1 Ndiipo Yesu wadachoka ku Kapelinaumu ni kupita ku mujhi wa Yudeya, ni kuyomboka mchinje Yolodani. Gulu la wandhu lidamchatanjho, niiiye wadaayaluza ngati umo idali kalidwe chake.
2 Afalisayo akumojhi adamchata, ni adamfunjha kwa kumuyesa, "Bwanji, thauko lathu litilola wamuna kumsiya mkazake?" 3 Yesu wadaafunjha, "Bwanji, Musa wadakulamulani chiyani?" 4 Anyiiwo adamuyahga, "Musa wadaagiza wammuna wakhoza kulemba talaka ni kumsiya wamkazi."
5 Yesu wadaakambila, "Musa wadakulembelani lamulo limenelo ndande simuyaluzika. 6 Nambho, kuyambila kuumbidwa kwa jhiko, Mnungu wadaumba wamuna ni wamkazi. 7 Chimwecho, wamuna siwasiye atate wake ni amake ni kulunjana ni mkazake, 8 ni anyiiwo awili sakhale thupi limojhi. Chipano anyiiwo osati awilinjho, nambho ni thupi limojhi. 9 Chimwecho, icho wachilunjanicha Mnungu, mundhu siwadachisiyanicha."
10 Yapo adabwelanjho mnyumba, oyaluzidwa adamfunjha Yesu kuusu chindhu chimenecho cho siyana. 11 Yesu wadaakambila, "Wammuna waliyonjhe uyo wamsiya wamkazi ni kukwata mwina, wamchitila chigololo mkazake. 12 Chinchijha, wamkazi wakamsiya mmunake ni kupita kukwatiwa ni wammuna mwina, wamchitila chigololo mmunake."
13 Wandhu wina adampelekela Yesu wana wang'onoang'ono waikile manja kuti wapache mwawi, nambho oyaluzidwa wake adaakaniza. 14 Yesu yapo wadaona chimwecho, wadakwiya ni kwaakambila, "Asiyeni wana waang'onoang'ono ajhe kwanga, ni simdachelekeza, ndande wandhu ali ngati wana anyiiawa nde sialowe muufumu wa Mnungu. 15 Zenedi nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo siwaulandila Ufumu wa Mnungu ngati wana wang'onoang'ono umo aulandilila, siwalowelatu muufumu wa Mnungu." 16 Ndiipo wadakhumbatila wana achameneo, ni kwaikila manja, ni kwaapacha mwawi.
17 Yesu yapo wamachoka, mundhu mmojhi wadamthamangila ni kumgwadila, wadamfunjha, "Oyaluza wabwino, nichite chiyani niupate umoyo wa muyaya?" 18 Yesu wadamfunjha "Ndande yanji unitana wabwino? Palibe mundhu wali wabwino, nambho Mnungu yokha. 19 Ulijhiwa thauko la musa, ‘Siudapha, siudachita chigololo, siudaba, siudachocha umboni wa unami, siudanyenga, walemekeze amako ni atate wako.’"
20 Mundhu mmeneyo wadayangha, "Oyaluza, thauko limenelo lonjhe nazichata kuyambila kuubwana wanga."
21 Yesu wadampenya ni wadamkonda, ni wadamkambila, "Wachepekeledwa ni chindhu chimojhi, pita ukaguliche kila chindhu ulinacho, ni ndalama izo siupate waapache wosauka, niiwe siukhale ni wopata kumwamba, ndiipo majha unichate." 22 Mundhu mmeneyo yapo wadavela chimwecho, wadadandaula mumtima, wadachoka uku wali ni chisoni, pakuti wadali ni chuma chambili.
23 Yesu wadapenya konjhekonjhe, wadaakambila oyaluzidwa wake, "Siikhale kulimba kwa mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa Mnungu!" 24 Oyaluzidwa wake adazizwa kupunda yapo adavela nghani zimenezo. Yesu wadaakambilanjho, "Anyabwenjilanga, ilimba kupunda kwa mundhu, kulowa mu Ufumu wa Mnungu. 25 Siikhale lahisi kwa nyama iyo itanidwa ngamila kulowa pa ndhoolo ya sindano, nambho osati wopata kulowa mu Ufumu wa Mnungu." 26 Oyaluzidwa wake adazizwa kupunda, adafunjhana, "Niyani basi uyo siwakhoze kuomboledwa?" 27 Yesu wadaapenyechecha ni kwaakambila, "Kwa mundhu siikhozekana, nambho kwa Mnungu ikhozekana, pakuti kila kandhu kwa Mnungu chikhozekana."
