1 Anyiimwe wana, ndande mwalunjana ni Ambuye Yesu mujhavela obala wanu pakuti ichi ni chindhu cha bwino. 2 "Alemekeze Atate wako ni amaye wako," ili nde lamulo loyamba ilo adakamba Ambuye, 3 "Upate mwawi ni ukhale vyaka vambili pajhiko."
4 Namwe anya Atate, simdachitila voipa wana wanu, nambho aleleni akhale ni ulemu ni mayaluzo ya Ambuye.
5 Namwe akapolo, mjhavela achambuye wanu apano pajhiko, kwa kwalemekeza. Chitani chimwecho kwa mtima wabwino ngati kumvela Kilisito. 6 Chitani chimwecho, asati yapo akupenyanipe dala kwa kwadilicha, nambho tumikilani kwa mtima wabwino ngati umo wafunila Mnungu, ndande anyiimwe ni akapolo a Kilisito. 7 Chitani njhito kwa mtima onjhe kwa kukondwela, ngati kwa atumikila Ambuye, asati kwa kwatumikila wandhu. 8 Mjhiwe kuti kila uyo wachita vabwino, wakhale kapolo kapina mfulu, siwalandile mbhaso kuchoka kwa Ambuye.
9 Namwe yawo mutumikilidwa, achitileni chimwecho akapolo wanu, simudaofya. Kumbukilani kuti anyiimwe muli ngati anyiiwo, Muli ni Ambuye yuyujha mmojhi wakumwamba, nayo sampatula mundhu.
10 Mathelo, niikufunani mukhale nganganga pa kulunjana ni Ambuye ni kwa kukhozechedwa kwa mbhavu zake. 11 Valani vida vonjhe va Mnungu, mkhoze kuchekeleza misambha ya Satana. 12 Nghondo yathu asati kubulana ni wandhu, nambho kubulana ni magulu ya viwanda mujhiko la chizimu, tibulana ni alamuli, afumu ni ambhavu za yawo alamulila jhiko lino la chizimu. 13 Chimwecho, valani vida ivo wakupachani Mnungu, mkhoze kulimbana pa siku la mavuto, ni mkabulana mbaka pothela simuendekele kukhala nganganga.
14 Chipano, imani nganganga, muli wojhimanga zene ngati lamba muchiuno mwanu, kuvomelezeka kukhale ngati chivalo cho jhikengelela pamtima, 15 mkhale tayali kulalikila Uthenga Wabwino wa mtendele ngati vilato myendo mwanu. 16 Kupitilila yonjhe, chikhulupi chikhale chitetezo mmanja mwanu, chikhoze kizithima misonga ya moto ya satana. 17 Ulandileni uomboli ngati chisoti cha chichulo, ngati upanga wa Mzimu uwo uli mawu la Mnungu. 18 Pembhelani siku zonjhe kwa mbhavu ya Mzimu, nikupembha mthandizo wa Mnungu. Chezelelani popande kulema nimwapembhela wandhu onjhe a Mnungu. 19 Mjhinipembhela ni ine, dala yapo nikamba, Mnungu wanipache chokamba, nikhoze kuuzila chisisi cha Uthenga Wabwino kwa kupilila, 20 pakuti Mnungu wanituma kuuzila Uthenga Wabwino, ingakhale namangidwa. Chimwecho nipembheleni, dala nikhoze kuima nganganga pakulalikila ngati umo ifunikila.
21 Chimwecho, nimtuma Tukiko mbale wathu uyo timkonda kupunda, ni mtumiki okhulupilika kwa kulunjana ni Ambuye, siwakujhiwicheni nghani zanga zonjhe dala mujhiwe icho nichita. 22 Nimtuma kwanu wakupacheni nghani zathu, dala wakuthileni mtima.
23 Chimwechpo achabale wanga nimpembha Mnungu Tate ni Atate wathu Yesu Kilisito, akupacheni mtendele, chikondi ni kukhulupilila. 24 Nimpembha Mnungu, wakupacheni Ubwino mwaonjhe yawo mukonda Ambuye wathu Yesu Kilisito, kwa chikondi icho chilibe mathelo.