Publicidade

Gálatas 2

Poolo wavomelezeka ni atumwi wina

1 Yapo vidapita vyaka kumi ni vinai nidapitanjho ku mujhi wa Yelusalemu pamojhi ni Banaba, chinchijha nidapita pamojhi ni Tito. 2 Nidapita kumeneko pakuti Mnungu wadanikambila nipite kumeneko, nidakhala nawo achogoleli kwa wokha, nidafotokozela Uthenga Wabwino ujha nilalikila kwa wandhu yawo asati Ayahudi. Nidachita chimwecho dala njhito yanga iyo nidaichita, niijha niichita saino isadakhala ilibe mate. 3 Adavomelezana ni ine, ata mnjanga Tito uyo wali Mgiliki, ingakhale siwadali Muyahudi siadamkakamize kuchitidwa mdulidwe, 4 ata ngati kudali ni wandhu wina yao amajhichita kuti mkhulupilila Kilisito yawo adafuna wachitidwe mdulidwe. Wandhu anyiyawa adalowa kwa kuchenjela ni kufujhila ufulu wathu tilinalo pa kulunjana ni Yesu Kilisito, dala akhoze kutichita makapolo a thauko la Musa. 5 Sitidavomelezane nawo ata pang'ono, dala uzene wa Uthenga Wabwino uendekele kukhala pamojhi ni anyiimwe muyaya.

6 Nambho achogoleli achamenewo alemekezeka kupunda, adalibe chindhu chonikambila. Zenedi adalemekezeka kupunda, nambho kwanga asati kandhu ndande Mnungu asiwamkondelela mundhu. 7 Pambuyo pake, adajhiwa kuti Mnungu wadathonituma kualalikila Uthenga Wabwino kwa wandhu anyiyawo asati Ayahudi ngati mujha Petulo wadatumidwa kwalalikila Ayahudi. 8 Mnungu uyo wadamkhozecha Petulo kukhala mtumwi kwa Ayahudi, nde mmweyo uyo wanikhozecha ine kukhala mtumwi kwa wandhu asati Ayahudi. 9 Ndiipo Yakobo, Petulo ni Yohana anyiiawo aoneka kuti ni achogholeli wakulu, adajhiwa kuti Mnungu wadanipacha ubwino umeneo, adavomela kugwilizana niine ni Banaba. Ife tidavomelezana tikachite njhito ya wandhu asati Ayahudi, nianyiiwo apite kwa Ayahudi. 10 Adatipembha chindhu chimojhipe, takumbukile osauka, nanenjho nichichita chindhu chimenecho.

Poolo wamnyindila Petulo ku mujhi Antiokia

11 Petulo yapo wadafika ku mujhi wa Antiokia ine nidamnyindila padanga ndande wadatholakwila. 12 Poyamba, yapo adali akali sadajhe wandhu yao adatumidwa ni Yakobo, Petulo wamatokudya ni wandhu yawo osati Ayahudi. Nambho yapo adajha wandhu ameneo, wadasiilatu kudya ni wandhu yawo osati Ayahudi, kwakuopa ghulu la wandhu yao akakamiza wandhu achitidwe mdulidwe. 13 Ayahudi wina yawo adakhulupilila adavomelezana nayo, ata Banaba nayo wadavomelezana ni ughunghuli wao. 14 Yapo nidaona kuti vichito vao sivilingana ni uzene wa Uthenga Wabwino, nidamkambila Petulo pachogholo pa wandhu wonjhe kuti, "Atangati iwe ni Myahudi, umo ukhalila ni wandhu wina ukhala ngati wandhu yawo osati Ayahudi, siukhala ngati Myahudi! Ukhoza bwanji kwakakamiza wandhu yawo osati Ayahudi kukhala ngati Ayahudi?"

Ayahudi ni wandhu yawo osati Ayahudi aomboledwa kwa kukhulupilila

15 Zenedi ife ni Ayahudi ko badwa, ni asati ngati wandhu amaiko yina yayo Ayahudi ayatana ochita machimo! 16 Tijhiwa uzene kuti mundhu siwakhoza kukhala wovomelezeka pachogolo pa Mnungu kwa kugwila thauko, nambho kwa kumkhulupila Yesu Kilisito. Ife Ayahudi nafe tamkhulupilila Yesu Kilisito kuti tikoze kuvomelezeka ni Mnungu kwa kupitila chikhulupi chatu kwa Kilisito, ni asati kwa kuchata thauko ndande palibe mundhu ata mmoji wakoza kuvomelezeka ni Mnungu kwa kuchata thauko. 17 Chipano tikafuna tivomelezedwe ni Mnungu kwa kulunjana ni Kilisito, ife sitioneke kuti niamachimo. Bwanji, chindhu ichi mate yake nikuti Kilisito watitangatila kuchita machimo? Siikhozeka ata pang'ono! 18 Ngati sinileke kuchata thauko dala nipate kuvomelezedwa pachogolo pa Mnungu, ndiponjho nikayamba kuchata thauko pamenepo sinikhale wamachimo. 19 Pakuti kwa thauko limenelo, ine namwalila, thauko lene lidanipa, nikhoze kukhala ndande ya Mnungu. Ine napachikidwa pamtanda pamojhi ni Kilisito, 20 nisaino nikhala wamoyo, nambho asati inenjho, nambho ni Kilisito wakhala mkati mwanga, ukhalo uno nikhala saino nikhala kwa kukhulupilila. Kukhulupilila kwanga kuchokana ni Mwana wa Mnungu, uyo wadanikonda ni wadauchocha umoyo wake ndande yanga. 21 Sinifuna kuukana mwawi wa Mnungu. Ngati mundhu wachitika wovomelezeka kwa Mnungu kwa njila yochata thauko, chimwecho nyifa ya Kilisito ilibe mate!

Veja também

Publicidade
Gálatas
Ver todos os capítulos de Gálatas
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-