Publicidade

João 2

Ukwati mmujhi wa Kana

1 Siku la katatu kudali ni ukwati mmujhi wa Kana, mkoa wa ku Galilaya, nawo amaye wake Yesu adalipo pamwepo, 2 Yesu naye wadalalikidwa pa ukwati pamojhi ni oyaluzidwa wake. 3 Divai yapo idatha, amaye wake adamkambila Yesu, "Divai yatha."

4 Ndiipo Yesu wadayangha amaye wake, "Ndandeyanji munikambila nghani imeneyo. Ndhawi yochita njhito yanga ikali yosafika."

5 Chimwecho amake adazikambila mbowa, "Chilichonjhe icho siwakukambileni, chitani,"

6 Pamenepo padali ni mapipa sita ya myala, iyo yaikidwa kwa chikhalidwe chakusamba cha Chiyahudi, kila mchuko udakakhoza kutenga michuko ya wili kapina itatu ya majhi. 7 Ndiipo Yesu wadaakambila, "Jhazani majhi mmapipa." 8 Ndiipo wadaakambilanjho, "Chipano tungani mkampelekele wamkulu wa phwando." 9 Wamkulu waphwando yapo wadalawa majhi yameneyo, wadapeza yang'anamuka kukhala divai. Siwada jhiwe uko ya choka, nambho anyiyawo adatunga majhi adajhiwa. Wamkulu wa phwando wadamtana wammuna wa ukwati, 10 wadamkambila, "Kila mudhu wayamba kwapacha wandhu divai ya bwino uti, ni akathokumwa ni kukwana, wakonja ijha yosakome. Nambho iwe wachocha divai ya bwino mbaka saino."

11 Yesu wadachita chizindikilo ichi choyamba ku Kana, ya ku Galilaya wadaalangiza ulemelelo wake, ni oyaluzidwa wake adamkhulupilila.

12 Pambuyo, Yesu wadachika pamojhi ni amaye wake ni achabale wake ni oyaluzidwa wake, adapita ku Kapelinaumu uko adakhala kwa masiku yochepa.

Yesu wapita ku Nyumba ya Amnungu

13 Phwando la Pasaka la Ayahudi lidawandikila, chimwecho Yesu wadakwela kupita ku Yelusalemu. 14 Ndiipo wadaapheza wandhu mujha mu Nyumba ya Amnungu niaghulicha ng'ombe, mbelele ni nghunda ni ong'anamula ndalama akhala pa gome. 15 Wadakonja mkwapulo wa maluzi, nikwatopola onjhe apite kubwalo pamojhi ni ng'ombe ni mbelele zao, wadataya ndalama za anyiyao amang'anamula ndalama ni kuzigadabula gome zao. 16 Wadakambila anyiwajha amaghulicha nghunda, "Chochani vindhu ivi pano. Simuda chita Nyumba ya Atate wanga kukhala pamalo pa malonda!" 17 Oyaluzidwa wake adakumbukila malembo yayo yalembedwa chimwechi, "Chikondi changa mu Nyumba mwanu siuniphe."

18 Ayahudi akumojhi adamfunjha Yesu, "Ukhoza kuchita chizindikilo chanji kulangiza kuti iwe uli ni ulamuli wochita vindhu ivi?"

19 Yesu wadaayangha, "Gomolani Nyumba ya Amnungu ino, nane siniimange kwa siku zitatu."

20 Ndiipo Ayahudi adamfunjha, "Nyumba ya Amnungu ino idamangidwakwa vyaka alubaini ni sita, bwanji iwe siukhoze kuimanga kwa siku zitatupe?"

21 Nambho Nyumba ya Amnungu iyo Yesu waichula ni thupi lake. 22 Yapo wadahyuchidwa, oyaluzidwa wake adakumbukila kuti wada kambapo chimwecho, ndipo adayakhulupilila malembo yoyela ni mawu yayo wadakamba Yesu.

Yesu waijhiwa mitima ya wandhu

23 Yesu yapo wadali ku Yelusalemu ku phwando la Pasaka, wandhu ambili ada mkhulupilila yapo adaona vizindikilo ivo wadachita. 24 Nambho Yesu siwadakhulupilile chikhulupi chao kwake, ndande onjhe wamaijhiwa mitima yao. 25 Siwadafune kukambilidwa chili chonjhe kuusu wandhu, pakuti wadavijhiwa vindhu vonjhe ivo vili mmitima mwawo.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_10-32-54-