Publicidade

João 6

Yesu waapacha wandhu elufu zisano chakudya

1 Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadayomboka nyanja ya Galilaya, iyo imatanidwanjho Tibelia. 2 Ndiipo Gulu lalikulu la wandhu lidaendekela kumchota ndande adaviona vizindikilo ivo wadachita pa kwalamicha odwala. 3 Ndiipo Yesu wadakwela kuphili, wadakhala pamojhi ni oyaluzidwa wake. 4 Ndhawi imeneyo phwando la Pasaka la Ayahudi lidawandikila. 5 Yesu yapo wadapenya ni kuona gulu lalikulu nilimjhela, wadamkambila Filipo, "Sitigule kuti mabumunda yakudya wandhu adye?" 6 Yesu wadakamba chimwecho kwa kumuyesa Filipo, pakuti wadajhiwa icho siwachichite.

7 Ndiipo Filipo wadamuyangha, "Ata ngati tidakhala ni ndalama zochuluka sizikwana kughula chakudya cha kwakwana wandhu anyiyawa, hata ngati kila mmojhi wasiwapachidwe chibandu chaching'onope"

8 Oyaluzidwa wake mwina uyo wamatanidwa Andulea, mbale wake wa Simoni Petulo, wadamkambila, 9 "Walipo mnyamata mmojhi uyo wali ni mabumunda yasano iyo yakonjedwa kwa ufa wa shayili ni njhomba ziwili, nambho vindhu ivi sivikwana kwa wandhu onjhewa?"

10 Ndiipo Yesu wadakamba, "Akambileni wandhu akhale panjhi." Pamalopo padali ni matengo yayafupiyafupi yambili. Ndiipo adakhala, adalipo wachimuna elufu zisano. 11 Chimwecho Yesu wadatenga mabumunda, wadaayamika Amnungu, wadagaawila wandhu anyiyao adakhala panjhi, kila mmojhi wadapata ngati umo wadafunila, wadachita chimwecho ni zijha njhomba. 12 Wandhu yapo adakhuta, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Kusani vipande ivo va khala visadataika." 13 Chimwecho adakusa vipande vijha va mabumunda ni kuvitila mvitundu. Adavijhaza mvitundu kumi ni viwili.

14 Ndiipo wandhu anyiwajha yapo adaona vizindikilo ivo wadachita Yesu, adakamba, "Zenedi uyu nde mlosi uyo wakujha pa jhiko." 15 Yesu yapo wadajhiwa kuti wandhu amafuna amgwile dala amchite mfumu kwa mbhavu, wadajhipatula, ni kupita yokha ku phili.

Yesu wayenda pamwamba pa majhi

16 Jhuwa yapo limabila, oyaluzidwa wake adachika kunyanja, 17 adakwela sitima kupita ku Kapelinaumu. Mdima udalowa nambho Yesu wadali wakali osafike. 18 Nyanja idayamba kuvunduka ndande ya vuma wa mkulu. 19 Oyaluzidwa yapo adapita patali ngati meta zitatu kapina zinai, adamuona Yesu ni waenda pamwamba pa majhi, wadawandikila sitima, adaopa kupunda. 20 Ndiipo Yesu wadakambila, "Simudaopa, ni ine!" 21 Yapo adamkalibisha Yesu mu mbwato, ndhawi imweyo adafika kujhiko ilo amapita.

Wandhu amfunafuna Yesu

22 Mawa lake, gulu la wandhu yao adakhaalila kuchija la kawili la nyanja nipo adajhiwa kuti kudalipo ni bwato umojhipe, ni Yesu siwadakwele pamojhi ni oyaluzidwa wake, nambho oyaluzidwa adali apita okha. 23 Chimwecho zidafika mabwato yina kuchoka ku Tibelia kumalo uko adadya wandhu mabumunda, Ambuye Yesu yapo adayamika Amnungu. 24 Wandhu yapo adajhiwa kuti Yesu ni oyaluzidwa wake achokapo pamenepo, adakwela mbwato kupita ku Kapelinaumu kumfunafuna.

