Achamenewo Aizlaeli ni ajhukulu a mambuye, niiye Kilisito kwa kubadwa ngati mundhu, wachoka ku fuko lao. Mnungu walamulile pamwamba pa yonjhe, ni watamandidwe muyaya! Ikhale chimwecho.

6 Osati kuti mau la Mnungu lang'anamulidwa, pakuti osati wandhu wonjhe a ku Isilaeli apatulidwa ni Mnungu. 7 Osati mibadwa yonjhe ya Ibulahimu ni wana wake a zene. Nambho, ngati umo yalembedwa mmalembo ya Mnungu, "Mibadwa yake siichokane ni Isaka." 8 Mate yake kuti, osati wajha abadwa ngati wandhu umo abadwila nde Wana a Mnungu, nambho ni anyiwajha abadwa kuchokana ni ahadi ya Mnungu nde satanidwe wana a Ibulahimu. 9 Pakuti mawu wadakamba Mnungu nde yaya, "Ndhawi ngati ino pachaka sinibwele, niiye Sala siwapate mwana wa mmuna."

10 Osati yameneyope, chinchijha Labeka naye siwapate wana amawila kwa tate mmojhi, yani Isaka tate wathu. 11 Nambho dala Mnungu aoneke kuti ali ni ufulu osangha, wana amawila amenewo akali sadabadwe, ni akali saadajhiwe kuchita chindhu cha bwino kapina choipa, 12 Labeka wadakambidwa kuti yujha mwana wa woyamba siwamtumikile yujha wambuyo. Chimwecho kusanghula kwa Mnungu uchokana ni umo wafunila mwene, niosati machitidwe ya wandhu. 13 Ngati umo malembo ya Mnungu yalembedwa, "Yakobo nidamkonda, nambho Esau nidamuipila,"

14 Chipano tikambe chiyani? Bwanji Mnungu siwachita umo ifunikila? Notho! 15 Pakuti Mnungu wadamkambila Musa, "Sinimlengele lisungu mundhu waliyonjhe uyo sinifune kumlengela lisungu, sinimlengele lisungu mundhu waliyonjhe uyo nimfuna." 16 Chimwecho yonjhe yakhulupila lisungu la Mnungu, nambho siya khulupilila bidii kapina kufuna kwa mundhu. 17 Pakuti malembo ya Mnungu yakamba chimwechi kwa nghani ya Falao, "Nidakuchita kukhala mfumu kuti kupitila iwe, nilangize mbhavu zanga, ni jhina langa lijhiwike." 18 Chimwecho Mnungu wamlengela lisungu mundhu wafuna kumlengela lisungu, niwakafuna kumchita mundhu wakhale wambuli wachita chimwecho.

Mbhwayi ya Mnungu ni lisungu la Mnungu

19 Kapina siunifunjhe, "Ngati vindhu vili chimwecho, Mnungu wakhoza kumlaumu mundhu? Yani wakhoza kuchuchana ni umo wafunila iye?" 20 Nambho iwe mundhu iwe ni yani ata uyesa kumfunjha Mnungu? Bwanji mphika ukhoza kumfunjha uyo wauumba, "Ndande yanji waniumba chimwechi?" 21 Uyo waumba mphika wakhoza kulipotela njhito dothi umo wafunila ni kuumba miphika iwili kwa dothi limwelijha, umojhi kwa kutumila kwa ulemu, ni china ku kutimia kwa kawaida.

22 Chimwecho nde umo ili kwa Mnungu. Wamafuna kutilangiza mbhwayi yake ni kutijhiwicha mbhavu zake. Wamaembekeza ni kwaalimbila mtima kupunda anyiwajha wamafunika kuphezana ni mbhwayi yake? 23 Mnungu waadafuna kulangiza kuchuluka kwa ulemelelo wake uwo wadatipungulila kwa kutilengela lisungu, ife wadatikonjekela kwa kulandila ulemelelo wake. 24 Pakuti ife nde achameneo adaatana, osati kuchoka kwa Ayahudipe nambho kuchoka kwa wandhu amaiko yonjhe. 25 Pakuti nde umo wakambila mchikalakala cha mlosi Osea,

"Wandhu anyiwajha adali osati wanga

sinaatane ‘Wandhu wanga!’

Ni jhiko ilo sinidalikonde,

sinilitane ‘Wokondwedwa wanga!’

26 Nipajha adakambidwa ni Mnungu, ‘Anyiimwe osati wanga’

pamenepo satanidwe wana wa Mnungu uyo wali wamoyo."

27 Niiye mlosi Isaya, kwa nghani ya Izilaeli wadakweza mvekelo niwakamba, "Ata ngati mbadwa a Izilaeli ni ambili ngati mchenga wa mumtunda wa nyanja, ni ochepape yao salamichidwe, 28 Pakuti Mnugu siwalamule chisanga jhiko lonje." 29 Ngati mlosi wa Mnungu Isaya wadakamba poyambila, "Mbuye wa mbhavu zonjhe siwadakatisiilila wana akumojhi a Isilaeli, tidakatokala ngati Sodoma ni tidakatokhala ngati Gomola."

Kosakhulupilile kwa Izililaeli

30 Chipano tikambe chiyani? Wandhu anyiawo osati a Izilaeli siadafunefune kukhala ovomelezedwa ni Mnungu, apachidwa kuvomelezeka kwa njila ya chikhulupi. 31 Nambho a Izilaeli yao adafunafuna thauko la kwachita kukhala ovomelezeka ni Amnungu, siadalipate. 32 Ndande ya kukhulupila vichito vao pambuyo pa kukhulupilila chikhulupi. Chimwecho, adajhikwala pamwamba pa mwala ujha "Ukwiicha." 33 Ngati umo yalembedwela mmalembo ya Mnungu yalembela,

"Penya siiniike kumeneko kusayuni mwala wa kujhikwala,

mwala uwo siwachite wandhu agwe.

Nambho uyo siwamkhulupilile siwapata njhoni!"

Veja também

Publicidade
Romanos
Ver todos os capítulos de Romanos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-