1 Ndiipo bwalo lonjhe lidaima ni kumpeleka Yesu kwa Pilato. 2 Adayamba kumnamizila milandu pokamba, "Mundhu uyu tamuona niwanyenga wandhu ajhiko lathu, wakaniza wandhu kuti asamapeleka malipilo kwa mfumu wa ku Loma ni kujhichita iye kuti Kilisito Mfumu" 3 Ndiipo Pilato wadamfunjha Yesu, "Eti iwe ni Mfumu wa Ayahudi?" Yesu wadamuyangha Pilato, "Iwe umwene nde wakamba." 4 Pilato wadakambila wakuluakulu ajhukulu ni gulu lonjhe lidali pamenepo, "Palibe cholakwa icho nichiona kwa mundhu uyu." 5 Nambho anyiiwo adachimikiza kukamba, "Mayaluzo yake yachita wandhu apanduke mu Yudea yonjhe. Wadayambila ku Galilaya ni chipano wali pano pa Yelusalemu."
6 Pilato yapo wadavela chimwecho, wadafunjha funjho, "Bwanji, mundhu uyu ni waku Galilaya?" 7 Yapo wadajhiwa kuti Yesu wadali wajhiko ilo wamalamulila Helode, wadampeleka kwa Helode, nayo uyo wadali ku Yelusalemu ndhawi imeneyo.
8 Helode wadakondwa kupunda yapo wadamuona Yesu. Kuyambila kale wadakhumbila kupunda kumuona Yesu ndande wadavela nghani zake. Iye Helode wamalindilila kumuona Yesu uku niwachita vodabwicha. 9 Helode wadamfunjha Yesu mafunjho yambili, yayo Yesu siwadayanghepo ata limojhi. 10 Ajhukulu wakuluakulu ni oyaluza thauko anyiawo adali adamnamizila mawu ya mbili Yesu. 11 Ndiipo Helode ni asikali wake adamkwiicha Yesu kwa kumtukwana. Adamveka chovala cha chifumu, ni kumbweza kwa Pilato. 12 Siku limenelo Helode ni Pilato adakhala mabwenji nambho kuyambila poyamba adali adani.
13 Ndiipo Pilato wadasonghanicha wakuluakulu wa ajhukulu ni wandhu yawo adali pajha, 14 wadakamba, "Mwampeleka mundhu uyu pano kumpacha mlandu, kuti wakwinjizila wandhu apanduke. Chipano vechelani, namfunjha pamaso panu ni naona kuti palibe cholakwa chilichonjhe cha kumuika mundhu uyu mmilandu. 15 Osati inepe, ata Helode siwadaone kulakwa kulikonjhe, chimwecho walamula wambweze kwathu. Zenedi mundhu uyu siwadachite chindhu chilichonjhe chomchita walamulidwe kuphedwa. 16 Chimwecho, sinimlange kumbula mikwapulo, alafu sinimsiilile." 17 Pakuti chidali chikhalidwe pasiku la pwando la Pasaka Pilato kwamasulila wandhu wandende mmojhi.
18 Nambho wandhu wonjhe adayamba kukweza mvekelo kamojhi ni kukamba, "Waphedwe mundhu mmeneyo, tifuna umsiilile Balaba." 19 Balaba mmeneyo wadaikidwa mndende ndande kuchiticha wandhu kupanduka, mumujhi ni ndande ya kupha.
20 Pilato wamafuna kumlekelela Yesu, chimwecho wadakamba nawonjho, 21 nambho anyiiwo adayendekela kubula pokoso pokamba, "Wapachikidwe! Wapachikidwe!" 22 Pilato wadakambilanjho kakatatu, "Bwanji walakwa chiyani mundhu uyu? Ndande, siniona cholakwa chilichonjhe icho chimchita kuti wapedwe. Chimwecho, sinilamule wabulidwe mikwapulo, alafu sinimsiilile."
23 Nambho wandhu adayendekela kukweza mvekelo waukulu kuti Yesu ifunika wapachikidwe pamtanda. Chimwecho, pothela mapokoso yao yadavomelezeka. 24 Chimwecho, Pilato wadalamula kuti vofuna vawo vikwanilichidwe. 25 Wadammasulila yujha mundhu wa mndende, uyo wadamangidwa ndande ya kupeleka kupanduka ni kupha wandhu. Uyo anyiiwo amafuna wamasulidwe, wadamchocha Yesu kwa anyiiwo kuti amchitile icho amachifuna.
