Publicidade

Mateus 10

Atumwi khumi ni awili

1 Yesu wadaatana wandhu wake wajha wayaluza khumi ni awili, wadaapacha ulamulilo wakuchocha viwanda ni kulamicha wodwala ni mavuto yonjhe. 2 Maina ya atumwi khumi ni awili nde yaya, Simoni uyo watanidwanjho Petulo ni Anduleya uyo wadali mbale wake Petulo ni Yakobo mwana wa Zebedayo ni mbale wake uyo wadatanidwa Yohana, 3 Filipo ni Batolomayo, Tomaso ni Matayo uyo wamalandila malipilo, ni Yakobo mwana wa Alufayo, ni Tadeyi, 4 Simoni uyo wamabulanila jhiko lake, ni Yuda Isikalioti uyo wadamng'anamuka Yesu.

Yesu waatuma atumwi khumi ni awili

5 Yesu wadaatuma atumwi khumi ni awili wajha ni kwaalamula, "Msadapita kwa wandhu yawo samjhiwa Mnungu, kapina kulowa mmujhi wa Asamaliya. 6 Nambho pitani kwa wandhu a jhiko la Izilaeli yawo ali ngati mbelele izo zasowa. 7 Pitani mkalalikile wandhu Uthenga uwu, ‘Ufumu wa kumwamba wawandikila.’ 8 Mwaalamiche odwala, ahyucheni akufa, alamicheni a makate, chochani viwanda. Anyiimwe mwapachidwa chajhe, chochani chajhe. 9 Msatenga zahabu mmatumba yanu, kapina siliva, kapina gelenjha za shaba. 10 Msadatenga thumba lakupembhela ndalama mnjila, kapina vivalo viwili, kapina malapasi, wala mpulu. Pakuti uyo wachita njhito wafunika wapachidwe mkokolo wake."

11 "Mkalowa mmujhi uliwonjhe kapina chijhijhi chalichonjhe, mfuneni mundhu uyo wakhoza kukulandilani, khalani mnyumba imeneyo mbaka pajha simchokepo. 12 Yapo simulowe mnyumba, mwaalonjele wene khomo kwa kwambila mtendele ukhale namwe. 13 Wene khomo akakulandilani bwino, anyiiwo siakhale kwa mtendele. Nambho ngati siakulandilani, anyiimwe simkhale kwa mtendele. 14 Mundhu waliyonjhe wakakana kukulandilani kapina kukuvechelani, yapo simujhichoka, yakung'undheni malifumbi ya mmyendo mwanu kulangiza chizindikilo kuti akana kuulandila uthenga wa Mnungu. 15 Zene nikukambilani, pa siku la lamulo Mnungu siwalange kupunda wandhu ngati achameneo kupitilila wandhu mijhi ya sodoma ni Gomola."

Mavuto yayo yakujha

16 "Vechelani, ine nikutumani anyiimwe ngati mbelele pakati pa mibinji. Mkhale ochenjela ngati njoka, ni apole ngati nghunda. 17 Mkhale maso ni wandhu sakuchucheni, chimwecho sakugwileni ni kukupelekani kunyumba ya milandu ni kukubulani mnyumba yokomanilana Ayahudi. 18 Simupelekedwe kwa alamuli ni afumu ndande ya ine, dala mwaalalikile Uthenga Wabwino kwa anyiiwo ni kwa wandhu yao osati Ayahudi. 19 Yapo sakupelekeni kubwalo la milandu, msadakhala ni mandha kuti simukambe chiyani, pakuti simupachidwe chokamba ndhawi imeneyo. 20 Pakuti osati anyiimwe mukamba, nambho Mzimu Woyela wa Mnungu siukambe kupitila anyiimwe."

21 "Mbale siwamnga'namuke mbale wake kuti wphedwe, ni tate siwamung'anamuke mwana wake, wana nawo siwang'anamuke obala wao ni kwa wapha. 22 Wandhu wonjhe siakuipileni ndande ya kunikhulupilila ine. Nambho yujha siwalimbe mtima mbaka pothela, ndeuyo siwalamichidwe. 23 Wandhu akakuvutichani pamujhi thawilani mujhi wina. Zene nikukambilani, simumaliza njhito yanu mmijhi yonjhe ya Izilaeli popande Mwana wa Mundhu kujha."

