Publicidade

João 10

Chifani cha owesa

1 Yesu wadakamba, "Zenedi nikukambilani, waliyonjhe uyo siwalowa mkhola la mbelele kopitila pachicheko, nambho wakwela ni kulowela pamalo pina, mmeneyo mnghungu ni olanda. 2 Nambho uyo walowa koopitila chicheko chimecho, mmeneyo nde owesa wa mbelele. 3 Mlonda wachakulila, ni mbelele zivela mvekelo wake, nayo wazitana mbelele kila imojhi kwajhina lake, ni kuzitulucha kubwalo. 4 Ndiipo wakatho zitulucha kubwalo wazichogolela mbelele, nazo zimchota, ndande ziujhiwa mvekelo wake. 5 Mbelele zimenezo sizikhoza kumchata mlendo, nambho sizimthawe ndande sizijhiwa mvekelo wake."

6 Yesu wakambila chifani ichi, nambho anyiiwo siadajhiwe icho wamakambila.

Yesu Owesa wa Bwino

7 Ndiipo wadakambilanjho, "Zene ni ikukambilani, ine ni chicheko cha mbelele. 8 Onjhe anyiyao adanichogolela anghungu ni olanda, ni mbelele sizidavechele. 9 Ine ni chicheko. Mundhu waliyonjhe uyo siwalowe kupila ine siwaomboke, siwalowe ni kutuluka, ni kupheza dyela. 10 Mnghungu wakujha kuti wabe, kupha ni kuwananga. Ine nidajha kuti mukhale ni umoyo wa muyaya chimwecho akhale nawo siku zonjhe."

11 "Ine owesa wabwino. Owesa wabwino wachocha umoyo wake ndande ya mbelele zake. 12 Owesa wa mkokolo, ni mbelele osati zake, yapo waona mibinji, wazisiya mbelele ni kuthawa, chimwecho mibinji izigwila ni kuzisiyanicha. 13 Iye wathawa ndande ni owesa wa mkokolo, iye siwasamala mbelele. 14 Ine ni owesa wabwino. Nizijhiwa mbelele izo zili zanga, ni mbelele zanga zinijhiwa ine, 15 ngati Atate umo anijhiwila ine, nane umo najhiwila Atate. Niuchocha umoyo wanga ndande ya anyiiwo. 16 Ni nili ni mbelele zina palibepo mkhola umu. Ifunika nijhenawo, nawo savele mvekelo wanga, ni sikukhalepo ni gulu limojhi ni owesa mmojhi."

17 "Ndande iyi, Atate anikonda ni kuuchocha umoyo wanga kuti niulandilenjho. 18 Palibe uyo wanilanda umoyo wanga, ine niuchocha namwene. Nikhoza kuuchocha ni nikhoza kuutenganjho. Nde umo Atate anilamulila nichite."

19 Kudali ni kulimbananjho pakati pa Ayahudi ndande ya mawu yayo wamayakamba Yesu. 20 Ambili pakati pao adakamba, "Wali ni viwanda, ni opande njelu! Ndande yanji timvechele?"

21 Wina adakamba, "Mawu yaya osati ya mundhu wa viwanda. Bwanji mundhu wa chiwanda wakhoza kulamicha maso ya mundhu siwapenya?"

Yesu wakanidwa ni Ayahudi

22 Ndhawi imeneyo idali ndhawi yozizila, ndiipo kudalipo ni phwando la kuielechanjho nyumba ya Amnungu ku Yelusalemu. 23 Yesu nayo wamatoenda mu nyumba ya Mnungu mu msasa wa Solomoni. 24 Chimwecho gulu la wandhu lidamzungulila, lidamfunjha, "Siutiike mmaganizo mbaka siku lanji? Ngati iwe nde Kilisito, tikambile padanga."

25 Yesu wadayangha, "Nakukambilani nambho simuvomela. Njhito izo nichita kwa ulamuli wa Atate wanga linichochela umboni. 26 Anyiimwe simukhulupilila ndande anyiimwe osati mbelele zanga. 27 Ngati mujha mbelele zivela mvekelo wa owesa wao, wandhu wanga achijhiwa icho nichikamba nane najhiwa ni akhala ochatila wanga. 28 Ine napacha umoyo wamuyaya ni muyaya siasiana ni Amnungu. 29 Atate wanga yao anipacha mbelele zimenezo niwakulu kupitilila onjhe, palibe uyo wakhoza kuzichocha kwa Atate wanga. 30 Ine ni Atate wanga tili amojhi."

31 Ndiipo Ayahudi adatondolanjho miyala kuti amponye Yesu. 32 Yesu wadaakambila, "Nakulangizani njhito zambili kuchoka kwa Atate. Njhito iti pa zimenezo ikuchitani munibule miyala?"

33 Ayahudi adamuyangha, "Sitikuponya miyala ndande ya njhito za bwino, nambho ndande ya kwaatukwana Amnungu! Mate yake ujhichita iwe Amnungu, ni iwe ni mundhupe."

34 Ndiipo Yesu wadaayangha, "Bwanji, siidalembedwe mu malembo, kuti, ‘Ine nakamba anyiimwe ni minungu?’ 35 Ikhakala Amnungu wadaatana minungu wajha adapachidwa mawu la Amnungu, chimwecho malembo ya Amnungu ni ya uzene siku zonjhe. 36 Bwanji anyiimwe mkamba kuti nitukwana ndande nikamba ine ni mwana wa Amnungu? Ine Atate adanisangha ni kunituma pa jhiko la panjhi. 37 Ngati sinichita njhito iyo natumidwa ni Atate, simdanikhulupilila. 38 Nambho ngati nizichita njhito za Atate, atangati simunikhulupilila, zikhulupilileni njhito zimenezo, kuti mwajhiwe Atate ali mkati mwanga, nane nili mkati mwao."

39 Adaesanjho kumgwila nambho wadapulumuka mmanja mwao.

40 Ndiipo Yesu wadapitanjho ku chija la mchinje Yolodani, pamalo yapo wamabatizila Yohana, wadakhala kumeneko. 41 Wandhu ambili adamchata adakamba, "Yohana siwadachite chizindikilo chilichonjhe. Nambho yonjhe yayo wayakamba Yohana kuusu mundhu uyu yazene." 42 Wandhu ambili adamkhulupilila Yesu pamalo pamenepo.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-