Publicidade

Lucas 1

1 Wolemekezeka Teofilo, wandhu ambili ayesa kulemba bwino nghani za vindhu vijha vidachitika pakati pathu. 2 Adayalemba ngati umo tidafotokozeledwa ni wandhu wajha adali amboni, yawo adaziona nghani zimenezo ni maso yawo ni kuuzila uthenga. 3 Ine nane yapo nafunafuna mosamala ni kuujhiwa uzene, naona bwino kukulembelani kwa utalatibu kila kandhu olemekezeka Teofilo, nghani zimenezo ngati umo zidachitika, 4 nichita chimwecho kuti nawenjho ukhoze kuujhiwa uzene wa nghani zijha udayaluzidwa.

Kubadwa kwa Yohana m'batizi kuuzidwa

5 Pa ndhawi ya Helode mfumu wa Kuyudea, kudali mjhukulu wa Mnungu mmojhi uyo wamatanidwa Zakaliya, wochokela kugulu la anjhembe la Abiya. Nayonjho Elizabeti, mkazake Zakaliya wamachokela kukhamu la wanjhembe la Aloni. 6 Zakaliya ni mkazake Elizabeti adali wandhu yawo wovemelezeka pamaso pa Mnungu. Amakhala kochata malamulo ni thauko la Mnungu. 7 Anyiiwo adalibe wana pakuti Elizabeti wadali wambende, ni wonjhe awili adali azee kupunda.

8 Siku limojhi yapo idali zamu ya Zakaliya kuchita njhito ya njhembe Mnyumba ya Mnungu, 9 ngati umo lili khalidwe, Zakaliya wadasanghidwa kwa gudugudu, kulowa Mnyumba ya Mnungu kuti watutumuche ubani. 10 Yapo iye wamabucha ubani, wandhu ambili adali kubwalo naapembhela. 11 Ndiipo mtumiki wakumwamba wa Ambuye wadamtulukila Zakaliya mkati mmenemo, wadaima bendeka lakwene la guwa lotutumuchila ubani. 12 Yapo Zakaliya wadamuona mtumiki wakumwamba wa Ambuye, wadaopa. 13 Nambho mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamkambila, "Zakaliya Usadaopa, pakuti Mnungu wavela mapembhelo yako, ni mkazako Elizabeti siwakubalile mwana wammuna, ni iwe siumpache jhina Yohana. 14 Nawe siusekelele ni kukondwela kupunda, ni wandhu ambili sakondwele chifuko cha kubadwa kwake. 15 Ambuye samchite kukhala wamkulu, ni siwamwa divayi kapina chakumwa chilichonjhe cholojhelecha, siwajhazidwe ni Mzimu Woyela kuyambila siku lakubadwa kwake. 16 Yohana siwaabweze wandhu ambili Akuizilaeli kuti abwele kwa Ambuye Mnungu wao. 17 Ni iye siwachogolele pachogolo pa Ambuye ni siwachogozedwe ni mzimu ni mbhavu ngati za Eliya. Siwaing'anamuche mitima ya achatate kuti yaaganizile achanawao, ni kwachita osavela kuti akhale ni maganizo yabwino, ni kwaika wandhu wake tayali pakujha kwa Ambuye."

18 Zakaliya wadamfunjha mtumiki wa kumwamba wa Mnungu, "Chindhu ichi sichikhozeke bwanji? Ine ni mzee, ni mkazanga nayonjho wazeeka!" 19 Mtumiki wakumwamba wa Mnungu wadamuyangha Zakaliya, "Ine Gabilieli, mtumiki wa kumwamba wa Mnungu, uyo niima pachogolo pa Mnungu, natumidwa kuti nikambe ni iwe, ni kukukambila uthenga uwu wabwino. 20 Chipano, siukhale bubu, ndande siudavechele yayo nakukambila, siukhoza kukamba mbaka yapo siyachokele yameneyo nakukambila." 21 Ndhawi imeneyo, wandhu wonjhe amamlindilila Zakaliya, anyiiwo amadabwa ndandeyanji wachedwa mnyumba ya Mnungu. 22 Yapo Zakaliya wadatuluka kubwalo siwadakhoze kukamba. Anyiiwo adajhiwa kuti walangizidwa chindhu mkati mwa Nyumba ya Mnungu. Pakuti wadaendekela kukamba nao kwa vizindikilo, ndande siwamakhoze kukamba mawu. 23 Yapo yadatha masiku yake yochita njhito ya unjhembe, Zakaliya wadabwela kukhomo lake. 24 Pambuyo pake, mkazake wa Zakaliya uyo watanidwa Elizabeti wadali ni pathupi. Siwadachoke pakhomo pake kwa ndhawi ya miezi isano, wadakamba, 25 "Umu ndeumo anichitila Ambuye. Aniona ni kunichhitila ubwino, ni kunichochela njhoni zanga pamaso pa wandhu."