24 "Palibe oyaluzidwa uyo wakhala wamkulu kupitilila oyaluza wake, kapina kapolo uyo wakhoza kukhala wamkulu kumpitilila mbuye wake. 25 Mundhu wayaluzidwa wafunika wakhale ngati oyaluza wake, ni kapolo wakhale ngati ambuye wake. Ngati wamkulu wa nyumba amamtana Belizebuli, bwanji, wandhu amnyumba mwake siatanidwa mayina yoipa kupunda?"

Yani wa kumuopa

26 "Chimwecho, msadaaopa wandhu. Abisa vindhu achichita, nambho kuli ndhawi ikujha wandhu saone ivo avibisa ni kila mundhu siwajhiwe visisi vao. 27 Yajha nakukambilani yapo tidali tekha, anyiimwe mkambileni kila mundhu, ni yajha nakukambilani konong'ona anyiimwe mkambileni kila mundhu. 28 Msadaopa yawo akhoza kukuphani anyiimwe, nambho sakhoza kuyomwecha mizimu yanu. Nambho muopeni yujha wakhoza kuyomwecha thupi pamojhi ni mzimu mumoto wa muyaya. 29 Bwanji, njhete ziwili zigulichidwa kwa senti imojhi? Nambho palibe ata imojhi iyo ikufa popande Atate wanu akumwamba kujhiwa. 30 Nambho anyiimwe, ata chichi la mmitu yanu lawelengedwa lonjhe. 31 Chimwecho msadaopa, anyiimwe amate kupunda kupitilila mbalame!"

Kumvomela ni kumkana Yesu

32 "Mundhu waliyonjhe uyo siwavomele pachogolo pa wandhu kuti iye ni wanga, ine nane sinimvomele pamaso pa Atate wanga yawo ali ku mwamba. 33 Nambho mundhu waliyonjhe uyo siwanikane pachogolo pa wandhu, ine nane sinimkane pamaso pa Atate wanga aku mwamba."

Sinidapeleke mtendele nambho upanga

34 "Msadaganiza kuti najha kwaachita wandhu akhale kwa mtendele pajhiko. Notho. Sinidajhe kwaachita wandhu akhale kwa mtendele, nambho najha kupeleka upanga. 35 Pakuti najha kwaachita ayambane mnyamata ni atate wake, mwali ni maye wake, mpongozi wamkazi ni mpongozi wake, 36 ni adani a mundhu ni wandhu wajha ali mnyumba mwake."

37 "Mundhu waliyonjhe uyo waakonda atate wake kapina amaye wake kupitilila ine, mmeneyo siwakhoza kukhala oyaluzidwa wanga. Ni mundhu waliyonjhe waakonda anamwali wake kapina wana wake waachimuna kupitilila ine, mmeneyo siwakhoza kukhala oyaluzidwa wanga. 38 Mundhu uyo siwavomela kuvutika ni kunichata ine, mmeneyo siwakhoza kukhala oyaluzidwa wanga. 39 Mundhu waliyonjhe uyo siwaulonde umoyo wake siwausoweze, nambho waliyonjhe uyo wausoweza umoyo wake ndande ya ine, siwaupate umoyo wa muyaya."

Chikho

40 "Mundhu waliyonjhe uyo wakulandilani anyiimwe kukhomo lake, wanilandila ine ni mundhu uyo wanilandila ine, wamlandila yujha wanituma. 41 Mundhu waliyonjhe uyo wamulandila mlosi ndande ni mlosi, siwalandile chikho cha ulosi. Mundhu waliyonjhe uyo wamlandila mundhu wabwino ndande ni mundhu wabwino, siwalandile chikho cha kukhala mundhu wabwino. 42 Nikukambilani uzene, mundhu waliyonjhe uyo siwampache mmojhi wa oyaluzidwa yawa chikho cha majhi yozizila ndande yakukhala oyaluzidwa wanga, zenedi siwapate chikho chake."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-