1 Ngati mmojhi wanu wali ni mlandu ni mnjake, mpita bwanji kumpacha mlandu kwa wandhu samjhiwa Mnungu, pamalo pa kumpacha mlandu pachogolo pa wandhu amjhiwa Mnungu? 2 Bwanji simujhiwa kuti wandhu a Mnungu sialamule wandhu siamjhiwa Mnungu? Ikakhala wandhu yawo siamjhiwa Mnungu sialamulidwe ni anyiimwe, ndande yanji simudalamulila ata vindhu vaving'ono? 3 Bwanji mujhiwa kuti sitaalamule niatumiki a kumwamba a Mnungu? Bwanji yaya siyadapitilile umo tikhalila pajhiko! 4 Yapo kukhala ni nghani pamwamba pa vindhu vakawaida, bwanji mwatana akahale alamuli wandhu anyiyao sialilemekeza gulu lawandhu amkhulupilila Yesu? 5 Nikamba chimwechi ndande yake muone njhoni, bwanji zene kuti palibe ata mmojhi pakati panu uyo wali ni hekima kuti watataule vuto pakati pa abale amkhulupila Kilisito. 6 Pambuyo pake, mundhu mmojhi waokhulupilila Yesu wapeleka mlandu wandhu akhulupilila Yesu anjanu kwa anyiyao sadakhulupilile kulamula mlandu!
7 Kumeneko kukhala ni milandu pakati panu mwachinawene kulangiza mwalepela. Ndande yanjhi simdakavomela kuchitilidwa voipa, simbasa mvomele kulandidwa chuma chanu? 8 Pambuyo pake, mwachina wene nde mulanda ni kunyenga, ni yameneyo mwachitila anjanu yawo amkhulupilila Yesu! 9 Zene mujhiwa kuti anyiyawo achita voipa siapata ufumu wa Mnungu. Simdanyengeka Achigololo, kapina alambila viboliboli kapina akomana chithupi kumbuyo kwa maumbidwe, 10 kapina anghungu, kapina akhumbila kuipa, kapina alojhela, kapina otukwana, kapina alanda anyiyawa siaupata Ufumu wa Mnungu. 11 Akumojhi wanu adali amtundu umeneo. Nambho mudachukidwa ni mdakhala bwino kwa kuchochedwa machimo ni Mnungu, mwavomelezeka ni Mnungu kwa Ambuye Yesu Kilisito ni kwa Mzimu wa a Mnungu wathu.
12 Mundhu siwakhoze kukamba, "Navomelezedwa kuchita chindhu chilichonjhe." Yetu, nambho osati kila vindhu vali vabwino kwaiwe. Nikhoza kukamba navomelezedwa kuchita chindhu chilichonjhe, nambho sinifuna kulamulidwa ni chindhu chalichonjhe. 13 Ukhoza kukamba, "Chakudya ndande ya mimba, ni mimba ndande ya chakudya." Yetu, nambho Mnungu siwaviwanange vonjhe. Thupi osati ndande ya chigololo, nambho kwa kwaatumikila Ambuye, ni Ambuye ayasunga mathupi yathu ni kuyapacha chakudya. 14 Mnungu wadahyukicha Ambuye Yesu, ni siwatihyukichenjho ife kwa mbhavu zake.
15 Mujhiwa kuti mathupi yanu ni viwalo va thupi la Kilisito. Mukhoza kutenga chiwalo cha thupi la Kilisito ni kuchichita malo ya thupi la hule? Siikhozeka! 16 Pakuti uyo walunjana ni hule wakhala thupi limojhi ni huleyo yalembedwa mmalembo ya Mnungu, "Nao awili akhala thupi limojhi." 17 Nambho iye walunjana ni Ambuye wakhala mzimu umojhi ni Ambuye.
18 Chithaweni chigololo. Machimo yina yonjhe wachita mundhu wachita kubwalo kwa thupi lake, nambho mundhu uyo wachita chigololo wachita mkhati mwathupi lake mwene wake. 19 Simujhiwa kuti mathupi yanu ni nyumba ya Mzimu Wamnungu, uwo ukhala mkati mwanu ni uwo mwapachidwa ni Mnungu? Mathupi yanu osati yanu mwachinawene nambho ni ya Mnungu, 20 pakuti mdaghulidwa kwa mtengo wa ukulu. Tumilani matupi yanu kwa ulemelelo wa Mnungu.