1 Yesu yapo wadamaliza kukamba, wadachoka ni oyaluzidwa wake kupita kuchija la mchinje Keduloni. Pamenepo yapo idavyalidwa mitengo ya Mizeituni, wadalowa mmenemo iye ni oyaluzidwa wake. 2 Yuda, uyo wamafuna kumng'anamuka Yesu, wadapajhiwa pamalo pamenepo pakuti wamapita kumeneko mala zambili ni oyaluzidwa wake. 3 Ndiipo, Yuda wadaatenga asikali ni alonda kuchokela kwa ajhukulu waakulu ni Afalisayo, wadajha nao kubusitani watenga nyali, myenje ni vida. 4 Chimwecho Yesu yapo wadayajhiwa yonjhe yayo siyampheze, wadatulukila pachogholo pao, wadafunjha, "Mumfunafuna yani?"
5 Ndiipo adamuyangha, "Yesu wakunazaleti!"
Yesu wadakambila, "Ine nde mwene."
Yuda wadaima pamojhi nao. 6 Chimwecho, Yesu yapo wadaakambila, "Ine nde mwene," Adabwela kumbuyo, ni kughwa panjhi. 7 Yesu wadaafunjhanjho, "Mumfunafuna yani?"
Adayangha, "Yesu wa ku Nazaleti!"
8 Yesu wadaakambila, "Natho kukambilani kuti ine nde mwene. Chimwecho, ngati munifunafuna ine, asiyeni anyiyawa ajhipita." 9 Wadakamba yameneyo dala yakwanile mawu yayo wadakamba, "Anyiyao mudanipacha palibe uyo namsoweza."
10 Simoni uyo Yesu wadamtana Petulo wadali ni mpeni, wadausolola, wadamdula khutu la kwene mbowa wa mjhukulu wamkulu. Mbowa mmeneyo wamatanidwa Maluko. 11 Ndiipo, Yesu wadamkambila Petulo, "Bweza mpeni wako mthumba lake. Bwanji, sinida vutika mavuto yayo anipacha Atate?"
12 Ndiipo ghulu la asikali, ni wamkulu wa asikali Aloma ni alonda a Mnyumba ya Amnungu adamgwila Yesu, ni kummanga maluzi, 13 ni kumpeleka huti kwa Anasi, mpongozi wa Kayafa, uyo wadali mjhukulu wamkulu chaka chimenecho. 14 Kayafa mmeneyo nde uyo wadapacha mwambo Ayahudi kuti mbasa wafe mmojhi ndande ya wandhu ambili.
15 Simoni Petulo ni oyaluzidwa mwina uyo wamamchata Yesu. Oyaluzidwa mwinayo wamajhiwika ni mjhukulu wamkulu, chimwecho wadalowa pamojhi ni Yesu mkati mwa khumbi la mjhukulu wamkulu. 16 Nambho Petulo wadaima kubwalo pafupi ni chicheko. Chimwecho oyaluzidwa mwinayo uyo wamajhiwika ni mjhukulu wamkulu wadatuluka kubwalo kupita kukambana ni mwali uyo wamalonda pachicheko, Petulo walowe mkati. 17 Mbowa yujha, wamalonda pa chicheko wadamfunjha Petulo, "Bwanji, iwe mmojhi wa oyaluzidwa amundhu uyu?"
Petulo wadayangha, "Asati ine!"
18 Chimwecho mbowa ni alonda amaotha moto ndande kudali ni mbhepo. Ni Petulo nayo wadaima nao pamwepo kuotha moto.
19 Ndiipo mjhukulu wamkulu wadamfunjha Yesu nghani za oyaluzidwa wake ni mayaluzo yake. 20 Yesu wadamuyangha, "Nakamba ni wandhu padanga. Nyengo zambili nimayaluza munyumba za zokomanilana za Ayahudi ni mnyumba ya Mnungu, pamalo yapo aphezana Ayahudi onjhe, sinidakambe kandhu kobisa. 21 Ndande yanji unifunjha ine? Afujhe anyiyao avela icho nakambila. Anyiwo ajhiwa yayo nakambila."
