1 Yesu wadakambila woyaluzidwa wake, "Vindhu ivo vimchiticha mundhu kuchita machimo sivichelezedwa. Nambho siwavutike mundhu yujha siwamchitiche mundhu wachite machimo. 2 Idakali bwino mundhu mmeneyo wadakamangidwa mbhelo yopelela mkhosi mwake ni kuponyedwa pakati panyanja, kusiyana ni kumchiticha mundhu mmojhi wakhulupilila wachite chimo. 3 Chimwecho jhipenyeleleni! Ngati mbale wako wakhulupilila wakachita machimo, mnyindile ni ngati walapa, mlekelele. 4 Ata ngati wakachimwa mala saba pa siku limohji nikujha kwako mala saba, wakakamba, ‘Nalapa,’ umlekelele."
5 Oyaluzidwa wake adamkambila Yesu, "Mtionjezele chikhulupi." 6 Yesu wadayangha, "Mdakakhala ni chikhulupi chaching'ono ngati mbeu ya haladali, mdakakhoza kuukambila mtengo wa mkuuyuwu, ‘Zuka upite ukamele mnyanja,’ ni iwo udakakuvelani."
7 Yesu wadakamba, "Ngati mmojhi wanu wali ni mbowa uyo walima kapina kudyecha mbelele. Bwanji, mbowayo yapo wabwela kuchoka kumunda, wopata yujha wamkambila mbowa wake wajhe chisanga kudya chakudya? 8 Bwanji, mmalo mwake siwamkambila, ‘Nikonjele chakudya nidye, ukonjeke kuti unitumikile yapo nikudya ni kumwa. Ndiipo pambuyo pake ukhoza kudya ni kumwa.’ 9 Bwanji, mundhu mmeneyo siwamuyamika mbowa mmeneyo ndande wachita chijha wadalamulidwa wachite? 10 Chimwecho, namwenjho mkathochita yonjhe yayo mulamulidwa, kambani, ‘Ife ni mbowa yawo tilibe phindu, tayachitape yayo talamulidwa kuchita.’ "
11 Yesu ni oyaluzidwa wake yapo wadali paulendo wopita ku Yelusalemu, wapitila malile ya Samaliya ni Galilaya. 12 Yapo wamapita mu chijhijhi chimojhi, wadakomana ni wandhu khumi adamjhela Yesu ni adaima patali. 13 Adakweza mvekelo, "Ambuye Yesu, tilengeleni lisungu!" 14 Yesu yapo wadaaona amakate wajha, wadaakambila, "Pitani mkajhilangize kwa ajhukulu." Yapo adali akali mnjila, adalama utenda ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlambila Mnungu. 15 Mmojhi wao yapo wadaona kuti walama, wadabwelela kwa Yesu uku niwamtamanda Mnungu kwa mvekelo waukulu. 16 Wadagwa chifufumimba mmiyendo ya Yesu ni kumuyamika. Mundhu mmeneyo wadali Msamaliya. 17 Yesu wadamfunjha, "Bwanji, osati wandhu khumi yao adalamichidwa ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlimbila Mnungu? Bwanji, anyiwajha tisa alikuti? 18 Bwanji, padalibe ata mmojhi uyo wadabwela kumpacha ulemu Mnungu, nambho uyu mlendope?" 19 Ndiipo Yesu wadamkambila mundhu yujha, "Ima ujhipita, chikhulupililo chako chakulamicha."
20 Siku limojhi Afalisayo adamfunjha Yesu kuti Ufumu wa Mnungu ukujha chakanji, iye wadayangha, "Ufumu wakumwamba siukujha kwa kuuona kwa maso. 21 Chimwecho, palibe mundhu uyo siwakhoze kukamba, ‘Uliyapa,’ kapina, ‘Uwo uliyapo.’ Pakuti Ufumu wa Mnungu uli mkati mwanu."
22 Ndiipo wadaakambila oyaluzidwa wake, "Masiku yatokujha yapo simukhumbile kuliona siku limojhi la masiku ya ine Mwana wa Mundhu, nambho simuliona. 23 Wandhu saakukambileni, ‘Uyo uko,’ kapina, ‘Uyu yapa!’ Nambho, msadaakhulupilila. 24 Pakuti siku limenelo, ine Mwana wa Mundhu sinionekele ngati dangalila umo liwalila kumwamba, kuyambila mathelo imojhi mbaka injake. 25 Poyamba ine Mwana wa Mundhu, nifunika niyambe kuvutika kupunda ni kukanidwa ni wandhu ambadwa uno."
26 "Ngati umo idali pa masiku ya Nuhu, nde umo siikhalile pa masiku ya kujha kwa ine Mwana wa Mundhu. 27 Pa masiku ya Nuhu, wandhu amadya ni kumwa, amakwata ni kukwatiwa mbaka siku lijha yapo Nuhu wadalowa mu chombo, kufulikila yapo mafuliko ya vula yayikulu yadachokela ni kuwapha wandhu ni vindhu vonjhe. 28 Idali chimwecho pa masiku ya Lutu. Wandhu amadya ni kumwa, amagula ni kugulicha, amalima ni kumanga nyumba. 29 Nambho siku limenelo Lutu yapo wadachoka ku Sodoma, udagwa moto wa chibeliti kuchokela kumwamba udamwazika ngati vula, ni kwaapha wonjhe. 30 Umu ndeumo siikhalile kwa ine Mwana wa Mundhu yapo sinichokele."
31 Wadaendekela kukamba, "Siku limenelo, mundhu uyo siwakhale pa chindu la nyumba siwadachika kutenga vindhu vake ivo wadavisiya mkati mwa nyumba. Chimwechonjho mundhu uyo wali kumunda siwadabwelela kukhomo kutenga chilichonjhe. 32 Kumbukilani vindhu vidampata mkazake wa Lutu! 33 Mundhu waliyonjhe uyo wafuna kuupulumucha umoyo wake siwautaye, ni mundhu waliyonjhe uyo siwautaye umoyo wake, siwauombole. 34 Nikukambilani chemwechi, usiku umeneo wandhu awili saagone pamojhi pachithanda, nambho mmojhi siwatengedwe ni mnjake siwalekedwe. 35 Wachikazi awili saakhale pamojhi kupela chakudya pa mbhelo, nambho mmojhi siwatengedwe ni mnjake siwalekedwe. 36 Wandhu awili saakhale pamojhi kulima munda, mmojhi siwatengedwe, ni mnjake siwalekedwe."
37 Pamenpo woyaluzidwa adamfunjha, "Ambuye, kuti uko siyachitike yaya?"
Wadayangha, "Yapo pali chitanda, ndeyapo sizisonghane nghwazi."