1 Pambuyo pa yameneyo, Ambuye wadasangha wandhu wina sabini ni awili. Ni wadatuma wandhu awiliawili kuti amchogolele kila mujhi ni kila malo yayo iye wamufuna kupita. 2 Wadakambila, "Vokolola ni vochuluka, nambho wokolola ni ochepa. Basi, mpembheni Ambuye avokolola kuti wapeleke wokolola mmunda mwake. 3 Chipano, mapitani! Jhiwani kuti, ine nikutumani ngati mbelele iyo ipita pakatikati pa mibinji. 4 Msadatenga chikwama kapena thumba, kapina vilatu vong'anamulila ni simdamlonjela mundhu waliyonjhe nimpita mnjila. 5 Yapo simulowe mnyumba iliyonjhe, poyamba alonjeleni chimwechi, ‘Mtendele wa Ambuye ukhale mkati mwa nyumba iyi.’ 6 Ngati mnyumbamo muli mudhu uyo wakonda mtendele, basi mtendele wanu siukhale ni iye. Nambho ngati palibe uyo wakonda mtendele, mtendele wanu siukubweleleni mwachinawene. 7 Khalani mnyumba imeneyo ni kudya ni kumwa ivo sakupacheni, chifuko kila uyo wapota njhito wafunika kulandila mkokolo wake. Msadasamukasamuka kuchoka mnyumba imojhi ni kupita mnyumba ina. 8 Ngati mkalowa mmujhi ni kulandilidwa, idyani vakudya ivo viikidwa pachogolo panu. 9 Alamicheni wodwala yawo ali kumeneko ni kwakambila, ‘Ufumu wa Mnungu wawandikila kwa anyiimwe.’ 10 Nambho yapo mulowa mu mujhi ulionjhe, ni wandhu ngati sakulandilani, chokani. Ni anyiimwe yapo mujhipita mmikwakwa yawo, mkambe, 11 ‘Ata lifumbi la mmujhi wanu ilo lakanilila ni mmapazi yathu, sitikukung'undhileni. Nambho mujhiwe kuti Ufumu wa Mngungu wawandikila!’ 12 Zenedi nikuchimikizilani, pasiku la lamulo, wandhu amujhi umenewo sakhale ni mavuto yayakulu kupitilila ya wandhu amujhi wa Sodoma."
13 "Simvutike anyiimwe mkhala ku kumijhi wa Kolazini! Simvutike anyiimwe mkhala kumijhi ya Betisaida! Pakuti, vodabwicha izo zachitika kwanu zidakakhala kuti zachitika ku mijhi ya Tilo ni Sidoni, wandhu wake adakakhala pavyoso ni kujhitila vyoso mmuthu mwao kulangiza kuti alapa 14 Nambho siku la lamulo, nambho siku la lamulo sikhale lahisi kulimba mtima kwa mujhi wa Tilo ni Sidoni kupitilila anyiimwe. 15 Ni imwe wandhu a uku Kapenaumu, uganiza kuti siujhikweze mbaka kumwamba? Notho! Nambho siuchichidwe mbaka kumalo kwa wandhu amwalila."
16 Ndiipo Yesu wadakambanjho oyaluzidwa wake, "Mundhu waliyonjhe uyo wakuvelani nikukuvelani anyiimwe, wanivela ine. Ni uyo wakana wakulandilani anyiimwe wakana kunilandila ine. Ni waliyonjhe uyo wakana kunilandila ine, wakana kumlandila yuja wanituma."
17 Pambuyo, anyiwajha sabiini ni awili adabwela uku ajala chimwemwe, ni kukamba, "Ambuye, ingakhale tikavilamula viwanda vitivela kwa mbhavu zanu." 18 Yesu wadayangha, "Nidamuona Satana niwagwa kuchoka kumwamba ngati viweyuweyu va mbhambe. 19 Yesu wadakambila ochatila wake kuti, Nikupachani ulamulilo wakuponda njoka ni chipilili ni mbhavu za adani wonjhe, sipakhalapo chindhu chilichonjhe icho sichikupwetekeni. 20 Nambho ata chimwecho, msadakondwela ndande viwanda vakuvelani, nambho kondwelani kuti maina yanu yalembedwa kumwamba."
21 Ndhawi imweijha, Yesu wali wojhala Mzimu Woyela, wadakondwa, wadakamba, "Nikuyamikani imwe Atate, Ambuye wa kumwamba ni jhiko la panjhi, pakuti mwabisa vindhu ivi wandhu wozindikila ni anjelu, nambho mwavumbulila wana wang'onang'ono. Yetu Atate, umu nde umo mwakondela."
