1 Yesu waadakambila, "Simudadandaula mumitima yanu. Mwaakhulupilila Amnungu, munikhulupilile ni ine. 2 Munyumba ya Atate wanga muli ni makhalo yambili, ngati siidakali chimwecho, nidakakukambilani. Chipano nipita kukukonjelani malo. 3 Nikapita kukukonjelani malo, sinibwele kukutengani mujhe kwanga, yapo nili ine namwe mukhalepo. 4 Anyiimwe mujhiwa mapitidwe ya uko nipita."
5 Tomaso wadamfunjha, "Ambuye, uko mpita ife sitikujhiwa, sitiijhiwe bwanji njila yopita kumeneko?"
6 Ndiipo Yesu wadamuyangha, "Ine namwene nde njila, naakambila wandhu uzene ni kwapacha umoyo wa muyaya. Palibe uyo wakhoza kupita kwa Atate ila kwanjila yanga. 7 Ngati munijhiwa ine, simwajhiwe ni Atate wanga. Ni kuyambila chipano, mwajhiwa, ni mwatho kwaona."
8 Filipo wadamkambila Yesu, "Ambuye tilangizeni Atate, kwatu ikwana."
9 Yesu wadamkambila, "Filipo nakhala namwe ndhawi yonjheyi, ukali osanijhiwe? Uyo waniona ine waona Atate. Ukamba bwanji, ‘Tilangizeni Atate?’ 10 Bwanji, siukhulupilila kuti ine nili mkati mwa Atate, ni Atate ali mkati mwanga? Mawu yayo nikukambilani osati kwa lamulo langa, Atate yawo alimkati mwanga achita njhito zao. 11 Ifunika munikhulupilile yapo nikamba nili mkati mwa Atate ni Atate alimkati mwanga. Ngati osati chimwecho mnikhulupilile kwa njhito izo nizichita. 12 Zene nikukambilani, uyo wanikhulupilila siwachite vindhu ivo nichita ine, ni siwachite vavikulu kupunda, ndande nipita kwa Atate. 13 Chilichonjhe icho simupembhe ngati umo nifunila sinichite, dala Atate apachidwe ulemelelo mkati mwa Mwana. 14 Mkanipembha chilichonjhe ngati umo nifunila, sinikuchitileni."
15 "Ngati mnikonda malamulo yanga yawo nikupachani simuya chitile njhito. 16 Sinaapembhe Atate nawo sakupacheni Wakukuthandizani mwina, uyo siwakhale namwe muyaya. 17 Iye ni Mzimu wa zene. Jhiko lapanjhi silikhoza kumlandila ndande silimuona kapina kumjhiwa. Nambho anyiimwe mumjhiwa ndande wakhala namwe ni wali mkati mwanu."
18 "Sinikusiyani amasiye, sinijhenjho kwanu. 19 Ikali ndhawi yochepa wandhu ajhiko la panjhi sanionanjho, nambho anyiimwe simunione, pakuti ine nili wamoyo namwenjho simukhale moyo. 20 Ndhawi ijha ikafika simujhiwe kuti ine nilimkati mwa Atate, namwe muli mkati mwanga ni ine nilimkati mwanu."
21 "Uyo wayalandila malamulo yanga ni kuyagwila, mmeneyo nde uyo wanikonda. Uyo wanikonda ine siwakondedwe ni Atate wanga, nane sinimkonde ni kujhijhiwicha kwa iye."
22 Chimwecho Yuda nambho osati Isikaliyote adamkambila, "Ambuye, sikhozeke bwanji mujhilangize kwa ife ni osati kwa jhiko?"
23 Yesu wadayangha, "Wandhu yao anikonda akalichitila njhito mawu langa ni Atate wanga saakonde, nafe sitijhe kwa anyiiwo ni kukhala pamojhi nawo. 24 Uyo siwanikonda siwayachitila njhito mawu yanga. Uthenga uwo muuvela osati wanga nambho uchokela kwa Atate yao anituma."
25 "Nikuyaluzani vindhu ivi nikali pamojhi namwe, 26 nambho Othandiza, Mzimu woyela, uyo samtume kukhala mmalo mwanga, siwakuyaluzeni kila kandhu ni kukukumbuchani yonjhe yayo nakukambilani."
27 "Mtendele nikusiilani, nikupachani mtendele wanga. Yetu nikupachani osati ngati umo likupachilani jhiko la panjhi. Simudakhaikila mumtima ni simdaopa. 28 Mudanivela yapo nimakamba, ‘Nipita ni sinibwelenjho kwanu.’ Ngati mdanikonda, mdakakondwa ndande nipita kwa Atate, mateyake iwo wakulu kusiyana niine. 29 Chipano nakukambilani yakali yosa chokele, ndande yapo siyachokele mukhulupilile. 30 Sinikamba namwenjho kopitilila, ndande mlamuli wa jhiko lino watokujha, kwaine siwakhoza kandhu, 31 nambho wandhu ajhiko lino afunika kujhiwa kuti ine naakonda Atate, nde ndande nichita ngati umo anilamulila Atate."
"Imani tijhipita!"