Publicidade

Lucas 15

Chifani cha mbelele iyo yasowa

1 Siku limojhi wolandila malipilo ni wandhu amachimo adamjhela Yesu ni kumvechela. 2 Nambho Afalisayo ni oyaluza thauko adadandaula ni kukambilana, "Mundhu uyu waalandila wandhu amachimo ni kudya nawo." 3 Ndiipo Yesu wadaakambila chifani ichi,

4 "Ngati mundhu mmojhi pakati panu wakakhala ni mbelele mia mojha, ni mbelele imojhi yasowa, bwanji, siwazileka tisiini ni tisa zijha nikupita kuthengo kuifuna iyo yasowa mbaka waipate? Siwazileke tisini ni tisa zijha kuphululu ni kupita kuifuna ijha yasowa mbaka waipate. 5 Wakathoipata, siwainyamule paphewa uku ni wakondwela kupunda. 6 Yapo wafika kukhomo, waatana achabwenji lake ni majhilani wake ni kwakambila, ‘Tiyeni tikondwele pamojhi, ndande naipata ijha mbelele iyo idasowa.’ 7 Nikukambilani chimwecho, sikukhale chikondwelo chachikulu kumwamba ndande ya mundhu mmojhi wamachimo uyo walapa, kupitilila wandhu tisini ni tisa wovomelezeka pamaso pa Mnungu yawo kulapa."

Chifani cha gelenjha iyo yataika

8 "Ngati wamkazi wali ni vibandhu khumi va madini ya gelenjha, nambho wakataya imojhi, siwawasha nyali ni kulambula mnyumba ni kuifunafuna mwadongosolo mbaka waipate? 9 Yapo siwaipate, siwatane achabwenji wake ni majhilani wake ni kukamba, ‘Mkondwele pamojhi niine, chifuko chibandhu changa cha madini ya gelenjha icho chidasowa nachiona.’ 10 Nikukambilani chimwecho, kuli chikondwelo pachogolo pa atumiki akumwamba a Mnungu ndande ya mundhu wochimwa mmojhi uyo walapa."

Chifani cha mnyamata wataika

11 Pamenepo Yesu wadayendekela kukamba, "Kudali mundhu mmoji uyo wadali ni anyamata awili waachimuna. 12 Wamng'ono wadaakambila atate wake, ‘Atate, munipache vilanjo vanga.’ Ndiipo atate wao adagawa vindhu vao ni kumpacha chuma chake mwana wamng'onoyo. 13 Pambuyo pa masiku yochepa, mwana wamng'ono yujha wadatenga chuma chonjhe ni kupita ku jhiko la kutali, kumeneko wadatumila chuma chake kwa kuwananga. 14 Yapo wadawananga chuma icho wadalinacho, idachokela njala yaikulu mjhiko limenelo, wadayamba kuhangaika ndande wadalibe kandhu. 15 Chimwecho, wadapita kwa mundhu mmojhi wa jhiko lijha kupembha njhito, niiye wadampeleka ku munda kwake kudyechela nguluwe. 16 Chimwecho mnyamata yujha wadakhumbila kudya chakudya cha nguluwe, nambho padalibe mundhu uyo wadampacha chakudya chilichonjhe. 17 Nambho njelu yapo zidayamba kumbwelela, wadajhikambila mwene, ‘Mnyumba mwa atate wanga muli mbowa zochuluka, izo zikudya chakudya mbaka kutaya, ndande yanji ine nife ni njala!’ 18 Nibwelela kwa atate wanga ni kwaakambila, ‘Atate, nakuchimwilani imwe ni Amnungu kumwamba. 19 Sinifunikanjho kuti nitanidwe mwana wanu. Munichite ngati mmojhi wa mbowa zanu.’ 20 Ndiipo wadayamba ulendo wopita kwa atate wake. Nambho yapo wadali wakali patali, atate wake adamuona, adamlengela lisungu. Adamthamangila mwana wao ni kumkhumbatila kwa chisangalalo. 21 Mwana yujha wadaakambila atate wake, ‘Atate, nakuchimwilani imwe ni Mnungu. Sinifunikanjho kutanidwa mwana wanu.’ 22 Nambho atate wake adaakambila mbowa zake, ‘Pita chisanga katenge njhalu yabwino mumveke! Mvekeni pete ni malapasi ya mtengo waukulu! 23 Mkamtenge njinda ya ng'ombe wonona tichinje, tichite phwando ni tidye! 24 Chifuko mwanawangayu wadamwalila, nambho chipano wali wamoyo, wadataika, nambho wapatikana.’ Ndiipo adayamba kuchita phwando."

25 "Ndhawi imeneyo, mwana wamkulu yujha wadali wakali kumunda. Yapo wamabwela ni kuwandikila pakhomo pao, wadavela nyimbo ni ng'oma ni zibulidwa. 26 Wadamtana mmojhi wa mbowa ni kumfunjha, ‘Bwanji, kuli chiyani?’ 27 Yujha mbowa wadamuyangha, ‘Mphwako wabwela pakhomo, ni atate wako ampha njinda wonona ndande yake amlandila mphako wakali wamoyo.’ 28 Nambho mwana wamkulu yujha wadakwiya ni wadakana kulowa mnyumba. Ndiipo atate wake adatuluka kubwalo ni kumpempha kupunda. 29 Nambho iye wadayangha atate wake, ‘Vechelani! Nakutumikilani vyaka vonjhevi ni palibe siku ilo nakana kuchita icho munilamula, nambho simudanipachepo ata kamwana ka mbuzi kuti nichite phwando niachabwenji langa! 30 Nambho mwana wanu uyu uyo wawananga chuma chanu ni mahule, yapo wabwela pakhomo mwamphela njinda ya ng'ombe!’ 31 Atate wake adamuyangha, ‘Mwana wanga, iwe uli pamojhi nane masiku yonjheya, ni vindhu vonjhe ivo nilinavo ni vako. 32 Chimwecho, imafunika tichite phwando ni kukondwela, ndande mbale wakoyu wadamwalila, nambho chipano wali wamoyo ni wadataika nambho chipano wapatikana.’ "

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-