Kubadwa kwa Yesu kuuzilidwa

26 Mumwezi wa sita wa pathupi pa Elizabeti, Mnungu wadamtuma mtumiki wake Gabilieli kupita kumujhi wa Galilaya, uwo utanidwa Nazaleti, 27 wapite kwa mwalimbeta uyo wamatanidwa Maliya, uyo wadapachidwa chilipa ni wammuna uyo wamatanidwa Yusufu, wa mbadwa wa Daudi. 28 Mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamchokela ni kumlonjela ni kumkambila, "Iwe wapachidwa mwawi, Ambuye ali pamojhi ni iwe!" 29 Maliya yapo wadavela moni imeneyo wadaiganizila kupunda niwadakamba kuti moni iyi mate yake chiyani. 30 Nambho mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamkambila, "Maliya usadaopa, pakuti Mnungu wakupacha mwawi. 31 Vechela, siupate pathupi ni kubala mwana wa mmuna, niiwe siumpache jhina Yesu. 32 Iye siwakhale mundhu waulamulilo, ni siwatanidwe mwana wa Uyo wali kumwamba kupunda. Ni Ambuye Mnungu sampache ufumu ngati umo wadali Daudi, tate wake. 33 Chimwecho iye siwalamulile mbadwa wa Yakobo muyaya, ni ufumu wake siukhala ni mathelo!" 34 Maliya wadamuyangha ni kumfunjha mtumiki wa kumwamba wa Mnungu, "Sivikhozekane bwanji vindhu ivi, pakuti sinidapezane chithupi ni wammuna?" 35 Mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamuyangha Maliya, "Mzimu woyela siukujhele iwe, ni mphavu zake uyo wali kumwamba kupunda sizikuvinikile iwe ngati chitunjhi. Chimwecho, ni Woyela uyo siwabadwe siwatanidwe Mwana wa Mnungu. 36 Ata mbale wako Elizabeti uyo wamatanidwa wambende, chipano wali ni pathupi pa miyezi sita, ingakhale iye ni mzee kupunda. 37 Mate yake palibe chindhu icho sichikhozeka kwa Mnungu." 38 Maliya wadayangha, "Ine ni mbowa wa Ambuye, mawu yaya yachitike ngati umo mwakambila." Ndiipo mtumiki wa kumwamba wadachokapo.

Maliya wamuyendela Elizabeti

39 Pa masiku yamweyo, Maliya wadapita kwa msanga kujhiko la mapili la Yudeya. 40 Kumeneko Maliya wadalowa mnyumba ya Zakaliya, ni kumlonjela Elizabeti. 41 Elizabeti yapo wadavela mvekelo wa Maliya, mwana wadavina kwa chimwemwe mmimba mwake. Ni iye Elizabeti wadajhazidwa ni Mzimu Woyela. 42 Wadakweza mvekelo ni kunena, "Iwe wapachidwa mwawi kupunda ni Mnungu kupitilila wachikazi wonjhe, ni wali ni mwawi mwana uyo siubale! 43 Ndande yanji chindhu ichi chinichokele ine, mbaka maye wa Ambuye wanga aniyendele ine? 44 Yapo nidavelape moni yanu, mwana uyo wali mmimba wadavina kwa chimwemwe. 45 Uli ni mwawi iwe wakhulupilila kuti siyachitike yameneyo Ambuye akukambila!"

Maliya waimba kumkweza Mnungu

46 Maliya wadakamba,

"Mtima wanga umkweza Ambuye,

47 ni mtima wanga ukondwela ndande ya Mnungu Muomboli wanga.

48 Pakuti Mnungu wanikumbukila kwa lisungu ine mbowa wake wojhichicha. Kuyambila chipano mibadwa yonjhe siinitane wamwawi.

49 Pakuti Mnungu wambhavu zonjhe wanichitila vavikulu,

jhina lake ni woyela.

