1 Yesu ni oyaluzidwa wake yapo adafika ku Yelusalemu, ku vijhijhi va Besifage ni ku Besania, pafupi ni phili la Mizeituni, wadaatuma oyaluzidwa wake awili amchogolele. 2 Wadaakambila, "Pitani kukijhijhi chili pachogolo panu. Yapo simmalowe mmenemo, simpheze mwana wa phunda, uyo siwadatumike ni mundhu waliyonjhe. Mmasuleni ni mjhenayo. 3 Ngati mundhu wakakufunjhani ndande yanji mummasula, myangheni kuti Ambuye atomfuna ni sambweze chipanoyapa."
4 Anyiwajha oyaluzidwa adachoka, ni adampheza mwana wa phunda wamangidwa pafupi ni pakhomo la nyumba, mbhepete mwa njila. Yapo amammasula, 5 wandhu wina yawo adali pamenepo, adaafunjha, "Mchita chiyani? Ndande yanji mummasula mwana wa phundayo?" 6 Oyaluzidwa wajha adayangha ngati umo Yesu wadaakambila, ni wandhu achamenewo adaasiya apitenayo. 7 Adampeleka yujha mwana phunda kwa Yesu. Adayala njhalu zao pamsana pa yujha mwana punda, ni Yesu wadakwela pamsana ni kukhala. 8 Wandhu ambili adayala njhalu zao mnjila, ni wina adadula ndhawi zazing'onozing'ono za mitengo adaziyala mnjila ndande ya kumlemekeza Yesu. 9 Wandhu wonjhe adamchogolela ni anyiwajha amamchata mmbuyo, adakweza mvekelo niakamba, "Mtamandeni Mnungu! Wapachidwe mwawi uyo wakujha kwa jhina la Ambuye! 10 Mnungu waupache mwawi Ufumu uwo ukujha wa atate wathu mfumu Daudi. Watamandidwe Mnungu uyo wali kumwamba kupunda."
11 Yesu wadalowa kumujhi wa ku Yelusalemu ni kupita mbaka kunyumba ya Mnungu, wadapenyechecha kila chindhu. Nambho, ndande jhuwa lidabila, wadapita ku Besania pamojhi ni anyiwajha oyaluzidwa wake khumi ni awili.
12 Umawa wake yapo amachoka ku Besania kupita ku Yelusalemu, Yesu wadali ni njala. 13 Wadauona mtengo wa mtini kwa patali, uwo udali ni machamba yambili. Wadauchata kuti wapenye ngati wakhoza kupheza chipacho chalichonjhe. Nambho yapo wadauwandikila, wadauona ulibe chipacho chalichonjhe, nambho udali ni machamba yokha, pakuti nyengo ya yobala vipacho idali ikali. 14 Yesu wadaukambila ujha mtengo wa mtini, "Kuyambila lelo mbaka muyaya, siubalanjho." Ni oyaluzidwa wake adamvela yapo wadakamba chimwecho.
15 Ndiipo, adafika ku Yelusalemu, Yesu wadafika panyumba ya Mnungu, wadayamba kwatopola kubwalo wandhu yawo amagulicha ni kugula vindhu pamenepo. Wadagadabula meza zaanyiwajha amang'anamucha ndalama, ni mipando ya anyiwajha amagulicha nghunda. 16 Nisiwadamlole mundhu waliyonjhe watenge chindhu chalichonjhe kuchoka panyumba ya Mnungu. 17 Ndiipo wadaayaluza, "Bwanji, siidalembedwe mmalemba yoyela, kuti, ‘Nyumba yanga siikhale malo ya mapembhelo ya wandhu amaiko yonjhe?’ Nambho anyiimwe mwaichita kukhala mbhanga ya anghungu."
18 Waakuluakulu wa ajhukulu ni oyaluza thauko yapo adavela yameneyo, adayamba kufunafuna njila ya kumpha Yesu. Nambho amamuopa, ndande ya gulu la wandhu wonjhe lidazizwa ni mayaluzo yake. 19 Yapo ujhulo udajha, Yesu ni ochatila wake adachoka mujhi wa ku Yelusalemu.
20 Umawamawa, yapo amapita, adauwona ujha mtengo wa mtini wauma wonjhe. 21 Petulo wadakumbukila icho wadakamba Yesu, wadamkambila, "Oyaluza penyani, ujha mtengo wamtini mdauleswa, wauma"
22 Yesu wadamkambila, "Mkhulupilileni Mnungu. 23 Nikukambilani uzene, mundhu waliyonjhe wakalikambila phili ili kuti lipite likajivyale mnyanja ya mchele, popande kukhaikila mumtima mwake, nambho wakakhulupilia kuti chindhu icho wachikamba sichichokele, ni Mnungu siwamchitile. 24 Chipano nikukambilani, yapo msali ni kupembha chindhu, khulupililani kuti mwachilandila, nianyiimwe simchipate. 25 Ni yapo mpembhela, mlekelelane, kila mundhu wamlekelele mnjake uyo wamlakwila, ni Atate wanu ali kumwamba siakulekeleleni anyiimwe volakwa vanu. 26 Nambho ngati simwalekelela wina, ni Atate wanu ali kumwamba siakulekelelani anyiimwe volakwa vanu."
27 Ndiipo, adafikanjho ku Yelusalemu. Yesu yapo wamaenda panyumba ya Mnungu, waakulu akulu wa ajhukulu, ni oyaluza thauko ni azee adamchata, 28 adamfunjha, "Bwanji, uchita yaya kwa ulamulilo wa yani? Yani wakupacha ulamulilo wochita vindhu ivi?"
29 Yesu wadaayangha, "Nikufunjheni funjho limojhi, mkaniyangha, ni ine sinikukambileni nichita yaya kwa ulamulilo wa yani. 30 Nikambileni, ulamulilo wo batiza wa Yohana udachokela kuti, kwa Mnungu kapina kwa wandhu?"
31 Adayamba kukambilana, "Tikakamba, ‘Ulamulilo wake wobatiza wachoka kwa Mnungu,’ hiwatifunjhe, ‘Ndande yanji sidamkhulupilile.’ 32 Nambho tikakamba kuti, ‘Ulamulilo wake Wachoka kwa wandhu,’ wandhuwo saipile." Amaopa gulu la wandhu, pakuti wandhu wonjhe adajhiwa kuti Yohana wadali mlosi. 33 Basi adayangha, "Ife sitijhiwa." Naye Yesu wadaakambila "Niine sinikukambilani kuti nichita yaya kwa ulamulilo wanji."