22 Ndiipo wadakamba, "Atate wanga anikozecha kuchita chindhu vonjhe. Palibe uyo wamjhiwa mwana nambho Atate, ni palibe uyo wajhiwa Atate nambho Mwana, ni yunjha waliyonjhe mwana wafuna kumvumbulila."
23 Ndiipo Yesu wadang'anamukila oyaluzidwa wake ni kwakambila, "Muli ni mwawi anyiimwe muona! 24 Zenedi nikukambilani, alosi ni mafumu adakumbila kuyaona yayo muyaona, namposadayaone, ni adakumbila kuyavela yayo muyavela, nambho sadayavele."
25 Pambuyo mundhu mmojhi woyaluza thauko wadaima kuti wamuyese Yesu, wadamfunjha, "Oyaluza, nichite chiyani kuti nikhale ni umoyo wamuyaya?" 26 Yesu wadamuyangha, "Uzindikila chiyani yapo usoma mmalembo ya thauko la Musa? Uyazindikila bwanji malembo yameneyo?" 27 Mundhu yujha wadamuyangha Yesu, "Mkonde Ambuye Mnungu wako kwa mtima wako wonjhe, ni kwa umoyo wako wonjhe, ni kwa mbhavu zako zonjhe ni kwa njelu zako zonjhe ni, ‘Umkonde njako ngati umo ujhikondela umwene.’ " 28 Yesu wadamkambila kuti, "Wayangha bwino. Chita chimwecho kuti ukhale ni umoyo."
29 Nambho mundhu woyaluza thauko yujha wamafuna kujhilangiza kuti iye ni wozindikila pamaso pa Mnungu, wadamfunjha Yesu, "Mundhu wapafupi wanga ni yani?" 30 Yesu wadayangha, "Mundhu mmojhi wamachokela ku Yelusalemu kupita ku Yeliko. Yapo wadali panjila wadaphezana ni achifwamba, adamvula njhalu, adammenya, adachoka ni kumusiya pamwepo wali pafupi kumwalila. 31 Kwa mwayi, mjhukulu wa Mnungu mmojhi wadali kupita njila imweijha. Yapo wadamuona mundhu yujha, wadampita kumbhepete. 32 Chimwecho, mthandizi wamjhukulu wa Mnungu mmojhi nayo wadafika pamalo pajha, wadamuona nayo wadampita kumbhepete ni kuchoka. 33 Nambho mundhu mmojhi wa jhiko la Asamaliya yapo wadali paulendo, wadafika yapo wadali mundhu yujha, niiye yapo wadamuona wadamulengela lisungu. 34 Ndiipo wadafika pafupi, wadavichuka vilonda vake kwa divai ni kumnyeka mafuta ni kuvimanga. Yapo wadamaliza kuchita chimwecho, wadamkweza pa chinyama chake ni kupita nayo kunyumba ya alendo kumdwaza. 35 Umawa wake, wadatenga vibandhu viwili va miyala yaphindu kupunda nikumpacha yujha mwene nyumba ya alendo, nikukamba, ‘Mdwaze mundhu uyu, ni chalichonjhe icho sichiongezeke sinijhe kubwezela nikabwela.’" 36 Ndiipo Yesu wadamfunjha, "Yani pakati pa wandhu atatuwa uyo wadalangiza kuti ni mundhu wapafupi wa yujha wahundukilidwa ni achifwamba?" 37 Yujha woyaluza thauko wadayangha, "Uyo wadamlengela lisungu nde mnjake wake." Yesu wadamkambila, "Nawenjho upite ukachite chimwecho."
38 Yapo Yesu ni oyaluzidwa wake adali paulendo, adafika mumujhi umojhi, uwo wamakhala wamkazi mmojhi uyo wamatanidwa Masa, wadamlandila kukhomo kwake. 39 Masa wadali ni mwali mnjake uyo wamatanidwa Maliya, mmeneyo wadakhala pafupi ni mmiyendo mwa Yesu kuvechela mayaluzo yake. 40 Nambho Masa wamachauchika ni njhito zambili. Ndiipo wadamchata Yesu ni kumkambila, "Ambuye, bwanji simuona kuti mbale wanga wanisiila nichite njhito zonjhe nekha? Mkambileni wakanithangatile." 41 Nambho Ambuye adamuyangha, "Masa, Masa, ujhichaucha ni vindhu vambili, 42 ni chindhu chimojhipe icho chili chabwino icho Maliya wachisangha, ni balibe mundhu uyo siwamulande."