Publicidade

João 7

Yesu siwakhulupilidwa ni achabale wake

1 Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadachita njhito mmalo ya mbili ya Galilaya. Siwamafune kupita ku Yudea ndande achogholeli wa Ayahudi amafuna kumpha. 2 Ndhawi imeneyo Phwando la Ayahudi la Visakasa yani kukumbukila kusamuka samuka kuphululu lidawandikila, 3 ndiipo, achabale wake adamkambila, "Uchokepo pano upite ku Yudea dala oyaluzidwa wako azione njhito izo uchita. 4 Mundhu siwachita vindhu ko bisika ngati wafuna kujhiwika ni wandhu. Pakuti uchita vindhu ivi, chipano jhijhiwiche pajhiko la panjhi." 5 Ndande ata achabale wake sadamkhulupilile.

6 Ndiipo Yesu wadaakambila, "Ndhawi yanga iyo ifunika ikali yosafike. Nambho anyiimwe ndhawi yanu ilipo sikuzonjhe. 7 Wandhu apajhiko saakhoza kukuipilani anyiimwe, nambho ine aniipila ndande nachocha umboni wa vindhu ivo avichita ni voipa. 8 Anyiimwe mapitani kuphwando. Ine sinipita kuphwando limenelo, ndande ndhawi yanga siida fike." 9 Yapo wadakamba yameneyo, wadakhalila ku Galilaya.

Yesu kuphwando la visakasa

10 Achabale wake yapo adapita kuphwando, Yesu nayo wadapita kuphwando, nambho wadapita kwa chisisi. 11 Chimwecho achogholeli wa Ayahudi amato mfunafuna pa phwando limenelo, adafunjhila, "Wali kuti mundhu yujha?"

12 Kudali ni kung'olong'ota kwambili kuusu Yesu pakati pa gulu la wandhu. Akumojhi wao adakamba, "Mundhu uyu ni wabwino." Wina adakamba, "Notho! Wanyenga wandhu." 13 Nambho padalibe mundhu uyo wadakamba ngani za Yesu pa ndhandala, ndande amaopa achogholeli wa Ayahudi.

14 Pwando yapo lidafikila pakatikati, Yesu wadapita pa Nyumba ya Amnungu, ni kuyamba kuyaluza. 15 Basi, Ayahudi adazizwa ni kukamba, "Mundhu uyu wapata kuti mayaluzo yaya niuku siwadasome?"

16 Ndiipo Yesu wadayangha, "Mayaluzo yayo niyaluza opande yanga, nambho yachoka kwa yujha wanituma. 17 Mundhu uyo wakonda kuchita icho afuna Amnungu, siwajhiwe mayaluzo yanga ngati yachokela kwa Amnungu, kapina nikamba yanga namwene. 18 Mundhu wajhikambila mwene wafunafuna uelekelo wake mwene, nambho uyo wafunafuna uelekelo wa uyo wanituma, mmeneyo wazene ni walibe voipa mkati mwake. 19 Bwanji Musa siwadakupacheni Thauko? Nambho palibe mmojhi wanu uyo waligwila thauko. Ndande mufuna kunipha?"

20 Ndiipo wandhu adamuyangha, "Iwe uli ni viwanda! Yani wafuna kukupha?"

21 Yesu wadaayangha, "Ine nachita chizindikilo chimojhi, mwaonjhe chakudabwichani 22 Musa wadakuagizani mwachite mdulidwe wana wanu. Ingakhale silidachoke kwa Musa, nambho lidachokela kwa azee wanu. Namwe mumchita mundhu mdulidwe mbaka Siku lo Pumulila. 23 Ingakhale mundhu wachitidwa mdulidwe mbaka Siku Lopumulila dala Thauko silida wanangidwa, ndande yanjhi mukwiya ndande ine namlamicha mundhu Siku Lopumulila? 24 Msidamlamula mundhu kwa kumpenya kubwalope, nambho mchoche lamulo lovomelezeka."

Bwanji, yuno nde Kilisito?

25 Wandhu wina a ku Yelusalemu adamatofunjhana, "Bwanji, mundhu yujha amfunafuna amphe sinde uyu? 26 Chipano wali pano, wakamba pachogolo pa wandhu wonjhe, nambho palibe uyo wamkambila kandhu. Bwanji, kapina achogholeli ajhiwa kuti uyu nde Kilisito? 27 Nambho kilisito yapo siwajhe palibe mundhu uyo siwamjhiwe kumalo uko wachoka, nambho ife tijhiwa uko wachoka mundhu uyu!"

