1 Pambuyo pa yaya Yesu wadapita kumijhi ni ku vijhijhi kulalikila Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mnungu. Ni woyaluzidwa wake khumi ni awili wadachogozana naye. 2 Ni wachikazi wina adachochedwa viwanda, ni kwalamicha matenda yawo, adapiata pamojhi ni iye. Wachikaziwo adali, Maliya kuchokela ku Magedelena, uyo wadachochedwa viwanda saba, 3 Ni Yoane mkazake wa Kuza, wamkulu wa alonda wa nyumba ya Helode, Susana ni wina ambili. Wachikazi anyiyawa amamthangatila Yesu pamojhi ni oyaluzidwa wake kwa chuma chao achinawenewake.
4 Gulu lalikulu yapo lidajha kwa Yesu, kuchokela mmijhi yosiyanasiyana, amajha kwa Yesu. Ni iye wadayamba kukamba nao kwa chifani, 5 "Wovyala wadapita kumwaza mbeu zake kumunda. Yapo wamamijha mbeu zake, zina zidagwela mbhepete mwa njila, ni wandhu woyenda njila adaziponda ni kudyedwa ni mbalame. 6 Zina zidagwela pa dothi lidali pamwamba pa mwaala, yapo zidamela, zidafyota ndande idalibe chinyezi. 7 Zinjake zidagwela pa mitengo yaminga, minga izmenezo zidamela pamojhi ni mbewu zimenezo, nazo zidazengedwa zijha mbeu. 8 Mbeu zina zidagwela pa dothi la bwino, zidamela ni kubala kupunda zidali zambili mala mia kupitilila zijha vidavyalidwa."
Yesu yapo wadamaliza kukamba chimwecho, wadakweza mvekelo, "Mundhu waliyonjhe uyo wavela, wajhiwe!"
9 Woyaluzidwa wake adamfunjha Yesu mate ya mfano umeneo. 10 Iye wadayangha, "Anyiimwe mwapachidwa njelu ya kujhiwa chisisi cha ufumu wa Mnungu, nambho kwa winawo, osati chimwecho. Nambho kwa wandhu wina nikamba nao kwa chifani, kuti ata yapo apenya sadakhoza kuona, ni yapo avechela sadazindikila."
11 "Basi, mate ya chifani chimenecho nde iyi, mbeu ni mawu la Mnungu. 12 Mbeu zijha zigwela mnjila zilangiza wandhu yao avela mawu la Mnungu, ni Satana wakujha ni kuchocha mawu limelo mmitima mwawo kuti sadakhulupilila angaomboledwe. 13 Mbeu izo zidagwela padothi lijha lidali pamwamba pa myala, zilangiza wandhu yawo avela mawu la Mnungu ni kulilandila kwa chimwemwe. Nambho uthenga wa Mnungu siukhala mmtima mwao, ndande akhulupilila kwa ndhawi yochepa, ni yapo ayesedwa, agooka mtima. 14 Mbeu izo zidagwela pamitengo yaminga, zilangiza ni wandhu yawo avela mawu la Mnungu, nambho yapo ayendekela nalo azengedwa ni kukhaikila ni chuma ni machaucho ya ufulu wa umoyo wapajhiko. Wandhu achameneo sakhala kwa kuchata mawu la Mnungu. 15 Nambho mbeu izo zidwagwela padothi la bwino zilangiza wandhu yao avela mawu la Mnungu ni kulisunga mmitima mwawo monjhe. Wandhu achemenewo akhala kwa kuchata mawu la Mnungu."
16 "Wandhu sawasha nyali ni kuiika kunjhi kwa chithanda. Mmalo mwake, ayiika padanga kuti anyiyawo alowa mkati akhoze kuona dangalila."
17 "Chindhu chilichonjhe icho chabisidwa sichiikidwe padanga, ni icho chaikidwa pachisisi sichijhiwike ni kuikidwa padanga."
18 "Chimwecho, mkhale maso ni umo muvelela, pakuti uyo wali ni kandhu siwaonjezeledwe, nambho uyo walibe kandhu, siwalandidwe ata chaching'ono icho waganiza kuti walinacho."
