Publicidade

João 11

Kumwalila kwa Lazalo

1 Padali ni mundhu mmojhi wa ku Besania, wamatanidwa Lazalo, wamadwala. Wamakhala kuchijhijhi cha Besania kumeneko amakhala ni achalongo wake Malia ni Masa. 2 Malia uyu nde yujha wadaanyeka Ambuye mafuta ya mtengo wa ukulu yayo yanunghila ni kuichangula myendo kwa machichi yake. Mbale wake Lazalo nde uyo wadali odwala. 3 Chimwecho achalongo wake Lazalo onjhe adatuma uthenga kwa Yesu, "Ambuye mmbwenji lanu wadwala!"

4 Yesu yapo wadavela chimwecho, wadakamba, "Lazalo siwamwalila kwa utenda uno, nambho wadwala ndande ya kwaapacha Amnungu ulemelelo, wadwala dala Mwana wa Amnungu walemekezedwe kupitila utenda umeneo."

5 Yesu wadali ni ubwenji wa pamtima ni Masa ni Malia ni Lazalo. 6 Yapo wadavela kuti Lazalo wadwala, Yesu wadaendekela kukhala pamalo pajha wadali kwa masiku yawili. 7 Ndiipo pambuyo pa yameneyo, wadakambila oyaluzidwa wake, "Chipano tiyeni tibwelenjho ku Yudea!"

8 Oyaluzidwa wake adamkambila, "Oyaluza! Yapita ndhawi yo chepa Ayahudi yapo amafuna kuiiphani kwa myala, ndande yanji mfuna kupitanjho kumeneko?"

9 Yesu wadayangha, "Bwanji saa za usana osati khumi ni ziwili? Chimwecho mundhu akayenda usana siakhoza kujhikhuwala ndande aliona dangalila la jhiko lino. 10 Nambho usiku mundhu wajhikwala ndande dangalila palibemo mkati mwake." 11 Yesu yapo wadakamba mawu yameneyo, wadaakambila, "Mbwenji lathu Lazalo waghona litulo, nambho ine sinipite kumuucha."

12 Oyaluzidwa wake adamkaambila, "Ambuye ngati waghona, siwauke."

13 Anyiiwo amaghaniza wamakamba kuti waghona litulo, nambho wamakambilila nyifa ya Lazalo. 14 Ndiipo, Yesu wadakambila popande kwa bisa, "Lazalo wamwalila, 15 nambho nikondwa ndande sinidalipo kumenepo yapo Lazalo wamamwalila. Chipano tiyeni kukhomo lake."

16 Tomaso uyo watanidwa mawila wadaakambila oyaluzidwa achanjake kuti, "Tiyeni nafe tikafe pamojhi ni Ambuye!"

Yesu nde uhyucho ni umoyo

17 Yesu yapo wadajha kumeneko wadapheza chitanda cha Lazalo chatho khala siku zinayi mmainja. 18 Kijhijhi cha Besania chidali pafupi ni Yelusalemu, utali wa kilometa zitatu kuchoka ku Yelusalemu. 19 Ayahudi ambili adafika kwa masa ni Malia kwa tondeza kwa nyifa ya mlongo wao.

20 Chimwecho Masa yapo wadavela kuti Yesu watokujha, wadapita kumlandila nambho Malia wadakhala pakhomo. 21 Ndiipo Masa wadamkambila Yesu, "Ambuye, ngati mudakalipo pano, mlongo wanga siwadakafa! 22 Nambho nijhiwa kuti atangati chipano chilichonjhe icho siwapembhe Amnungu, sakupacheni."

23 Ndiipo Yesu wadamkambila, "Mlongo wako siwahyuke."

24 Masa wadayangha, "Nijhiwa kuti siwahyuke ndhawi ya uhyucho, siku lo thela."

25 Yesu wadamkambila, "Ine nde uhyucho ni umoyo. Uyo wanikhulupilila ine atangati wakamwalila, siwakhale moyo, 26 ni waliyonjhe uyo wakhala wa moyo ni khulupilila, siwamwalila muyaya. Bwanji ulikhulupilila ili?"

27 Masa wadamkambila, "Etu Ambuye! Ine nikhulupila kuti imwe nde Kilisito uyo wasanghidwa ni Amnungu, Mwana wa Amnungu, uyo wakujha pajhiko."

Yesu wamlilila Lazalo

28 Pambuyo pa yameneyo, Masa wadapita kumtana Malia kwa chisisi, wadamkambila, "Oyaluza alipano, akutanani." 29 Nayo yapo wadavela chimwecho wadaima msangu, ni kumchata Yesu. 30 Ni Yesu wadaliwakali osafike pa kijhijhi, wadali wakali pamalo pampajha wadalandilidwa ni Masa. 31 Ndiipo Ayahudi anyiyawo adali mnyumba ni amtondeza Malia yapo adamuona mujha waima ni kutuluka kubwalo chisanga, adamchata. Amaghaniza wapita kumanda kuomboleza.

