1 Ndiipo Yesu wadakamba, "Ine ni mzabibu wa zene, ni Atate nde amlimi. 2 Ndhawi yaliyonjhe iyo siibala vipacho mkati mwanga, Atate aidula, ni ndhawi iyo ibala aikonjezela ijhipunda kubala. 3 Anyiimwe mwatho elechedwa muuzimu ndande ya uthenga uwo nidakuyaluzani. 4 Khalani mkati mwanga, ngati umo ine nikhalila mkati mwanu. Ngati umo ndhawi ya mzabibibu siikhoza kubala yokha vipacho popande kukhala mumtengo wa mzabibu, chimwecho anyiimwe simukhoza kuchita chijha achifuna Amnungu ngati simukhala mkati mwanga."
5 "Ine ni mzabibu, anyiimwe ni ndhawi. Yao akhala mkati mwanga, nane nikakhala mkati mwao, achameneo sachite vindhu vabwino vambili, popande ine simukhoza kuchita kandhu. 6 Mundhu wakasiya kukhala mkati mwanga wataidwa kubwalo ngati ndhawi ni kuuma. Ndhawi ngati zimenezo wandhu azikusa ni kuzitaya pamoto zipyelele. 7 Anyiimwe mkakhala mkati mwanga ni mawu yanga yakakhala mkati mwanu, chipano, pembhani chilichonjhe icho mfuna namwe simpachidwe. 8 Atate wanga apachidwa ulemelelo yapo mchita vindhu ivo vakwadilicha Amnungu, namwe simukhale oyaluzidwa wanga. 9 Ine nikukondani anyiimwe ngati umo Atate adanikondela ine. Khalani muchikondi changa. 10 Mkachita ngati umo afunila Atate ni kukhala muchikondi changa, ngati ine umo nichitila umo afunila Atate wanga ni kukhala mu chikondi chao."
11 "Nakukambilani vindhu ivi dala chimwemwe changa chikale mkati mwanu, ni chimwemwe chanu chikwanile. 12 Lamulo langa nde ili, mkondane ngati ine umo nidakukondelani anyiimwe. 13 Palibe chikondi chachikulu kupunda kusiyana ni chikondi cha mundhu uyo wachocha umoyo wake ndande ya bwenji lake. 14 Anyiimwe achabwenji langa mkachita yayo nikulamulani. 15 Sinikutananinjhoni mbowa, ndande mbowa siwajhiwa icho wachita wamkulu wake. Nambho ine nakutanani anyiimwe bwenji, ndande nakujhiwichani yonjhe yayo nayavela kuchoka kwa Atate. 16 Anyiimwe simudanisanghe ine, nambho ine nidakusanghani anyiimwe nakutumani mkachite ivo avifuna Amnungu, ni njhito azifuna Amnungu izo sizikhaliche siku zonjhe. 17 Chipano, lamulo langa kwanu nde ili, kondanani anyiimwe kwa anyiimwe."
18 "Ngati jhiko la panjhi likakuipilani anyiimwe, kumbukilani kuti lidaniipila ine likali kukuipilani anyiimwe. 19 Ngati mudakali wandhu ajhiko, jhiko lidakakukondani ngati wandhu wake. Pakuti anyiimwe osati ajhiko, nambho ine nakusanghani kuchoka mujhiko, ndendande wandhu ajhiko akuipilani. 20 Kumbukilani uthenga uwo nakukambilani, mbowa osati wamkulu kupitilila wamkulu wake. Ngati anivuticha ine, namwe sakuvuticheni, ngati adauchitila njhito uthenga wanga, siauchitile njhito uthenga wanu. 21 Nambho sakuchitileni yonjheyo ndande anyiimwe ni ochatila wanga, pakuti samjhiwa uyo wanituma. 22 Ngati sinidakajha ni kukamba mawu ya Amnungu sadakakhala ni machimo, nambho alibe chinamizilo kuti alibe machimo. 23 Uyo waniipila ine, waipila Atate. 24 Ngati nidakasiya kuchita vizindikilo pakati pao ivo sividachitidwepo ni mundhu waliyonjhe, sadakali ni machimo, chipano aviona vozizwicha nambho akali kuniipila ine ni Atate wanga. 25 Dala likwanile mawu ilo lidalembedwa mu malembo lao, ‘Aniipila popande cholakwa.’
26 "Yapo siwajhe othandiza uyo sinimtume kuchoka kwa Atate, Mzimu wauzene uyo wachokela kwa Atate, siwanichochele umboni. 27 Namwenjho simunichochele umboni pakuti mudali ni ine kuyambila mmayambo."