1 Pambuyo pa masiku yambili kupita Yohana Mbatizi wadajha ni kuyamba kulalikila wandhu kuphululu la kujhiko la Yudea niwakamba, 2 "Lapani pakuti ufumu wa kumwamba wawandikila!" 3 Uyu nde Yohana yujha nghani zake zidakambidwa ni mlosi Isaya kuti,
"Mundhu watana ku phululu,
‘Akonjeleni Ambuye njila yao
tambasulani njila yake!’"
4 Yohana wadavala njhalu izo zidakonjedwa ni mabweya ya ngamila ni lamba la chikwetu mchiuno mwake. Chakudya chake chidali nzige ni uchi wa mthengo. 5 Wandhu adafika kwa iye kuchokela kumujhi wa Yelusalemu ni kuchokela madela yonjhe ya kujhiko la Yudea ni mbhepete mwa mchinje Yolodani. 6 Adayavomela machimo yawo ni kuyasiya ni kuwabatiza pa mchinje Yolodani.
7 Yohana yapo adaona Afalisayo ni Masadukayo ambili amjhela kuti abatize. Wadaakambila kuti, "Imwe mbadwa wa njoka yani wakukambilani kuti mukhoza kukwepa chilango chikujha? 8 Mchite vichito vijha vilangiza kuti mwayasiya machimo yanu. 9 Msadaganiza ni kujhikambila kuti, Ibulahimu nde tate wanu. Zene nikukambilani kuti, Mnungu wakhoza kumpacha wana Ibulahimu kupitila myala iyi. 10 Basi nghwangwa yathoikidwa kudula mizo. Chimwecho mtengo uliwonjhe uwo suubala vipacho vabwino suudulidwe ni kutayidwa pamoto. 11 Ine nikubatizani kwa majhi kulangiza kuti mwayasiya machimo yanu. Nambho uyo wakujha mmbuyo mwanga wali ni mbhamvu kupitilila ine. Ine sinifunika kutenga vingwe va malapasi yake. Iye siwakubatizeni kwa Mzimu Woyela ni moto. 12 Mmanja mwake wagwila liselo lopetela. Nayo siwaeleche pamalo pake popetela ngano. Siwazikuse nikukusa ngano ni kuziika mnghokwe ni kupyeleza nghupete mmoto uwo siuthima."
13 Ndhawi imeneyo Yesu wadachoka ku Galilaya ni kufika ku mchinje Yolodani kuti Yohana wambatize. 14 Nambho Yohana wamafuna kumchekeleza Yesu niwakamba, "Ine nifuna nibatizidwe ni iwe. Ndandeyanji ukujha kwa ine nikubatize?"
15 Nambho Yesu wadayangha, "Siya ikhale chimwecho kwa ndhawi ino. Pakuti pakuchita chimwecho tiyachita yonjhe yayo wayafuna Mnungu." Ndiipo Yohana wadavomela kumbatiza Yesu.
16 Pampajha, Yesu yapo wadamaliza kubatizidwa wadachuuka mmajhi. Kumwamba kudamasuka ni wadaona Mzimu wa Mnungu niuchika ngati nghunda ni kutula pamwamba pake. 17 Mwachizulumukila mvekelo kuchokela kumwamba udaveka, "Uyu nde Mwana wanga wokondedwa uyo nikondwela nayo."