1 Yesu wadaatana pamojhi wajha khumi ni awili, wadapacha mbhavu ni ulamulilo wochoha viwanda ni kwalamicha wodwala yonjhe. 2 Ndiipo wadatuma apite akalalikile wandhu ufumu wa Mnungu ni kwalamicha wodwala. 3 Iye wadakambila, "Yapo mupita ulendo wanu musadatenga kandhu kalikonjhe, msadatenga mpulu, kapina chikwama, kapina chakudya, kapina ndalama, kapina njhalu yong'anamulila. 4 Nyumba yaliyonjhe iyo simulowe ni kukulandilani, khalani mmenemo mbaka yapo simuchoke mmujhi umeneo. 5 Ngati wandhu sakane kukulandilani mnyumba zawo, niyapo simujichoka, mkung'undhe malifumbi ya mmyendo mwanu kulangiza kuti anyiiwo asangha kuukana Uthenga wa Mnungu." 6 Chimwecho, wanyiwajha khumi ni awili adauyamba ulendo wopita kila kumalo uku nalalikila wandhu Uthenga wa Wabwino ni kulamicha odwala kila kumalo.
7 Chipano, Helode mfumu wa ku Galilaya, yapo wadavela nghani zonjhe izo zidachitika, ni wadachauchika mmaganizo chifuko wandhu wina amakamba, "Yohana mbatizi yujha wahyuka." 8 Nambho wina amanena kuti Eliya watulukila, ni wina amanena kuti mmojhi wa alosi akale wahyuka. 9 Nambho Helode wadakamba, "Yohana mmeneyo nidamdula mutu, chipano, mmeneyo ni yani nivela nghani zake?" Ndiipo wadafuna kupunda kuti wamuone.
10 Atumwi wake wajha yapo adabwela adamkambila Yesu yonjhe yayo adayachita. Yesu wadaatenga ni kupita nao kwa chisisi, mbaka ku mujhi uwo utanidwa Betisaida. 11 Nambho gulu la wandhu lijha yapo lidajhiwa uko wadapita Yesu, lidamchata. Yesu wadalandila ni kukamba nao nghani za Ufumu wa Mnungu ni kwalamicha wandhu wonjhe yao amafuna kulamichidwa.
12 Ujhulo, atumwi khumi ni awili wajha adafika kwa Yesu ni kumkambila, "Alaileni wandhu yawa apite kumijhi ni kuminda ili pafupi uko akhoza kupata chakudya ni malo yogona, pakuti pano tili ni paphululu." 13 Nambho Yesu wadayangha, "Anyiimwe nde mwapache chakudya." Anyiiwo adayangha ni kumkambila, "Tili ni mabumunda yasano ni njhomba ziwilipe. Pina tipite tikaagulile chakudya chokwana wandhu wonjhewa?" 14 Wandhu yawo adali pajha, adali wachimuna ngati 5,000.
Ndiipo, Yesu wadakambila atumwi wake, "Akambileni wandhu akhale panjhi mmagulu ya wandhu amsiniamsini." 15 Atumwi khumi ni awili wajha adachita ngati umo adakambilidwa, nawonjho adakhazika wandhu wonjhe. 16 Ndiipo, Yesu wadatenga mabumunda yasano ni njhomba ziwili zijha, wadapenya kumwamba, wadamuyamika ni kumtamanda Mnungu, wadaibandhula mabumunda ni kwapacha wajha atumwi wake kuti wagawile wandhu. 17 Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. Ni atumwi adakusanya vibandhu ivo vidakhala, adavijhaza mu miseche yokwana khumi ni yawili.
18 Siku limojhi, Yesu yapo wamapembhela pamalo payokha, ni oyaluzidwa wake adali pamojhi ni iye. Wadaafunjha, "Bwanji, wandhu akamba kuti ine ni yani?" 19 Oyaluzidwa adamuyangha, "Wandhu wina akamba kuti iwe ni Yohana mbatizi, ni wina akamba kuti ni Eliya ni wina akamba kuti, iwe ni mmojhi wa alosi akale uyo wahyuka kuchokela kwa omwalila." 20 Ndiipo Yesu wadafunjha, "Ngha anyiimwe mkamba kuti ine ni yani?" Petulo wadamuyangha, "Iwe nde Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu."
