1 Siku lopumulila, yapo Yesu wamayenda mkati mwa munda wa ngano, oyaluzidwa wake amacha vikonyo va ngano, adayadula ni kudya. 2 Afalisayo wina adawafunjha, "Ndande yanji mchita vindhu ivo sivifunika kuchitika pa Siku Lo Pumulila?" 3 Yesu wadayangha, "Bwanji, simudasome umo wadachitila Daudi ni achanjake yapo adali ni njala? 4 Iye wadalowa mnyumba ya Mnungu ni kutenga mabumunda yayo yadapatulidwaa ndande ya anjhembepe ni wadaagawila achanjake, thauko ilo likaniza mundhu waliyonjhe siwadadya mabumunda yameneyo, nambho anjhembe wokha!" 5 Chimwecho Yesu wadaakambila, "Mwana wa Mundhu nde Mbuye wa siku lopumulila."
6 Siku lina lopumulila, Yesu wadalowa mu nyumba yokomanilana Ayahudi, kuyaluza. Mkati mujha mudali mundhu mmojhi wopuwala jhanja la kwene. 7 Oyaluza thauko ni Afalisayo amatokumpenyechecha yesu kuti aone ngati siwamlamiche mundhu siku lo pumulila, kuti nianyiiwo akhoze kumpacha mlandu. 8 Nambho Yesu wadajhiwa maganizo yao. Chimwecho wadamkambila mundhu yujha wa jhanja lopuwala, "Nyakuka, ima pachogolo pa wandhu." Ni yujha mundhu wadapita kuima pachogolo pajha. 9 Ndiipo Yesu wadaakambila oyaluza thauko ni Afalisayo, "Nikufunjhani anyiimwe, bwanji, ni bwino siku lopumulila kuchita vindhu vabwino kapina kuchita vindhu voipa? Bwanji tikhoza kulamicha umoyo wa wandhu kapina kuyapha?" 10 Wadaapenyechecha konjhekhonje, ndipo wadamkambila mundhu yujha wopuwala jhanja, "Tambasula jhanja lako!" Niiye wadatambasula jhanja lake, nalo lidapata mbhavu. 11 Nambho Afalisayo ni oyaluza matauoko wajha adakwiya kupunda, ni adayamba kufunjhana achinawene kwachinawene umo samchite Yesu.
12 Siku limojhi Yesu wadapita kuphili kupembhela, wadachezela kumweko usiku wonjhe uku ni waapembha a Mnungu. 13 Umawa wake wadaatana oyaluzidwa wake, pakati pa oyaluzidwa ameneo wadaasangha atumwi khumi ni awili, ni wadatana atumwi. 14 Wandhu yawo wadasangha ni anyiyawa, Simoni uyo Yesu wadampacha jhina Petulo, ni Anduleya mkulu wake simoni ni Yakobo, ni Yohana ni Filipo ni Batolomayo, 15 ni Matayo, ni Tomaso ni Yakobo mwana wa Alifayo, ni Simoni uyo wamabulanila jhiko lake, 16 ni Yuda mwana wa Yakobo, ni Yuda Isikaliyoti uyo wadamuukila Yesu pambuyo.
17 Yesu Yapo wadachikapaphili pamojhi ni atumwi wake, wadaima pamalo pakhwawa. Pamenepo padali ni gulu lalikulu la oyaluzidwa wake, ni gulu lalikulu la wandhu kuchokela madela yonjhe ya ku Yudea ni Yelusalemu ni kuchokela kumbwani kwa ku Tilo ni Sidoni. 18 Wandhu achameneo adajha kumvechela Yesu ni kulamichidwa matenda yao, niiye wadalamicha wandhu wajha amavutichidwa ni viwanda. 19 Wandhu wonjhe amafuna kuti amgafye, pakuti mbhavu zimachoka ni kwalamicha wandhu wonjhe.
20 Yesu wadang'anamukila oyaluzidwa wake ni kwakambila,
"Muli ni mwawi anyiimwe osauka,
pakuti Ufumu wa Mnungu ni wanu.
21 Muli ni mwawi anyiimwe muli ni njala,
pakuti pambuyo simukhute.
Muli ni mwawi anyiimwe mulila ndande ya voipa,
pakuti pambuyo simusekelele."
22 "Muli ni mwawi anyiimwe pakuti wandhu akuipilani ni kukupatulani ni kukutukwananani, ni kukutanani anyiimwe ni woipa ndande ya Mwana wa Mundhu. 23 Kondwelani ni kuvinavina yapo siyachokele yameneyo, pakuti zawadi ni yaikulu kumwamba. Pakuti achambuyao adaachitila chimwecho alosi.
24 Nambho, simvutike anyiimwe wopata,
pakuti mwathokala umoyo wa ufulu.
25 Simvutike anyiimwe mwakhuta sazino,
pakuti simuone njala pambuyo.
Simvutike anyiimwe museka sazino,
pakuti pambuyo simuimbe nyimbo za ndhano ni kulila."
26 "Simvutike anyiimwe wandu wohje akutamandani,
pakuti chimwecho nde umo azee wao adaachitila alosi amthila chimwecho."