32 Ndiipo, Malia yapo wadafika pamalo yapo wadali Yesu, wadagwada, wadamkambila, "Ambuye, ngati mudakali pano, mlongo wanga siwadakamwalila!"

33 Yesu yapo wadamuona maliya walila, ni Ayahudi anyiyao adajha pamojhi ni Maliya nayo alila, wadali ni chisoni ni kudandaula mumtima. 34 Ndiipo wadamfunjha, "Mwamzika kuti?"

Adamkambila, "Ambuye, majhani mpenye."

35 Yesu wadalila. 36 Chimwecho, Ayahudi adakamba, "Penyani umo wamkondela Lazalo!"

37 Nambho wina adakamba, "Uyu wadalamicha maso yujha sapenya, siwadakhoza kumlamicha Lazalo?"

Yesu wamuhyucha Lazalo

38 Ndiipo Yesu uku ni wadandaula mumtima, wadafika yapo idali manda. Manda ene idali mbhanga, ni ida vinikilidwa mwala. 39 Yesu wadakamba, "Uchocheni mwala!" Masa mlongo wake Lazalo, wadamkambila, "Ambuye, watho yamba kunungha, ndande wakhala mmanda siku zinai!"

40 Yesu wadaamkambila Masa, "Bwanji sinidakukambileni kuti ukakhulupilila siuone ulemelelo wa Amnungu?" 41 Ndiipo adauchocha ujha mwala. Yesu wadapenya kumwamba, wapemba, ni wakamba "Nikuyamikani Atate ndande mwanivela. 42 Nijhiwa kuti munivela siku zonjhe. Nakamba yameneyo ndande ya wandhu alipano kuti apheze kukhulupilila kuti imwe nde yao mwanituma." 43 Yapo wadamaliza kukamba yameneyo, wadatana kwa mvekelo waukulu, "Lazalo, majha kuno kubwalo!" 44 Yujha wadamwalila wadatuluka kubwalo, wali omangidwa sanda mmyendo ni mmanja, ni kumaso wavinikilidwa njhalu.

Yesu wadakambila, "Mmasuleni, mumsiye wajhipita."

Achogoleli wa Ayahudi apanga kumpha Yesu

45 Ndiipo, Ayahudi ambili anyiyao adafika ni Malia yapo adaona yayo wadachita Yesu, adamkhulupilila. 46 Nambho wina wao adapita kwa Afalisayo kwaapacha nghani ya ivo wadachita Yesu. 47 Chimwecho ajhukulu waakulu ni Afalisayo adachita msonghano wa bwalo la milandu lalikulu, adafunjhana, "Tichite bwanji? Mateyake mundhu uyu wachita vizindikilo vambili kupunda. 48 Ngati tikamsiya waendekele kuchita vizindikilo ivi kila mmojhi siwamkhulupilile iye, ni achogoleli a Aloma saajhe kutichochela ulamulilo wathu wa Nyumba ya Amnungu ni jhiko lathu!"

49 Mundhu mmojhi pakati pao uyo wamatanidwa Kayafa, uyo wadali mjhukulu wamkulu chaka chimenecho, wadaakambila, "Anyiimwe simujhiwa chindhu chilichonjhe! 50 Simujhiwa kuti mbasa wafe mmojhi ndande ya wandhu, kusiyana liwanangidwe jhiko lonjhe?" 51 Kayafa siwadakambe chimwecho kwa maganizo yake mwene, nambho ndande iye wadali mjhukulu wamkulu wachaka chimenecho, wadalosa kuti Yesu siwafe ndande ya jhiko la Ayahudi, 52 osati kuti siwamwalile ndande ya Ayahudi okha, nambho ndande ya kwaakusa pamojhi wana Amnungu anyiyao amwazika.

53 Ndiipo, kuyambila siku limenelo achogholeli wa Ayahudi adayamba kufunafuna njila ya kumpha Yesu. 54 Chimwecho, Yesu siwadaendenjho padanga pakati pa Ayahudi, ndiipo wadachoka pamenepo, ni kupita pafupi ni phululu, mmujhi uwo utanidwa Eflaimu. Wadakhala kumemeneko ni oyaluzidwa wake.

55 Pwando la Pasaka la Ayahudi lidawandikila, wandhu ambili adapita ku Yelusalemu kuti akajhieleche likali osajhe pwando limenelo. 56 Wandhu amamfunafuna Yesu. Yapo adali pamojhi mu Nyumba ya Amnungu, adafunjhana, "Bwanji mundhu uyu siwafika kupwando?" 57 Chimwecho ajhukulu waakulu ni Afalisayo adachocha lamulo kuti mundhu waliyonjhe uyo siwajhiwe uko wali Yesu waakambile dala amgwile.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-