50 Lisungu lake kwa anyiyawo amulemekeza kupunda

ni lolimba kwa mibadwa ni mibadwa.

51 iye wachita vindhu vavikulu kwa mbhavu zake,

wayamwaza maganizo ya wandhu ambwinya yayo yali mmitima yawo,

52 iye waachicha alamuli kuchokela mmipando yawo ya chifumu,

nambho waakweza yawo ajhichicha.

53 Anjala wakhuticha vindhu vabwino,

ni wandhu wopata watopola manja yachajhe.

54 Iye wamthangatila Izilaeli mbowa wake,

ni wakumbukila ahadi yake yomlengela lisungu,

55 ngati umo wadakambila kwa anyambuyathu,

Ibulahimu ni mibadwa yake yonjhe muyaya."

56 Maliya wadakhala ni Elizabeti kwa miyezi itatu, ni pambuyo pake wadabwela kukhomo lake.

Kubadwa kwa Yohana mbatizi

57 Ndhawi yobala yapo idakwana Elizabeti wadabala mwana wammuna. 58 Wandhu apafupi ni achabale wake adavela kuti Ambuye alangiza lisungu lalikulu, adakondwela pamojhi ni iye.

59 Yapo lidakwana siku la nane kuyambila kubadwa kwa mwana, adapita kumdula jhando, ni achabale wake amafuna kumpacha jhina la atate wake ilo limatanidwa, Zakaliya. 60 Nambho amake adakana, ni kukamba, "Notho! Watanidwe jhina Yohana." 61 Anyiiwo adamuyangha, "Palibe mundhu ata mmojhi pa khamu lako uyo wali ni jhina limenelo." 62 Ndiipo anyiiwo adaafunjha atate wake kwa vizindikilo kuti wakambe jhina ilo wafuna kumpacha mwana wake. 63 Iye wadatanicha chithabwa ni wadalemba chimwechi, "Jhina lake ni Yohana." Wandhu wonjhe adazizwa. 64 Ndhawi imweyo Zakaliya wadakhoza kukamba ni kumtamanda Mnungu. 65 Wandhu apafupi wao wonjhe adadabwa kupunda, mbaka nghani zijha zidafika jhiko lonjhe la mapili ya Kuyuda. 66 Wandhu wonjhe yawo adavela nghani zimenezo adadabwa kupunda ni kujhifunjha, "Bwanji, mwana mmeneyo siwakhale wamtundu wanji?" Mate yake, zenedi mbhavu za Mnungu zidali pamojhi ni iye.

Ulosi wa Zakaliya

67 Ndiipo Zakaliya, tate wa Yohana wadajhazidwa ni Mzimu Woyela, ni wadakamba ulosi,

68 "Akwezedwe Ambuye Mnungu aku Izilaeli,

pakuti wajha kwaombola wandhu wake.

69 Iye watipacha muomboli wambhavu,

Wochokela mbadwa wa Daudi mbowa wake.

70 Ngati umo Mnungu wadakamba kuyambila kale,

kupitila alosi wake woyela,

71 kuti siwatilamiche ife kuchokela kwa adani

ni kuchokela mmanja mwa wandhu yawo atiipila ife.

72 Wadakamba kuti siwachitile ubwino achambuyathu,

ni kukumbukila chipangano chake choyela.

73 Ngati umo wadamuahidi tate wathu Ibulahimu kwa kulumbila,

kuti siwatipache ife mwawi,

74 Siwatichoche ife mmanja mwa adani wathu,

watikhozeche kumtumikila iye popande mandha,

75 moyela ni kuvomelezeka pamaso pa Mnungu,

masiku yonjhe ya umoyo wathu.

76 Ni iwe mwana wanga siutanidwe mlosi wa uyo wali kumwamba kupunda.

siwachogolele Ambuye kwakonjela njila yao,

77 ni siwauzile wandhu wao kuti sialamichidwe

kwa njila ya kwalekelela machimo yao.

78 Ndande ya lisungu ni upole wa Mnungu wathu,

ni dangalila la kulamicha kwake sikutiwalile kuchokela kumwamba,

79 kuti lamulikile wandhu wojhe yawo akhala kumdima waukukulu wa nyifa,

nikutichogoza munjila ya mtendele."

80 Mwana yujha wadakula ni kujhala mbhavu muuzimu. Wadakhala mphululu mbaka yapo wadajhilangiza kwa wandhu ku Izilaeli.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-