22 Yapo waadakamba yameneyo mlonda mmojhi uyo wadaima pafupi nayo wadaombela mmanja waadakamba, "Bwanji umuyangha chimwechi mjhukulu wamkulu?"
23 Yesu wadaadayangha, "Ngati nakamba kuipa, nilangize kuipako, ngati nakamba bwino, mbona unibula?"
24 Ndiipo Anasi wadampeleka Yesu waliomangidwa, kwa Mjhukulu Mamkulu wa Kayafa.
25 Petulo wamaotha moto. Adamfunjha, "Iwe uli mmojhi wa oyaluzidwa wake?"
Nambho Petulo wadakana ni kukamba, "Osati ine."
26 Mbowa mmojhi wa mjhukulu wamkulu, mbale wa mundhu yujha wadadulidwa kuthu ni Petulo, adamfunjha, "Ine nidakuona pamojhi naye ku busitani"
27 Petulo wadakananjho, posachedwe tambala wadalila.
28 Ndiipo adamtenga Yesu kuchokela kwa Kayafa, adampeleka kuikulu. Idali mmalenga kucha, nambho anyiiwo sadalowe muikulumo, dala sadakhala najisi, akhoze kudya pasaka. 29 Chimwecho, wadaachota kubwalo, wadakamba, "Kuli loipa liti kwa mundhu uyu?"
30 Adamuyangha, "Ngati siwadakali oyipa mundhu uyu sitidaka mpeleka kwanu."
31 Ndiipo Pilato wadakambila, "Chipano mtengeni mwachinawene, mumlamule kuchokana ni thauko lanu."
Ayahudi adayangha, "Ife tilibe lamulo la kupha mundhu waliyonjhe." 32 Idachitika chimwecho dala yakwanile mawu yayo wadakamba Yesu kulangiza nyifa yanji iyo siwafe.
33 Ndiipo Pilato wadalowanjho mnyumba yake ya chifumu, ni kuagiza Yesu wapelekedwe wadamfunjha, "Bwanji iwe nde Mfumu wa Ayahudi?"
34 Yesu wadamuyangha, "Yameneyo maganizo yako kapina akukambila wandhu nghani zanga?" 35 Ndiipo Pilato wadayangha, "Bwanji ine Myahudi? Jhiko lako ni ajhukulu akupeleka kwanga. Walakwa chiyani?"
36 Ndiipo Yesu wadayangha, "Ufumu wanga asati wajhiko lino. Ngati Ufumu wanga udakali wajhiko lino, ochatila wanga adakani menyela nghondo sinidagwilidwa ni Ayahudi. Nambho ufumu wanga asati wa jhiko lino."
37 Chimwecho Pilato wadamkambila, "Chipano iwe Mfumu?" Yesu wadayangha, "Iwe umo wakambila kuti ine Mfumu. Ine nabadwa dala nikhale mfumu, kwa ndande imeneyo najha pajhiko kwakambila wandhu uzene. Kila mundhu wazene wavela mvekelo wanga."
38 Pilato wadamkambila, "Zene nde chiyani?"
Pilato yapo wadakamba yameneyo, wadachotanjho Ayahudi kubwalo, wadakambila, "Ine sinidachione chilichonjhe icho walakwa mundhu uyu. 39 Nambho kwanu kuli ni chikhalidwe kuti ndhawi ya Pasaka nimmasulile omangidwa mmojhi. Chipano mfuna nimmasulile Mfumu wa Ayahudi?"
40 Ndiipo adabula mapokoso, "Notho! Asati uyu nambho timasulileni Balaba!" Nayo balaba wadali olanda. Wadali ni alonda kuchokela kwa ajhukulu waakulu ni Afalisayo, wadajha nao kubusitani watenga nyali, myenje ni silaha.