27 "Nambho nikukambilani anyiimwe munivela, akondeni adani wanu, ni kwachitila yabwino yawo akuipilani. 28 Mwapache mwawi yawo akulosani, apembheleni kwa Mnungu yawo akuchitani voipa. 29 Ngati mundhu awakumenya chaya la kwene, mng'anamukile ni chaya lakumanjele. Mundhu wakakulanda koti lako msiile ni laya lako. 30 Mundhu waliyonjhe wakakupembha mpache, ni ngati mundhu mwina watenga chuma chako usadafuna kuti wakubwezele. 31 Anyiimwe achitileni wina ngati umo mufunila anyiimwe wandhu akuchitileni."
32 "Ngati mwakonda yawo akukondanipe, bwanji, mlangiza ubwino wanji? Ndande ali ni machimo wakonda ali ni machimo anjao. 33 Alafu, ngati mwachitila vabwino wandhu yawo akuchitilani anyiimwe vabwino bwanji, mlangiza ubwino wanji? Ata anyiyawo ali ni machimo ayachita chimwecho. 34 Ni ngati mkakongola wajhape mukulupilila akubwezelenipe, bwanjhi, mulangiza ubwino wanji? Ata yawo ali ni machimo akongolecha amachimo anjao yao akulupilila abwezele. 35 Nambho anyiimwe akondeni adani wanu, achitileni vabwino. Akongoleni popande kukhulupilila kuti sakubwezeleni. Ndiipo mbhoto yanu siikhale yaikulu, ni anyiimwe simukhale Wana a Mnungu wali kumwamba. Pakuti iye ni wabwino kwa wandhu osayamika ni oyipa. 36 Mukhale ni lusungu kwa wandhu wonjhe, ngati umo atate wanu a Mnungu ali ni lisungu."
37 "Msidalamula, namwenjho simlamulidwe, msidalaumu wina, ni Mnungu nayonjho siwakulaumuni anyiimwe, alekeleleni wina, ni Mnungu siwakulekeleleni anyiimwe. 38 Apacheni wandhu wina vindhu, ni Mnungu siwakupacheni anyiimwe. Zenedi, simlandile mmanja mwanu chipimo chojhala ni kuchindilidwa bwino mbaka kumwazika, pakuti chichijha mwapimila wina, nianyiimwe simpimilidwe chimwecho ni Mnungu."
39 Ndiipo Yesu wadakambilanjho chifani ichi, "Bwanji, sapenya wakhoza kumchogoza sapenya mnjake? Notho! Ngati saachite chimwecho ndekuti onjhe awili saabile mjhenje. 40 Uyo wajhiyaluza siwakhoza kujhiwa kupunda kuposa oyaluza wake, nambho waliyonjhe wajhiyeluza wakathomaliza kujhiyeluza wakhala ngati yujha wamyeluza."
41 "Ndande yanji uchipenyecha chikoko icho chili mdiso la mnjako, nambho umwenewake ulemekela kuliona phesi ilo lili mkati mwa diso lako? 42 Kapina, ukhoza bwanji kumkambila m'bale wako, ‘M'bale, ebu nikuchoche chikoko icho chili mudiso lako,’ ni siuliona phesi ilo lili mdiso lako umwene wake? Gunghuli iwe! Poyamba chocha uti phesi ilo lili mdiso mwako, ndipo ukhoze kupenya bwino ni kuchocha chikoko icho chili mkati mwa diso la m'bale wako."
43 "Chimwecho, palibe mtengo wabwino uwo ubala vipacho voipa, kapina mtengo woipa uwo ubala vipacho vabwino. 44 Wandhu aujhiwa mtengo kuchokana ni vipacho vake. Pakuti wandhu sakucha masuku kuchokela ku mitengo yandhujha, kapina mpelesa kuchokela ku mitengo ya kanghande. 45 Chimwecho, mundhu wabwino wachocha vindhu wabwino ivo vasungidwa mumtima mwake. Ni mundhu woyipa wachocha vindhu voipa ivo vasungidwa mumtima mwake. Pakuti mundhu wakamba kuchokana ni vijha vajhala mumtima mwake."
46 "Ndande yanji munitana, ‘Ambuye, Ambuye,’ nambho simchita yayo nikukambilani? 47 Sinikulangizeni chifani cha mundhu uyo wakujha kwaine, nikuyavechela mawu yanga ni kuyatumila. 48 Iye wali ngati mundhu uyo wamanga nyumba, uyo wadakumba msingi panjhi kupunda mbaka pa mwala wolimba nikuyamba kumanga pamenepo. Mafuliko yapo yadajha, yadamenya phupha la nyumba, nambho nyumba imeneyo siidatingizike, pakuti idamangidwa bwino pamalo polimba. 49 Nambho, uyo wavela mawu yanga ni siwayachitumikila, mundhu mmeneyo wali ngati mundhu uyo wadamanga nyumba pamwamba pamchenga, popande kukumba msingi panjhi. Mafuliko yapo yakafika, yadabula nyumba ni idagomoka yonjhe."