Publicidade

Lucas 13

Kulapa machimo

1 Nyengo imweyo, padali wandhu yawo adamkambila Yesu nghani za wandhu fulani kuchokela ku Galilaya, yawo Pilato wadalamula kuti aphedwe ni mwazi wao usingizidwe ni zinyama izo zachinjidwa ndande ya mahoka. 2 Nayo Yesu wadaayangha, "Bwanji, mganiza Agalilaya yawa adaphedwa adali olakwa kwapitilila Agalilaya wina, ndande adaphedwa nchimwecho? 3 Nikukambilani uzene, osati mchimwecho, anyimwe namwe, ngati simulapa machimo yanu simuyomwe ngati anyiiwo. 4 Kapina anyiwajha khumi ni nane adaphedwa yapo lidagwela phupha kujha ku Siloamu, mganiza anyiiwo adali amachimo kupitilila wandhu onjhe amakhala ku Yelusalemu? 5 Nikukambilani osati nchimwecho, nambho namwenjho ngati simulapa, simuyomwe ngati anyiiwo."

Chifani cha mtengo wa mtini uwo siubala

6 Ndiipo, Yesu wadakambila chifani ichi, "Padali ni mundhu mmojhi uyo wadali ni mtengo uwo umatanidwa mtini, udavyalidwa mmunda wake wa mizabibu. Mundhu mmeneyo wadapita kucha vipacho vake, nambho siwadapate ata chipacho chimojhi. 7 Ndiipo, wadamkambila wopenyelela munda wa mzabibu, ‘Vechela! Pavyaka vitatu chipano nakhala nikujha kufuna vipacho pamtini uwu, nambho sinipata. Udule! Ndande yanji mtengo umeneu uyendekele kutumila chayila popande phindu?’ 8 Namhho yujha wopenyelela munda wamzabibu wadamuyangha, ‘Ambuye, tiusiyenjho chaka chimojhi, niine siniuzunguchile jhenje nikuuthila chayila. 9 Ngati siubale vipacho pachaka, chabwino, ngati popande siubala, basi udaudule.’ "

Yesu wamulamicha wamkazi siku Lopumulila Ayahudi

10 Siku limojhi Lopumulila, Yesu wamatoyaluza mnyumba yopembhelela Ayahudi. 11 Mnyumba mmenemo mudali wamkazi mmojhi uyo wamalamulidwa nichiwanda pavyaka khumi ni nane. Nayo wadali nichipindi, nisiwamakhoze kuima. 12 Yesu yapowadamwona wamakazi mmeneyo, wadamtana, ni wadamkambila, "Wamkazi, wamasulidwa chipindi chako." 13 Yesu yapo wadamwikila manja pamwamba pa mutu wake kwa kughafya, ghafula thupi lake lidakhululukanjho, wadayamba kumtamanda Mnungu. 14 Nambho wamkulu wa nyumba ya mapembhelo wadakwiya ndande Yesu wadamlamicha wamkaziyo siku lo pumulila. Nde wamkulu wa nyumba yopezelana ayahudi wadakambila wajha wandhu, "Mulinisiku sita izo mfunika kuchita njhito. Chipano, mjhijha pasiku zimenezo kulamichidwa, nambho osati siku Lopumulila." 15 Ndiipo Yesu wadayangha, "Aghunguli anyimwe! Bwanji, palije uyo wamasulila punda kapina ng'ombe wake kuchokela mkhola nikupita nayo kumwechela majhi ata ngati siku Lopumulila? 16 Ni uyu wamkazi uyu, uyo wali mbadwa wa Ibulahimu, wavutichidwa ni Satana kwa vyaka kumi ni nane. Bwanji, siwafunika kulamichidwa ata ngati siku Lopumulila?" 17 Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, adani wonjhe wake adalenga mwano, nambho wandhu adakondwa kupunda ndande ya vodabwicha ivo wadachita Yesu.