26 Wajha anghondo Yapo amapita nayo Yesu, adakomana ni mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Simoni waku Kilene wamachoka kubwalo kwa mujhi. Adamgwila ni kumnyamulicha mtanda mmbuyo mwa Yesu. 27 Chiwelengo chochuluka cha wandhu chimamchata Yesu, adalimo ni wachikazi yawo amamlilila ni kumdandaulila. 28 Yesu wadang'anamukila ni kwakambila, "Anyiimwe Anyamaye aku Yeslusalemu, msadanililila ine, nambho mjililile mwachinawene wake ni wana wanu. 29 Pakuti nyengo itokujha iyo simukambe, ‘Ali ni mwawi wachikazi ambende, yawo siadabalepo ni mawele yake siyadayamwichepo!’ 30 Ndhawi imeneyo, wandhu sayakambile mapili, ‘Tigweleni,’ ni timapili, ‘Tivinikileni.’ 31 Pakuti ngati anichitila chimwechi ine sinidalakwe chalichonjhe, siamchitile chiyani mundhu walakwa?"
32 Kudali ni wandhu wina awili owananga adapita nao akaphedwe pamojhi ni Yesu. 33 Yapo adafika pamalo yapo patanidwa Fuvu la Mutu, kumalo kumeneko adampachika Yesu pamojhi ni wandhu wajha owananga. Mmojhi kwene ni mnjake kumanjele. 34 Yesu wadakamba, "Atate, mwalekelele wandhuwa, pakuti sajhiwa icho achichita." Ndiipo adagawana njhalu zake kwa kuchita gudugudu. 35 Wandhu adangoimilila pampajha naampenya. Ni achogoleli Ayahudi adamkwiicha Yesu pokamba, "Wadaombola wina! Chipano wajiombole mwene wake, ngatidi ni iye ni Kilisito, wosanghidwa ni Mnungu!" 36 Asikali nawo adaja, adamkwiicha, adampelekela divai yowawa, 37 Niayiiwo adamkambila, "Ngati zenedi iwe ni Fumu wa Ayahudi jhiombole umwene."
38 Chibao chidali pamwamba pa mtanda wake chidalembedwa chimwechi, UYU NDE FUMU WA AYAHUDI.
39 Mmojhi wa wajha owananga adapachikidwa mmitanda pamojhi ni Yesu wadamtukwana, niwakamba, "Bwanji, iwe sinde Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu? Jhiombole mwene utiombole ni ife." 40 Nambho owananga mnjake wadamnyindila, wadakamba, "Bwanji, iwe suopa Mnungu ata pang'ono? Pakuti iwe nawe wapachikidwa ngati iye. 41 Iwe ni ine tafunika yaya, ndande yaya nde mkokolo wa volakwa vathu. Nambho mundhu uyu siwadachite cholakwa chilichonjhe." 42 Ndiipo yujha owananga wadamkambila Yesu, "Imwe Ayesu! Mnikumbukile yapo simulowe mu Ufumu wanu." 43 Yesu wadamuyangha, "Nikukambila uzene, lelolino siukale pamojhi ni ine kumwamba."
44 Idali ngati saa sita usana, mdima udalivinikila jhiko lonjhe mbaka saa tisa, 45 pakuti jhuwa lidasiya kuwala, paziya la nyumba ya Mnungu lidang'ambika pakatikati kuyambila kumwanba mbaka panjhi. 46 Yesu wadakweza mvekelo, wadakamba, "Atate, mzimu wanga ni uika mmanja mwanu." Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, wadamwalila.
47 Yujha Wamkulu wa asikali yapo wadaona yayo yachokela, wadamtamanda Mnungu pokamba, "Zenedi mundhu uyu wadali wavomelezeka pachogolo pa Mnungu." 48 Gulu la wandhu yawo adakomana pajha dala apenye ivo vidachitika, adabwela kumakomo, uku ni adajhibulabula vidale vawo kwa chisoni. 49 Anyiwajha wonjhe yawo amamjhiwa pamojhi ni wachikazi wajha amamchata kuchokela ku Galilaya, adaima patali kupenya vindhu ivo vimachitika.
50 Padali mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Yusufu, iye wadali mmojhi wa wandhu a Bwalo lalikulu la Ayahudi, mundhu mmeneyo wadali wovomelezeka pachogolo pa Mnungu. 51 Iye siwamavomeleze ni malamulo ya bwalo ni vichito vao. Mundhu uyu wamachokela ku mujhi wa Alimataya ni wamaulindilila Ufumu wa Mnungu. 52 Ndiipo Yusufu wadapita kwa Pilato kumpembha kuti wapachidwe chitanda cha Yesu. 53 Iye wadalichicha chitanda cha Yesu kuchokela pajha pamtanda. Wadalivilingila sanda yoyela ya mtengo waukulu, ni kuliika chitanda mu manda ilo lidasepedwa pamwala waukulu, umo simdaikidwemo chitanda chilichonjhe. 54 Siku limenelo lidali siku lojhikonjekela, ndande idali kuyamba kwa siku lopumulila.
55 Wachikazi wajha adamchata Yesu kuchokela ku Galilaya, adamchata Yusufu, ni adapaona pamalo yapo chidazikidwa chitanda cha Yesu. 56 Ndiipo adapita kukhomo. Adakonjekela mafuta yo nunghila ni mafuta ya kuchinyeka chitanda cha yesu. Siku lopumulila adapumulila ngati umo idalamulidwa ni thauko.