1 Chipano, nghani ya kuchocha njhembe ndande ya wandhu a Mnungu, chitani ngati umo nidaatumizila gulu la wandhu amkhulupilila Yesu aku Galatia. 2 Kila jumapili, kila mmojhi wanu wapatule ndalama ni kuzisunga, kuchokana ni kupata kwake, dala sikudakhala ni vuto la kuzipata ndalama za kunipacha. 3 Chimwecho yapo sinijhe kwanu, sinaatume anyiwajha simwasanghule pakati panu apeleke kalata ku Yelusalemu ni ndalama zijha mwasunga. 4 Ngati siifunike niine nipite, simkhale paulendo pamojhi ni ine.
5 Sinijhe kwanu pambuyo pakupitila ku Makedonia pakuti nifuna kupitila ku Makedonia. 6 Ikhozeka sinikhale kwanu kwa ndhawi kapina kukhala namwe nyengo yonjhe yo zizila, dala mukhoze kunithangatila pa ulendo wanga kwalikonjhe uko sinipite. 7 Sinikonda kupita kwanu msangamsanga nikuendekela ni ulendo, nifuna kukhala kwanu kwa masiku yambili, yapo Ambuye akanilola. 8 Nambho sinikhale pano pa Efeso mbaka ndhawi ya pwando la Pentekosite. 9 Mnungu wanipacha malo ya kuchita njhito yaikulu pano, nambho kuli ni wandhu ambili yao anichucha. 10 Nambho Timoseo wakajha, mtangatileni wakhale kwanu popande mandha, mate yake wachita njhito ya Ambuye chinchija ngati ine. 11 Ndiipo mundhu waliyonjhe wasada mdelela, nambho mmthangatileni kuti waende ulendo wake kwa mtendele, dala wajhe kwanga ndande ine nimlindilila pamojhi ni achabale wanga. 12 Nambho, kwa nghani za Apolo nampembelela kupunda wajhe kwanu pamojhi ni achabale, ingakhale siwamafune kujha chipano ila siwajhe wakapata malo.
13 Khalani maso, imani nganganga muchikhulupi, msadaopa, ni mkhale ni mbhavu. 14 Chitani kilakandu kwa chikondi.
15 Mumjhiwa Sitefana ni wandhu amnyumba mwake, ndeyao adali oyamba kumkhulupila Kilisito ku Akaya, niajhichocha kwathangatila wandhu a Mnungu, namwenjho nikupembhani, 16 ifunika mwalemekeze wandhu ngati achameneo mchite chijha akukambilani, chimchijha alemekezeni wandhu anyiyawo achita nawo njhito.
17 Nikondwa kuti Sitefana, Fotunato ni Akaiko ajha, ndande anyiyawa anipacha yajha yadachepekela yapo simudalipo, 18 pakuti anikondwelecha mumtima mwanga, ngati umo adakukondwelechani anyiimwe, chimchijha ifunika kwakumbukila wandhu amtundu uwu.
19 Magulu ya wandhu amkhulupilila Kilisito a kumeneko ku Asia yakulonjelani, Akila ni Pulisila pamojhi ni gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito ilo lili kukhomo kwao likulonjelani kupunda kwa kulunjana ni Ambuye. 20 Wandhu onjhe amkhulupilila Kilisito yawo alipano akulonjelani.
Lonjelanani kulangiza kuti mulinimtendele.
21 Ine Poolo nilemba moni zanga kwa jhanja langa namwene.
22 Waliyonjhe uyo siwaakonda Ambuye walesedwe!
Malanata mate yake, "Ambuye wathu majha!"
23 Napembha Ambuye Yesu aendekele kukuchilani vabwino.
24 Nikukondani mwaonjhe yawo mwalunjana ni Ambuye Yesu Kilisito.