1 "Nakukambilani yameneyo dala nikuimicheni nganganga kuti simudachisia chikhulupillilo chanu. 2 Wandhu sakutopoleni munyumba zao zokomanilana Ayahudi ni kulambila. Ndhawi ikujha waliyonjhe uyo wakuiphani anyiimwe siwaghanizile kuti wamtumikila Amnungu. 3 Sakuchitileni vindhu vimenevo ndande saajhiwa Atate, ni sanijhiwa ine. 4 Basi, nakukambilani vindhu ivi dala ndhawi ikajha, mkumbukile kuti nidathokukambilani.
"Sinidakukambileni vindhu ivi kuyambila mmayambo ndande nidali pamojhi namwe. 5 Chipano nipita kwayao anituma, nambho palibe uyo wanifunjha uko nipita. 6 Pakuti nakukambilani vindhu vimenevo, mwajhalidwa ni chisoni mmitima mwanu. 7 Nambho nikukambilani uzene, mbasa ine nipite, mate yake nikasiya kupita Othandiza siwajha kwanu. Nambho nikapita, sinimtume kwanu. 8 Nayo yapo siwajhe siwachimikizile wandhu ajhiko nghani za machimo, kuvomelezeka ni lamulo la Amnungu. 9 Achita machimo, ndande sanikhulupilila, 10 Mzimu woyela siwachimikizile kuusu kuvomelezeka kwanga pachogolo pa Amnungu, ndande nipita kwa Atate, nawo sanionanjho. 11 Kuusu kulamula, ndande satana wamkulu wa jhiko lino, watho lamulidwa.
12 "Nikali nayo yambili yakukukambilani, nambho kwa chipano simuyakhoza kuimila nganganga. 13 Nambho yapo suujhe Mzimu wa uzene siukuchoghozeni kuuzene onjhe, iye siwakamba kwa lamulo lake mwene, nambho siwakambe yayo wayavela kuchoka kwanga ni kukujhiwichani vindhu ivo sivichokele pambuyo. 14 Iye siwanipache ine ulemelelo pakuti siwakujhiwicheni yayo siwayapate kuchoka kwanga. 15 Vonjhe alinavo Atate nivanga, ndendande nakamba kuti Mzimu wa uzene siukujhiwicheni ivo siwayapate kuchoka kwanga."
16 "Ikali ndhawi yochepa, namwe simunionanjho, ni pambuyo pa ndhawi yochepa simunione!"
17 Chimwecho oyaluzidwa wake wina adafunjhana, "Walinimate yanji yapo wakamba, ‘Ikali ndhawi yochepa simunionanjho, ni ndhawi yochepa simunionenjho?’ Ni wakambanjho, ‘Pakuti nipita kwa Atate!’ 18 Wali ni mate yanji yapo wakamba, ‘Ikhali ndhawi yochepape?’ Sitijhiwa kuti wakamba chiyani."
19 Yesu wadajhiwa kuti amafuna kumfunjha, ndiipo wadaakambila, "Bwanji mfunjhana ndande nakamba, ‘Ikali ndhawi yochepa simuniona ni pambuyo pa ndhawi yochepa simunionenjho?’ 20 Nikukambilani uzene, anyiimwe simulile ni kuchita zaya, nambho wandhu ajhiko sakondwe, simukhale ni chisoni nambho chisoni chanu siching'anamuke ni kukhala chimwemwe. 21 Ndhawi iyo maye wajhimasula, wakhala ni chisoni ndande ndhawi yopweteka yafika, nambho wakatho jhimasula siwakumbukila kupweteka ndande ya chimwemwe chobadwa kwa mundhu pajhiko. 22 Chipano anyiimwe muli ni chisoni, nambho ine sinikujeleninjhoni, ni mitima yanu siikondwe, ni palibe mundhu uyo siwachichoche chimwemwe kwanu."
23 "Siku limenelo simunipembha ine chilichonjhe. Zene nikukambilani, chilichonjhe icho simwaapembhe Atate ngati umo nifunila saakupacheni. 24 Mbaka chipano simudanipembhe kandhu kalikonjhe kwa ulamulilo wanga. Pembhani namwe simupate dala chikondwelo chanu chikwanile."
25 "Nikukambilani vindhu vimenevo kwa kukuluwika. Nambho ndhawi ikujha sinikamba namwe kwa kukuluwika, nambho sinikambe namwe padanga nghani za Atate. 26 Siku limenelo simupembhe kuchokana ni anyiimwe umo munikhulupilila, ni sinikukambilani kuti sinikupembheleni kwa Atate, 27 Pakuti Atate akukondani anyiimwe, ni ndande anyiimwe mwanikonda ine ni mwakhulupilila kuti nachoka kwa Amnungu. 28 Ine nidachoka kwa Atate, nidajha pajhiko, ni chipano nilisiya jhiko nibwela kwa Atate."
29 Ndiipo, oyaluzidwa wake adamkambila, "Chipano ukamba popande kubisa ni siukamba kwa kukuluwika. 30 Chipano tijhiwa kuti iwe ujhiwa kila kandhu, ni palibe ndande yakukufunjha mafunjho. Tikhulupilila kuti wachoka kwa Amnungu."
31 Yesu wadaafunjha, "Bwanji, mkhulupilila chipano? 32 Ndhawi ikujha, ni yathofika yapo simmwazikane kila mmojhi siwapite kukhomo kwake, ni anyiimwe simunisiye ine nekha. Nambho ine sinilinekha, pakuti Atate alipamojhi niine. 33 Nakukambilani vindhu ivi dala mukhale ni mtendele pakulunjana niine. Simvutike pajhiko, nambho jhipacheni mtima! Ine nazikhoza mbhavu zoipa za jhiko lino!"