Yesu ni Bumunda ilo lipeleka Umoyo

25 Yapo adampheza kuchija lakawili la nyanja adamfunjha, "Oyaluza mwafika siku lanji pano?"

26 Yesu wadayangha, "Zene nikukambilani, munifunafuna osati ndande mudaviona vizindikilo, nambho ndande mudadya mabumunda ni mudakhuta. 27 Msadajhichaucha ndande ya chakudya icho chilula, nambho jhichaucheni ndande ya chakudya icho sichilula ndande ya umoyo wa muyaya. Mwana wa Adamu uyo Atate amchimikiza siwakupacheni chakudya chimenecho."

28 Ndiipo adamfunjha Yesu, "Tichite chiyani kuti tikhoze kuichita njhito ya Amnungu?"

29 Yesu wadayangha "Ino nde njhito iyo Amnungu afuna muichite, kumkhulupilila uyo amtuma."

30 Ndiipo adamfunjha, "Siutichitile chizindikilo chanji tione kuti tikhoze kukukhulupilila? Bwanji, siuchite chindhu chanji? 31 Azee wathu adadya icho chidatanidwa mana yapo adali kuphululu, ngati umo yalembedwa, ‘Wadaapacha chakudya icho chidachoka kumwamba.’ "

32 Ndiipo Yesu wadakambila, "Zene nikukambilani, osati Musa uyo wadakupachani chakudya kuchoka kumwamba, nambho Atate wanga nde yao akupachani chakudya cha uzene kuchoka kumwamba. 33 Pakuti bumunda la Amnungu nde uyo wachika kuchoka kumwamba ni kwapacha umoyo wandhu a jhiko la panjhi."

34 Ndiipo adamkambila, "Tipache chakudya chimenelo siku zonjhe."

35 Chimwecho wadaakambila, "Ine nde chakudya cha umoyo. Uyo wakujha kwanga siwaona njala ni uyo wanikhulupilila siwaona lujho muyaya. 36 Nambho ngati umo nidakukambilani ata ngati mwaniona simunikhulupilila. 37 Wandhu onjhe yao Atate sianipache sianichate, ni mundhu waliyonjhe uyo wakujha kwanga sinimkana, 38 pakuti nachika kuchoka kumwamba osati ndande yo chita ivo nivifuna, nambho kuchita ngati umo wafunila uyo wanituma. 39 Ni umu nde umo afunila yawo anituma, sinida mtaiza ata mmojhi pakati pa anyiyao anipacha, nambho nahyuche onjhe siku lo thela. 40 Chindhu cha chikulu icho achifuna Atate wanga kuti, waliyonjhe uyo wamuona mwana ni kumkhulupilila wakhale ni umoyo wa muyaya, nane sinimuhyuche siku lo thela."

41 Ndiipo, Ayahudi adayamba kumng'olong'otela yapo wadakamba kuti, "Ine nde chakudya icho chachika kuchoka kumwamba." 42 Niamakamba, "Uyu osati Yesu mwana wa Yusufu? Tajhiwa atate wake ni amake! Bwanji wakamba kuti iye wadachika kuchoka kumwamba?"

43 Ndiipo Yesu wadaakambila, "Siyani kung'olong'otelana mwachina wene kwa mwachinawene. 44 Palibe mundhu uyo wakhoza kujha kwanga, ngati siwadaghuzidwe ni Atate yao anituma, nane sinimuhyuche mundhu mneyo siku lo thela. 45 Yalembedwa mvikalakala va alosi, ‘Wandhu wonjhe sayaluzidwe ni Amnungu.’ Waliyonjhe uyo waavela Atate ni kujhiyaluza kwa iwo, wakujha kwanga. 46 Palibe uyo waonapo Atate, nambho uyo wachoka kwa Amnungu, mmeyo nde uyo waona Atate. 47 Nikukambilani zene, uyo wakhulupilila wali ni umoyo wa muyaya. 48 Ine nde chakudya cha umoyo. 49 Azee wanu adadya chakudya icho chitanidwa mana ku phululu, nambho adamwalila. 50 Nambho chino nde chakudya icho chichoka kumwamba, kuti waliyonjhe uyo wakudya siwadamwalila. 51 Ine nde chakudya chili cha moyo icho chachika kuchoka kumwamba. Mundhu waliyonjhe uyo siwadye chakudya ichi siwakhale moyo muyaya. Ni chakudya icho sinimpache, nde thupi langa ilo nichocha ndande ya wandhu ajhiko la panjhi."

