1 Kukakhala ni chindhu chalichonjhe cha kukutilani mtima kwa kulunjidwa Nikilisito, kukakhala ni mtendele walionjhe wa chikondi. Kugwilizana ni Mzimu, lika khalapo lisungu ni kulekelela wina. 2 Chitani yajha siyakwaniliche chimwemwe changa, ili mukhale ni kugwilizana, chikondi chimojhi, mtima umojhi ni kuganizila pamojhi. 3 Msada chita chindhu chalichonjhe kwandane yanu kapina kujidamila, ila kwa kunyenyekela kila mmojhi wamuone mnjake wamate kupita iye. 4 Kila mmojhi siwadajhipenya kupata kwake mwenepe, nambho wapenye kupata kwa mnjake. 5 Mukhale chimchijha ngati mujha muda khalilala ni Kilisito Yesu.
6 Iye kwa chiyambo wadali Mnungu,
siwadaone kujha kulingana ni Mnungu.
7 Iye wadajhichita si kandhu,
wadajhichita walingana ni mbowa.
Wadali ngati wandhu
wadaonekana ngati mundhu.
8 Wadanyenyekela ni kuvomela kumwalila
nyifa ya pamtanda.
9 Ndande imeneyo Mnungu adamwika pamwamba kupunda
nikumpacha jhina lalikulu kupitilila kila jhina.
10 Ili pa jhina la yesu kila mundhu walambile
kila chindhu cha kumwamba, pajhiko la panjhi, ni vapanjhi pa jhiko,
11 ni kila lilime livomele kuti YESU KILISITO NI AMBUYE,
pa ulemelelo wa a Mnungu Atate.
12 Nchimwecho okondedwa, yapo nidalinamwe mudanilemekeza masiku yonjhe, atachipano yapo nali patali namwe endekelani kulemekeza, chitani njhito kwa mandha ni kutendhemela ndande ya kuomboledwa kwanu, 13 pakuti Mnungu ndeuyo wachita njhito mukati mwanu, nikukupachani kukhoza nikuchita kwanu kwa kuchita chijha akufuna uchite.
14 Yachiteni yonjhe popande kudandaula wala kulimbana, 15 ili mkhale wana wa Mnungu mulibe lawama ni hatiya, ata ngati mukhala nikuzungulilidwa niwandhu anyiyawo akhala mujhiko loyipa ni lotayika simung'azikile pakati pao ngati umo ndhondwa zing'azila pajhiko, 16 muka uzila mawu ya umoyo nipamenepo nde yapo sinione ufulu siku la Kilisito kuti kulindilila ni njhita yanga vidachitike chajhe.
17 Atangati sinichochedwe njhembe pamojhi nichikhulupi chanu chili ngati njhembe kwa Mnungu, basi nikondwela kupunda kukugwilizani anyiimwe mwaonjhe chimwemwe chimenecho. 18 Nchimwecho namwe mfunika kukondwa ni kunigwiliza ine chimwemwe chanu.
19 Nikhulupila mwa Ambuye Yesu kumtuma Timoseo posachedwa yapa wajhe kwanu, kuti nitilidwe mtima kwa kupata nghani zanu. 20 Nilibe Mundhu mwina ngati timoseo uyo siwakupnyeleleni. 21 kila mmojhi wachita vindhu vake mumalo mwochita vindhu va Yesu Kilisito, 22 nambho mwachinawene mujhiwa umo timoseo wadajhichimikiza mwene, pakuti watumika pamojhi ni ine kulalikila Uthenga Wabwino. 23 Chimwecho nikhulupila kumtuma malakamojhi nikango jhiwa vindhu vanga umovikhalile. 24 Nane nikhulupila mwa Ambuye kuti nane sinijhe posachidwa.
25 Naona nafunika kumtuma kwanu mbale wathu Epafulodito, uyo mtumiki mnjanga, ni asikali mnjanga tenanjho nimtumiki mnjanu mudamtuma ili wani thangatile yapo nifuna mthandizo. 26 Wali ni khumbilo lalikulu lakukuonani anyiimwe mwaonjhe, wadandaula kupunda ndande anyiimwe mudavela wamadwala, 27 Yetudi wamadwala mbaka jhenje lokumbakumba, nambho Amnungu adamlengela lisungu niopande iyepe nambho ataine adanilengela lisungu nisidakhala ni chisoni. 28 Chimwecho nichita msanga kumtuma ili yapo simumuonenjho mukhale ni chimwemwe niine nichepe chisoni. 29 Mlandileni iye kwa chimwemwe mwa Ambuye, mwalemekeze wandhu ali ngati Epaflodito, 30 wafunika kulemekezedwa ndande wamafuna kumwalila yapo wama lalikila Uthenga Wabwino, wadaika umoyo wake iliwakhoze kunipacha ine mtandizo uwo anyiimwe simudakhoze kunipacha.