19 Siku limojhi, amake a Yesu ni achabale adapita kumuona, nambho adalepela kuti akomane naye ndande ya kuchuluka kwa wandhu. 20 Mundhu mmojhi wadamkambila Yesu, "Amako ni achabale wako ali kubwalo, afuna kukuona." 21 Nambho Yesu wadakambila wandhu wonjhe, "Amanga ni achabale wanga ni anyiyawo avela mau yanga ni kuyagwila."
22 Siku limojhi Yesu wadakambila oyaluzidwa wake, "Tiyeni tiyomboke kuchija kwa nyanja." Chimwecho, adakwela bwato ni kuyamba kuyomboka. 23 Yapo adali mbwato, Yesu wadali ni litulo, wadagona. Mwela waukulu udayamba kuvunduka, ni majhi yadayamba kulowa mu bwato, ni anyiiwo adali pafupi kubila. 24 Woyaluzidwa wake adamchata Yesu ni kumuucha, naakamba, "Ambuye, Ambuye! Tilipafupi kubila!" Iye wadauka ni kuunyindila mwela ni mbhepo, ni mwela udasiya ni kudali mtendele. 25 Ndiipo Yesu wadafunjhaa oyaluzidwa wake, "Chikulupililo chanu chilikuti?"
Nambho anyiiwo adazizwa ni adagwilidwa ni mandha, ni kuyamba kufunjhana, "Uyu ni yani, mbaka wanyindila mwela ni mbhepo ni vonjhe vimvela."
26 Ndiipo, Yesu pamojhi ni oyaluzidwa wake adayomboka nyanja ya galilaya ni kufika kuchijya la jhiko la Agelasi. 27 Yapo wamachika mbwato, wadampeza mundhu mmojhi wa mujhi ujha uyo wadali ni viwanda. Mundhu mmeneyo masiku yonjhe siwavale njhalu siwamakale kukhomo wamakhala mmbhanga zozikila wandhu. 28 Yapo wadamuona Yesu, wadalila kwa mvekelo waukulu ni kujiponya panjhi pachogolo pa Yesu ni kukamba kwa mvekelo waukulu, "Iwe Yesu mwana wa Mnungu uli kumwamba kupunda ufuna kunichita chiyani? Nikupembha siudanivuticha!" 29 Pakuti Yesu wachilamula chijha chiwanda chimchoke mundhu yujha. Nyengo zambili chiwanda chijha chimatomchaucha nyengo zambili, wandhu amamchekela mnyumba ni kummanga minyolo mmyendo ni pingu mmanjha ni kumlonda. Nambho wamadula minyololo imeneyo ni pingu ni chiwanda chimenecho chimampeleka kupululu. 30 Yesu wadamfunjha, "Jhina lako yani?" Iye wadayangha, "Ife tili ambili." Iye wadayangha chimwecho ndandeyake wadali ni viwanda vochuluka. 31 Viwanda vimenevo vidampembha Yesu kwa mbili kuti siwadayalamula yapite kujhenje lalikulu.
32 Padali ni gulu lalikulu la nguluwe pafupi nianyiiwo ilo limadyela mphepete mwa phili. Viwanda vijha vidampembha Yesu kwambili kuti waviloleze vilowe mnguluwezo, ni Yesu wadaviloleza vilowe mnguluwe. 33 Viwanda vicha vidamchoka mundhu yujha ni kulowa mu nguluwe, ni gulu lonjhe la nguluwe lidachikilila kumunjhi ni kubila mnyanja ni kufa.