52 Ndiipo Ayahudi adayamba kulimbana pakati pao, "Siwakhoze bwanji kutipacha thupi lake, tidye?"

53 Ndiipo Yesu wadaakambila, "Zene nikukambilani, mkasiya kudyaa thupi la mwana wa Mundhu ni kumwa mwazi wake, simukhala ni umoyo mkati mwanu. 54 Kila mmojhi uyo siwadye thupi langa ni kumwa mwazi wanga wali ni umoyo wa muyaya, nane sinimuhyuche siku lo thela. 55 Ndande thupi langa nde chakudya cha uzene, ni mwazi wanga nde chakumwa cha uzene. 56 Uyo wakudya thupi langa ni kumwa mwazi wanga, siwakhale mkati mwanga, nane sinikhale mkati mwake. 57 Ngati umo Atate yawo ali amoyo adanitumila, nane nili wamoyo kupitila iwo, chimwecho uyo waniidya ine siwakhale moyo kupitila ine. 58 Chino nde chakudya icho chachika kuchoka kumwamba, osati ngati mana iyo adadya azee wanu, ndiipo adamwalila. Uyo wakudya bumunda lino siwakhale moyo muyaya." 59 Yesu wadakamba mawu yameneyo yapo wamayaluza ku Kapelunaumu.

Mawu yayo yapeleka umoyo wa muyaya

60 Chimwecho, ochatila wake ambili yapo adavela mawu yameneyo, adakamba, "Mayaluzo yaya yolimba! Yani wakhoza kuyavomela?"

61 Yesu wadajhiwa mumtima mwake kuti oyaluzidwa wake amato dandaulila mawu limenelo, wadaafunjha, "Ndande yanji mayaluzo yaya yakujhujhumuchani? 62 Siikhale bwanji yapo simumuone Mwana wa Mundhu niwabwela kupita kumwamba uko wadachoka? 63 Mzimu wa Amnungu nde uwo uchocha umoyo, thupi silikhoza kandhu. Mawu yayo nakukambilani ni mzimu ni umoyo. 64 Nambho, akumojhi wanu saakhulupilila." Yesu wadaajhiwa kuyambila mmayambo anyiyawo saamkhulupilila, ni uyo siwamng'anamuke. 65 Chimwecho, wadakamba, "Nde ndande nidakukambilani kuti palibe uyo wakhoza kujha kwaine popande kukhozechedwa ni Atate wanga."

66 Ndhawi imweyo, ochatila ambili pakati pao adamsiya, siadachogozane nayenjho. 67 Ndiipo, Yesu wadaafunjha ochatila khumi ni awili, "Anyiimwe namwe mfuna kuchoka?"

68 Simoni Petulo wadamyangha, "Ambuye tipite kwa yani? Akati imwe muli ni mawu ya umoyo wa muyaya. 69 Ife tikhulupilila, ni tijhiwa kuti imwe nde yujha Oyela Amnungu"

70 Yesu wadaakambila, "Bwanji, sinida kusangheni anyiimwe khumi ni awili? Ata chimwecho mmojhi wanu Satana!" 71 Yesu wamamkamba nghani za Yuda mwana wa Isikaliyote, mmojhi wao oyaluzidwa anyiwajha khumi ni awili, uyo pambuyo wadamgulicha.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-