21 Ndiipo Yesu wadalamula kuti asadamkambila mundhu waliyonjhe nghani zimenezo. 22 Yesu wadakambanjho, "Ifunika mwana wa Mundhu kuvutika kupunda ni kukanidwa ni azee, ni achogoleli anjhembe ni oyaluza thauko la musa, ni iye wafunika wapedwe, nambho siku la katatu, siwahyuke." 23 Ndiipo, iye wadakambila wandhu wonjhe, "Mundhu waliyonjhe uyo wafuna kunichata ine, wafunika wajhikane mwenewake ni wanichate ngati ochatila wanga siku zonjhe. 24 Pakuti waliyonjhe uyo wafuna kulamicha umoyo wake siwausoweze, nambho waliyonjhe uyo siwausoweze umoyo wake ndande ya ine, mundhu mmeneyo siwayaombole. 25 Bwanji, mundhu siwapate chiyani wakavipata vindhu vonjhe vapajhiko, nambho wauyomwecha umoyo wake? 26 Mundhu waliyonjhe uyo siwanionele njhoni ine ni mayaluzo yanga, Mwana wa Mundhu siwamuonele njhoni mundhu mmeneyo yapo siwajhe ku ulemelelo wake, ni kuulemelelo wa Atate wake ni ulemelelo wa atumiki akumwamba a Mnungu. 27 Zenedi nikukambilani, pali wina ali pano, siafa akali osauona Ufumu wa Mnungu."
28 Pambuyo pa masiku nane yapo wadamaliza kukamba yameneyo, Yesu wadaatenga Petulo, ni Yohana ni Yakobo, wadakwelanao kuphili kupembhela. 29 Yapo wamapembhela, maonekedwe ya nghope yake yadang'anamuka, vovala vake vidali voyela ni kung'azikila kupunda. 30 Mwachizulumukila, adaonekana wandhu awili niakamba nayo, wandhu achamenewo adali Musa ni Eliya, 31 yawo adaonekana ali muulemelelo, yawo amakamba ni Yesu kuusu nyifa yake iyo siichokele ku Yelusalemu. 32 Petulo ni achanjake adagona litulo lalikulu, nambho yapo adathouka, adaona ulemelelo wa Yesu ni wandhu awili yawo adaima pamojhi ni iye. 33 Basi, wandhu awili wajha yapo amasiyana ni Yesu, Petulo wadamkambila Yesu, "Bwana, siikhale bwino ngati sitikhale pamojhi! Basi, timange visakasa vitatu, chimojhi chanu, chinjake cha Musa ni china cha Eliya." Nambho Petulo siwamajhiwe icho wamachikamba.
34 Yapo Petulo wakali kukamba chimwecho, mtambo udaavinikila mwachizulumikila, nawo adaopa kupunda yapo adalowa mumtambo ujha. 35 Mvekelo udaveka kuchokela mumtambo mujha, niukamba, "Uyu ni mwana wanga uyo namsangha, mveleni iye." 36 Pambuyo pakuveka mvekelo umeneo, Yesu wadaonekana wali yokha. Oyaluzidwa wake adayasunga mmitima yawo, sadamkambile mundhu waliyonjhe yayo adayaona.
37 Siku lochatila, yapo adachika kuchokela kuphili, gulu lalikulu la wandhu lidamchata Yesu yapo wadali. 38 Yapa, mundhu mmojhi pagulu pajha wadakweza mvekelo, niwakamba, "Woyaluza, majhani mumuone mwana wanga wayokha! 39 Ndande chiwanda chimlowa, nikumchita kuti wabule pokoso ni kumchita ngati wanjilinjili, ni kumchoka matovu mkamwa. Chiwandacho kumvuticha chipunda ni sichifuna kumusiya mwachisanga. 40 Nidapembha oyaluzidwa wako kuti achichoche chiwandacho, nambho alepela." 41 Yesu wadayangha, "Anyiimwe ni mbadwa woipa ni wopande chikhulupililo, sinikhale na anyiimwe kwa ndhawi yaitali yanji kuti munikhulupilile?" Ndiipo Yesu wadamkambila mudhu yujha, "Majhanayo mwana wako pano." 42 Ata yapo mwana yujha wamajha kwa Yesu, chiwanda chidamgwecha panjhi, ni kumbula njilinjili. Nambho Yesu wadachinyindila chiwanda ni kuti chimchoke, wadamlamicha mwana yujha, ni kumbweza kwa atate wake. 43 Wandhu wonjhe adazizwa kupunda kwa ukulu wa Mnungu.