Chifani cha mbeu yaying'ono ya mtengo uwo utanidwa haladali

18 Ndiipo Yesu wadafunjha, "Ufumu wa kumwamba ulingana ni chiyani? Siniulinganiche nichiyani? 19 Uli ngati mbeu yaing'ono ya mtengo uwo utanidwa haladali iyo wadaivyala mundhu mmojhi mumunda mwake. Idamela ni kukula ni kukhala mtengo waukulu, ni mbalame za kumlengalenga zidamanga visa vao mndhawi zake."

Mfano wa amila

20 Yesu wadafunjhanjho, "Ufumu wa Mnungu siniulinganiche ni chiyani? 21 Ulingati amila iyo wadatenga maye mmojhi ni wadasingizana ni ufa madebe yatatu, ndipo ufa wonjhe udatutumuka."

Khomo lowonda

22 Yesu wadayendekela ni ulendo wake kupita ku Yelusalemu, uku ni walalikila wandhu mmijhi ni vijhijhi. 23 Mundhu mmoji wadamfunjha Yesu, "Oyaluza, wandhu wochepa ndeyawo yawo saomboke?" 24 Yesu wadamuyangha, "Limbikilani kulowa pachicheko chowonda, zenedi nikuchimikizilani kuti wandhu ambili sayese kulowa kupitila chicheko chimenecho chowonda, nambho sakhoza. 25 Siifike ndhawi iyo mwene nyumba siwauke ni kucheka chicheko, simuime kubwalo ni kuodila nimkamba, ‘Ambuye, umtichekulile chicheko.’ Nambho iye siwakuyangheni, ‘Sinikujhiwani ni sinijhiwa uko mchokela.’ 26 Namwenjho simuyambe kukamba, ‘Ife nde yawo tidadya ni kumwa pamoji ni imwe, ni imwe mudatiyaluza mmikwakwa yatu.’ 27 Nambho iye siwakambe, ‘Sinikujhiwani uko mwachokela, chokani pachogolo panga mwaonjhe yawo muchita voipa!’ 28 Ndiipo kumeneko sikukhale chililo ni kukuta mano, yapo simwaone Ibulahimu, Isaka ni Yakobo ni alosi onjhe ali mu ufumu wa Mnungu, nambho mwachinawene wake simtaidwe kubwalo! 29 Wandhu siajhe kuchokela madela yonjhe ya jhiko, naachokela kunyanja mpaka kuphili, ni kuchokela kumpoto mbaka kunyanja, Mnungu sachite pwando ni Mnungu siwakulamule. 30 Zenedi nikukambilani, wajha ali wothela sakale woyamba, ni yawo ali woyamba sakhale wothela."

Yesu waulilila mujhi wa Yelusalemu

31 Ndhawi imweyo Afalisayo mmojhi ni wandhu wina adamchata Yesu ni kumkambila, "Uchoke pano ni upite kumalo kwina chifuko Helode wafuna kukupha."

32 Yesu wadayangha, "Pitani mkambile nghandweyo, ‘Ine nitulucha viwanda ni kulamicha odwala lelo ni mawa, ni siku lakatatu sinimalize njhito yanga.’ 33 Nambho, nifunika kuyendekela ni ulendo wanga lelo, mawa ni mkucha, pakuti palibe mlosi wakoza kumwalila kubwalo kwa mujhi wa yelusalemu."

34 "Iwe Yelusalemu! Iwe Yelusalemu! Utokupha alosi pakwamenya miyala yawo atumidwa kwa iwe. Bwanji, kangati nafuna kukukusa pamojhi ni wana wako pamoji ngati umo nghuku isonghanichila wanapiye wake, namhho anyiimwe simdafune! 35 Vechela! Mujhi wako ulekedwa muumphawi, simunionanjho mbaka ndhawi iyo simkambe, ‘Wali ni mwawi iye uyo wakujha mu jhina la Ambuye.’ "

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-