34 Wajha owesa yapo adaona yayo yadachokela adathawa, adapita kwakambila wandhu nghani izi mmijhi mwao ni mminda. 35 Wandhu adachoka kupita kuona yayo yadachokela. Yapo adafika yapo wadali Yesu, adamkomana mudhu uyo wadachochedwa viwanda, wakhala pafupi ni myendo ya Yesu, wavala njhalu ni wali ni njelu zake bwinobwino, wandhu wajha adaopa. 36 Wandhu yao adaona ivo vidachokela, wadafotokozela wandhu achameneo umo wadalamila mundhu yujha. 37 Ndiipo wandhu wonhje ni wandhu ambili mjhiko la Gelasi adagwilidwa ni mandha yayakulu. Chimwecho adampembha Yesu kuti wachoke, iye wadakwelanjho mbwato ni kuchoka. 38 Yesu yapo wamachoka, mundhu yujha wadachochedwa viwanda wadampembha Yesu kwambili kuti wachoke pamojhi ni iye, nambho Yesu wadamkambila, 39 "Bwela kukhomo ukafotokoze yonjhe yayo wakuchitila Mnungu." Mundhu yujha wadapita, niwauzila wandhu mmujhi wonjhe vindhu vavikulu ivo wachitilidwa ni Yesu.
40 Yesu yapo wadabwela kuchokela kuchija la a Gelasi wadalandilidwa kwa chimwemwe ndande amatomlindilila. 41 Pamenepo wadafika mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Yailo, uyo wadali mchogoleli wa nyumba yophezelana Ayahudi. Wadafika ni kugwada pa miyendo ya Yesu ni kumpembha wapite kukhomo kwake, 42 pakuti mwali wake wayokha wa vyaka ngati khumi ni viwili wadali kudwala pafupi kumwalila.
Yesu yapo wamapita gulu la wandhu amamzenga kupunda. 43 Basi pakati pa gulu la wandhu wajha, padali wamkazi mmojhi uyo wamasusa nghole kwa ndhawi ya vyaka khumi ni viwili, ingakhale wadathowananga chuma chake chonjhe icho wadalinacho kwa masing'anga, nambho palibe uyo wadakhoza kumlamicha. 44 Wamkazi yujha wadajha kumbuyo kwa Yesu ni kugafya njhonga ya chivalo chake, ndhawi imweyo nghole yake idasiya. 45 Yesu wadafunjha, "Yani uyo wanigafya ine?" Wandhu wonjhe adakana. Ni Petulo wadakamba, "Ambuye, ambili akuzungulilani ni kukuzengani!" 46 Nambho Yesu wadakamba, "Pali mundhu wanigafya, najhiwa ndande naona mbhavu zanga zanichoka." 47 Wamkazi yujha yapo wadaona kuti siwakoza kujibisanjho, wadatulukila uku niwatendhemela kwa mandha, wadagwa chifufumimba pamaso pa Yesu. Pamenepo wadafotokoza kwa wandhu wonjhe chifuko cha kumgafyila Yesu ni umo walamichidwila kwankamojhi. 48 Yesu wadamkambila, "Mwali, chikuluphililo chako chakulamicha. Pita kwa mtendele."
49 Yapo Yesu wadali wakali kukamba, wadafika mundhu mmojhi kuchokela kukhomo kwa mchogoleli yujha ni kumkambila Yailo, mchogoleli wa nyumba ya yokomanilana ayahudi, "Mwana wako wamkazi wamwalila, usadayendekela kumsaucha woyaluza." 50 Nambho Yesu yapo wadavela chimwecho wadamkambila Yailo, "Usadaopa, ungokhulupilila, mwali wako siwalame."
51 Yesu yapo wadafika kukhomo kwa Yailo, siwadamulole mundhu ata mmojhi kulowa nawo mnyumba mmenemo ingakale Petulo ni Yohana ni Yakobo ni obala amwali yujha. 52 Ndhawi imeneyo wandhu wonjhe amatolila ni kuimba zaya. Nambho Yesu wadakambila, "Msadalila, pakuti mwali uyu siwadafe, nambho wangogonape!" 53 Anyiiwo adamseka kwa kumdelela, pakuti adajhiwa kuti mwali yujha wamwalila. 54 Nambho Yesu wadamgwila janja mwali yujha ni kukamba, "Mwali, nyakuka!" 55 Umoyo wake udambwelela ni wadanyakuka ndhawi imweyo nikukalanjho wamoyo. Ni Yesu wadakambila obala wake kuti ampache chakudya. 56 Obala wake adazizwa kupunda, nambho Yesu wadalamula kuti asadamkambila mudhu waliyonjhe pa ivo vachokela.