Yapo wandhu wajha adali akali kudabwa kuusu yonjhe yajha yadachitika, Yesu wadakambila oyaluzidwa wake, 44 "Vechelani bwino yaya nifuna kukukambilani chipano, Mwana wa Mundhu wapita kuikidwa panjhi pa ulamulilo wa wandhu." 45 Nambho anyiiwo sadajhiwe mate ya mawu yajha wamakamba. Chindhu ichi chidabisidwa kwa anyiiwo kuti asadajhiwa, ni naonjho adaopa kumfunjha mate ya mkambo umenewo.
46 Kudachokela kuchuchana pa oyaluzidwa kuusu yani uyo siwakhale wamkulu kupitilila wina. 47 Nambho Yesu wadayajhiwa maganizo yawo, ndipo wadamtenga mwana wamng'ono ni kumuika pafupi ni iye, 48 wadakambila, "Mundhu aliyonjhe uyo siwamulandile mwana uyu kwa jhina langa, siwakhale wanilandila ine, ni waliyonjhe uyo wanilandile ine wamlandila uyo wanituma. Pakuti iye uyo wali wamng'ono kupunda pakati panu, nde uyo wali wamkulu kupitilila wonjhe."
49 Yohana wadakamba, "Bwana, tidamuona mundhu mmojhi niwachocha viwanda kwa jhina lanu, nambho tidamkaniza, pakuti sitili pamojhi ni iye." 50 Nambho Yesu wadamkambila, "Osadamkaniza, pakuti waliyonjhe uyo siwakuchuchani, iye wali pamoji ni anyiimwe."
51 Yapo yadawandikila masiku yotengedwa kwa Yesu kupita kumwamba, iye wadafunichicha kupita ku Yelusalemu. 52 Ndiipo, wadatuma athenga kuti amchogole, ni anyiiwo adapita ku mujhi umojhi wa Samaliya, kuti amkonjele bwino kila kandhu. 53 Nambho wandhu ammujhi ujha adakana kumlandila Yesu, chifuko adajhiwa kuti wapita ku Yelusalemu. 54 Oyaluzidwa a Yesu, Yakobo ni Yohana, yapo adayaona yamanenyo, adakamba, "Ambuye, mufuna tilamule moto kuchokela kumwamba kuti uwawanange anyiyawa?" 55 Nambho Yesu wadang'anamukila ni kwakaniza. 56 Yesu pamojhi ni oyaluzidwa wake adachoka ni kupita kumujhi wina.
57 Yapo adali mnjila, mundhu mmojhi wadamkambila Yesu, "Sinikuchateni kulikonjhe uko simupite." 58 Yesu wadayangha, "Nghandwe zili ni mbhanga, ni mbalame za kumlengalenga zili ni visa, nambho mwana wa mundhu walibe pa malo pogona ni kupumulila."
59 Ndiipo, wadamkambila mundhu mwina, "Nichate." Nambho mundhu yujha wadayangha, "Ambuye, munisiye uti nipite nikaazike atate wanga." 60 Nambho Yesu wadamkambila, "Asiye wandhu akufa waazike akufa anjao, nambho iwe pita ukaulalikile Ufumu wa Mnungu."
61 Mundhu mwina wadamkambila Yesu, "Ambuye, sinikuchateni, nambho munilole uti nipite nikalaile wandhu a kukhom langa." 62 Yesu wadamkambila, "Palibe mundhu uyo wagwila khasu ni kuyamba kulima wapenyanjho mmbuyo, mundhu mmeneyo siwafunika kulowa mu Ufumu wa Mnungu."