28 Ndiipo, Yesu yapo wamayaluza pa Nyumba ya Amnungu wadakweza mvekelo ni kukamba, "Anyiimwe munijhiwa ni mujhiwa uko nichoka. Sinidajhe kwa lamulo langa namwene, nambho uyo wanituma ine wazene, namwe simumjhiwa. 29 Nambho ine nimjhiwa ndande nachoka kwake, nde uyo wanituma."

30 Ndiipo, wandhu amafuna kumgwila, nambho palibe uyo wadayesa kumgwila ndande ndhawi yake idali ikali yosafike. 31 Wandhu ambili pagulu lijha adamkhulupilila, adakamba, "Bwanji, Kilisito yapo siwajhe siwachite vizindikilo vavikulu kupitilila ivi wachita mundhu uyu?"

Alonda adatumidwa amgwile Yesu

32 Afalisayo adavela wandhu niang'olong'ota kuusu nghani za Yesu. Ndiipo anyiiwo ni ajhukulu wakulu wadaatuma alonda amgwile. 33 Chimwecho Yesu wadaakambila, "Nikali namwe kwa ndhawi yo chepa, ndiipo sinipite kwa yujha wanituma. 34 Simunifunefune nambho simuniona, ni yapo sinikhale ine anyimwe simkhoza kufika."

35 Achogoleli wa Ayahudi adakambilana achinawene kwa chinawene, "Mundhu uyu siwapite kuti uko sitikhoza kumfunafuna? Siwapite kwa Ayahudi yawo ali kwa Agiliki, ni kwaayaluza? 36 Wali ni mate yanji yapo wakamba simunifunefune nambho simunipheza, ni simukhoza kufika?"

Viwila va majhi ya umoyo

37 Pasiku lothela siku la phwando, Yesu wadaima, wadakamba kwa mvekelo waukulu, "Uyo wali ni lujho wajhe kwanga wamwe. 38 Ngati umo yakambila Malembo Yoyela, ‘Uyo wanikhulupilila ine, viwila va majhi ya umoyo sivisililike mumtima mwake!’" 39 Wadakamba chimwecho kuusu Mzimu Woyela uwo samlandile anyiyawo amkhulupilila. Ndhawi imeneyo Mzimu Woyela udali ukali siudafike ndande Yesu wadali wakali osapachidwe ulemelelo.

Mkangano pakati pa wandhu kuusu Yesu

40 Wandhu wina pa gulu lijha yapo adavela nghani za Yesu, adakamba, "Zenedi mundhu uyu nde yujha mlosi!"

41 Wina adakamba, "Uyu nde Kilisito!"

Nambho wina adakamba kuti, "Siikhozeke bwanji Kilisito wachokele ku Galilaya? 42 Bwanji malembo Yoyela siyakamba kuti, Kilisito siwachokele kukhamu la Daudi, ni siwabadwe ku Beselehemu, mujhi wa Daudi?" 43 Ndiipo kudachokela mkangano pakati pa gulu la wandhu ndande ya Yesu. 44 Wandhu wina amafuna kumgwila nambho padalibe uyo wadayesa kumgwila.

Achogholeli wa Ayahudi akana kumkhulupilila Yesu

45 Chimwecho alonda adabwela kwa ajhukulu wakulu ni Afalisayo, ni anyiiwo adaafunjha, "Ndande yanji simudajhenaye pano?"

46 Alonda adayangha, "Palibe mundhu wakhoza kukamba ngati umo wakambila mundhu uyu!"

47 Ndiipo, Afalisayo adaafunjha wajha alonda, "Bwanji namwe mwanyengeka? 48 Palibe mchogholeli waliyonjhe kapina Afalisayo uyo wamkhulupilila? 49 Nambho gulu ili la wandhu lidamkhulupilila uku lali silijhiwa Thauko la Musa, gulu limenelo lalesedwa ni Amnungu!"

50 Ndiipo Nikodemo mmojhi wa Afalisayo, uyo wadamchata Yesu usiku, wadafunjha, 51 "Bwanji Thauko lathu limlamula mundhu wakali osavecheledwe huti ni kujhiwa wachita chiyani?"

52 Nawo adayangha, "Nawenjho wachoka ku Galilaya? Yapenyecheche malembo yoyela, pamenepo nde siujhiwe ku Galilaya siwachoka mlosi!" 53 Ndiipo, onjhe adachoka, kila mmojhi wadabwela kukhomo lake.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-