1 Tikambe chiyani chipano, nghani za Ibulahimu tate wathu iye ngati mundhu, wadajhiwa bwanji chindhu ichi cha kuvomelezeka pachogolo pa Mnungu? 2 Ngati Ibulahimu wadali wovomelezeka kwa Mnungu ndande ya mbhavu zake, basi wali ni chindhu chojhidamila pachogolo pa Mnungu. 3 Pakuti malembo yoyela yakamba, "Iblahimu wadaakhulupilila Amnungu, nawo Amnungu adamvomela kukhala ovomwelezeka." 4 Uyo wachita njhito walipidwa mkokolo wake, osati mbhaso nambho ni kuvomelezeka kwake. 5 Nambho mundhu uyo siwakhulupilila vichito vake mwene, nambho wakhulupila Mnungu uyo walekeleledwa voipa, chimwecho Mnungu wasamala chikhulupi cha mundhu mmeneyo, ni kumvomela kukhala woyela. 6 Naye Daudi wakambanjho chimwecho ndande ya kukondwa uko walinako mundhu uyo wavomelezedwa ni Mnungu kuti ni woyela, popande kukhulupilila vichito vake,
7 "Sakondwele wandhu yawo alekeleledwa machimo yao,
yawo machimo yao vafutidwa.
8 Siwakondwele kupunda mundhu yujha, Ambuye sayakumbukila machimo yake!"
9 Bwanji kukondwela kumeneko kukambidwa ni Daudi ni kwaanyiwajha achitidwa mdulidwepe mate yake Ayahudi, kapina ni kwaanyiwajha siadachitidwe mdulidwe mate yake wandhu yawo osati Ayahudi? Ni kwaanyiwajha sadachitidwe mdulidwe. Pakuti tathokamba, "Ibulahimu wadaakhulupilila Amnungu, niiwo Amnungu adamvomele kukhala woyela wakali siwadachitidwe mtulidwe." 10 Bwanji Ibulahimu wadavomelezeka ni Mnungu wakali siwadachitidwe mdulidwe Kapina yapo wadachitidwa mdulidwe? Yapo wadali wakali siwadachitidwe mdulidwe niosati yapo wadachitidwa mdulidwe. 11 Iblahimu wadachitidwa mdulidwe pambuyo, ni chikuchitidwa mdulidwe kumeneko kudali chizindikilo icho chidalangiza kuti Mnungu wadamvomela kukhala wa bwino, ndande ya chikhulupi chake icho wadali nacho yapo wadali wakali siwadachitidwe mdulidwe. Mchimwecho, Ibulahimu wakhala tate wa wajha wonjhe amkhulupilila Mnungu ingakale siadachitidwe mdulidwe, kuti ata anyiiwo avomelezeke pachogolo pa Mnungu. 12 Chimchijha Ibulahimu ni tate wa anyiwajha achitidwa mdulidwe, nambho osati ndande achitidwa mdulidwe, nambho ndande adakhulupilila ngati umo wadakhulupilila tate wathu Ibulahimu yapo adali akali sadachitidwe mdulidwe.
13 Mnungu wadamkambila Ibulahimu ni mbadwa wake kuti jhiko lidakakhala lao. Ahadi imeneyo sidachitike ndande Ibulahimu wadachata Thauko, nambho ndande wadakhulupilila Mnungu ndiipo Mnungu wadamchita kukhala wa bwino. 14 Pakuti ngati yawo sapachidwe yayo ayakamba Amnungu niwajape avela thauko, chimwecho chikhulupi chilibe mate yaliyonjhe, ni icho achikamba Amnungu osati chindhu cha mate. 15 Thauko lipeleka mbhwayi ya Mnungu, nambho ngati kulibe thauko siikhozekena kuliwananga thauko.
16 Ndande imeneyo, chindhu ichi wakamba Mnungu kuti siwachite likhulupilila kumkhulupilila iye, mawu yameneyo yakambidwa ni Mnungu yachokana ni ubwino wake, ni zene kuti yajha wayakamaba kuti siwatipache, siwatipache wonjhe, niosati kwaanyiwajhape avela thauko, nambho ni anyiwajha akhala kwa kumkhulupilila Mnungu ngati Ibulahimu. Iye ni tate waife taonjhe. 17 Ngati umo yalembedwela mmalembo ya Mnungu, "Nakuika ukhale tate wa wandhu a maiko yambili." Mawu yameneyo ni ya uzene pachogolo pa Mnungu uyo wadamkhulupilila Ibulahimu, Mnungu uyo waapacha wandhu akufa umoyo, ni kwa lamulo lake vindhu ivo sividakhalepo vikhalapo. 18 Ibulahimu pajha wadakambidwa mawu yajha yadali yolimba kuyakhulupila, nambho Ibulahimu wadaendekela kukhulupilila kuti Mnugnu siwamchite kukhala tate wa wandhu a maiko yambili, ngati umo yalembedwa mmalembo, "Mibadwa yako siikhale yambili ngati ndhondwa!" 19 Wadali mzee, ni vyaka vake vidawandikila miya mojha nambho pamojhi ni chimenecho chikhulupililo chake sichidachepekele ata ngati wadajhiwa kuti siwakhozanjho kupata mwana thupi lake lidali ngati lafa ni mkazake sala wadali wambende. 20 Ibulahimu siwadakhaikile lijha lidakambidwa ni Mnungu, wadapata mbhavu kuchokana ni chikhulupililo, wadayendekela kumkhulupilila ni kumpacha ulemelelo. 21 Ibulahimu wadajhiwa zenedi kuti Mnungu wakhoza kuyakwanilicha yajha wadakamba kuti siwatipache. 22 Iyi ndendande iyo Mnungu wadamvomelela Ibulahimu kukhala wabwino. 23 Chimwecho mawu yaya yalembedwa kuti, "Mnungu wadamvomela Ibulahimu kukhala wabwino" Siyadalembedwe ndande yaiyepe. 24 Nambho chindhu chimecho ni cha ife timkhulupilila Mnungu uyo wadamuhyukicha Yesu, Ambuye wathu. 25 Iye wadachochedwa wapedwe ndande ya machimo yathu, wadahyuka ndande ife tivomelezeke.