28 Petulo wadamkambila, "Ife tasiya kilakandhu takuchata iwe." 29 Yesu wadakamba, "Zenedi nikukambiulani, kila mundhu uyo waisiya wandhu amnyumba yake, kapina mbale wake, kapina mlongo wake, kapina maye wake, kapina atate wake, kapina wana wake kapina minda yake ndande yaine ni ndande ya Uthenga Wabwino, 30 siwalandile vindhu vochuluka pa ndhawi ya saino. Siwalandile nyumba, abale, alongo, maye, wana ni minda ni mavuto, ni masiku yayo yakujha siwalandile umoyo wa muyaya. 31 Nambho, yawo achogolela siakhale kumbuyo, ni akumbuyo siachogolele."
32 Yesu ni oyaluzidwa wake, adali mnjila amakwela kupita kumujhi wa Yelusalulemu, ni Yesu wadatowachogolela. Oyaluzidwa wake adazizwa, ni wandhu wonjhe yawo amamchata adaopa. Yesu wadaatenga oyaluzidwa wake khumi ni awilil kumbhepete, wadayamba kwakambila yajha siyampheze, 33 Yesu wadaakambila, "Vechelani, tipita ku Yelusalemu, nikumeneko Ine Mwana wa Mundhu siniikidwe mmanja mwa akuluakulu wa ajhukulu ni oyaluza thauko, ni anyiiwo siamlamule waphedwe ni kupachidwa kwa wandhu yawo osati Ayahudi. 34 Ni anyiiwo sianipepule, ni kunilavulila malovu, siambule mikwapulo ni kumpha. Nambho siku la katatu siwahyuke."
35 Ndiipo Yohana ni Yakobo, wana wa Zebadayo, adamchata Yesu nikumkambila, "Oyaluza, kuli chindhu tifuna mtichitile." 36 Yesu wadaafunjha, "Mfuna nikuchitileni chiyani?" 37 Adamuyangha, "Yapo simkhale pampando wanu wachifumu pa ulemelelo wanu, tipembha mmojhi wakhale bendeka lanu la kumanjele, ni mwina bendeka lanu la kwene." 38 Yesu wadaayangha, "Simjhiwa icho mpembha! Bwanji, simkhoze kuvutika ngati umo sinivutikile ine, kapina kuphedwa ngati umo siniphedwele ine?" 39 Adamuyangha, "Tikhoza." Yesu wadaakambila, "Zenedi, simvutike ngati umo sinivutikile ine, ni simufe ngati umo sinifele ine. 40 Nambho ni yani uyo siwakhale kwene ni kumanjele kwanga, osati njhito yaine, ni malo yameneyo siakhale yawo asanghidwa ni Mnungu."
41 Wajha oyaluzidwa wina khumi yapo adavela chijha adapembha Yakobo ni Yohana, adaakwiila. 42 Chimwecho, Yesu wadaatana, wadaakambila, "Mjhiwa kuti anyiwajha aoneka kuti ni alamuli a wandhu anyiyawo osati Ayahudi, walamula wandhu kwa mbhavu, kuti wandhu wao avele. 43 Nambho kwa anyiimwe siidakhala chimwecho, mundhu waliyonjhe uyo wafuna wakhale wamkulu, ifunika wakhale mbowa wa wonjhe. 44 Mundhu waliyonjhe uyo wafuna kukhala wamkulu, ifunika wajhatumikila wonjhe. 45 Ata, ine Mwana wa Mundhu sinidajhe kutumikilidwa, nambho kutumukila, ni kuchocha umoyo wanga kwa kwaombola wandhu ambili."
46 Ndiipo, adafika ku Yeliko. Yesu ni oyaluzidwa wake pamojhi ni gulu lalikulu la wandhu, adampheza mundhu mmojhi wosapenya, uyo wamatanidwa Batimayo, mwana wa Timayo, wakhala pambhepete pa njila niwapembha pembha vindhu. 47 Batimayo yapo wadavela kuti Yesu wa ku Nazaleti wamapita pamalo yameneyo, wadakweza mvekelo wake, niwakamba, "Imwe a Yesu, Mwana wa Daudi nilengeleni lisungu!" 48 Wandhu ambili adamnyindila, adamkambila wakhale chete, nambho iye wadapunda kukweza mvekelo, "Imwe Mwana wa Daudi, nilengeleni lisungu"
49 Yesu wadaima, ni kukamba "Mkambileni wajhe." Ndiipo adamtana, adamkambila, "Jhipache mtima, ima watokutana." 50 Niiye wadataya kutali njhalu yake, wadalumbha ni kumpitila Yesu.
51 Yesu wadamfunjha, "Ufuna nikuchitile chiyani?" Sapenya yujha wadamuyangha, "Oyaluza, nipemhba nipenye."
52 Yesu wadamkambila, "Pita, kukhulupilila kwako kwakulamicha." Pampajha, yujha sapenya wadakhoza kupenya, ndiipo wadamchata Yesu mnjila.