Publicidade

Lucas 19

Yesu ni Zakayo

1 Yesu wadapita kumujhi wa ku Yeliko, nayo wamapitapita mmikwakwa ya mmujhi umeneo. 2 Padali ni mundhu mmojhi mmujhi mmenemo wamatanidwa Zakayo. Mmeneyo wadali wamkulu wa wandhu wolandila malipilo ni wadali ni chuma chambili. 3 Iye wamafuna wamuone Yesu kuti ni mundhu wamtundu wanji, nambho wadalepela kumuona ndande iye wadali wamfupi, ni wandhu adachuluka. 4 Chimwecho, wadathamangila mchogolo, wadakwela mumtengo wa mkuyu kuti wakhoze kumuona Yesu, pakuti wamajhiwa Yesu wamapita mnjila imeneyo. 5 Yesu yapo wadafika pamalo yameneyo, wadapenya mmwamba mwa mtengo ni kumkambila, "Zakayo, chika chisanga, pakuti lelo sinikhale mlendo kukhomo lako." 6 Zakayo wadachika chisanga ni kumlandila Yesu kwa kukondwela. 7 Wandhu wonjhe yapo adaona yameneyo adayamba kudandaula ni kukamba, "Wapita kukhala mlendo wa mundhu wa machimo."

8 Nambho Zakayo wadaima ni kwaakambila Ambuye, "Vechelani Ambuye! Ine sinaninghe wosauka chuma changa chakumojhi, ningati namlanda mundhu chindhu chalichonjhe, sinimbwezele kanayi."

9 Yesu wadamkambila, "Lelo uomboli wajha mnyumba ino, pakuti uyu nayo ni wa mwana wa mmuna wa Ibulahimu. 10 Pakuti ine mwana wa Mundhu najha kufunafuna ni kulamicha chijha chidataika."

Chifani cha mbowa khumi

11 Wandhu yapo amavechela Yesu, amaganiza kuti Ufumu wa kumwamba ulipafupi kuchokela. Ndande adali pafupi kufika mmujhi wa ku Yelusalemu. Ndiipo Yesu wadakambila chifani, 12 Yesu wadakamba, "Padali ni mundhu mmojhi wa khamu la chifumu, wadapita kujhiko lakutali kuti wakalandile ulamulilo wokhala mfumu, ni pambuyo pake wabwele ni ulamulilo. 13 Nambho, wakali osachoke, wadatana mbowa zake khumi ni kumpacha kila mmojhi gawo la ndalama ni kwakambila, ‘Mchitile malonda ndalamazi mbaka yapo sinibwele.’ 14 Nambho wandhu ammujhi umenewo adamuipila ni adaatuma athenga kuti apite akamkambile, ‘Sitifuna mundhu mmeneyo wakhale mfumu wathu.’ "

15 "Ata chimecho mundhu mmeneyo wadapachidwa ulamulilo ni kubwela kukhomo kukhala mfumu. Ndiipo wadaatana wajha mbowa wake wadaapacha ndalama, kuti wajhiwe phindu ilo apata kila mmojhi. 16 Mbowa woyamba wadafika ni kukamba, ‘Ambuye, kwa fungu lijha mudanipacha napata mafungu khumi kuchokana ni ndalama zijha mdanipacha.’ 17 Mbuye yujha wadamkambila, ‘Wachitabwino, pakuti wakhala mbowa wokhulupilika pa vindhu vochepa, nikuningha ulamulilo wa mijhi khumi.’ 18 Mbowa wakawili wadafika ni wadakamba, ‘Mbuye, napata mafungo ya sano kuchoka mu fungo limojhi ilo mudanipacha.’ 19 Nayo wadamkambila, ‘Niiwe nikuningha ulamulile mijhi isano.’ 20 Mbowa mwina wadafika ni kukamba, ‘Bwana, ndalama yanu iyo mudanipacha iyi yapa. Nidaisunga bwino kupunda mu chitambaya. 21 Ndande yake nimaopa pakuti imwe ni mundhu uyo siufuna kuchefyedwa, utenga ivo osati vako, ni kucha yapo siudavyale.’ 22 Bwana wake wadamuyangha, ‘Iwe ni mbowa woipa, nikulamula kuchokana ni umo wakambila! Ngati udajhiwa kuti ine ni mundhu woipa, uyo nitenga ndalama za wandhu wina izo osati zanga, ni kuvuna vakudya ivo sinidavyale, 23 chipano ndande yanji siudawapache ndalama wandhu wochocha liba kuti nikabwela nitenge ndalama zanga pamojhi ni phindu?’ 24 Chimwecho wadakambila anyiwajha adaima pafupi, ‘Mlandeni ndalamazo mkampache uyo wali ni mafungo khumi.’ 25 Na anyiiwo adamkambila, ‘Nambho bwana, mmeneyo wali nayo mafungo khumi!’ 26 Iye wadayangha, ‘Nikukambilani kuti kila uyo wali ni kandhu, siwaongezeledwe. Nambho kwa uyo walibe kandhu, ata chochepa icho walinacho, siwalandidwe. 27 Nambho, anyiwajha adani wangawa, yawo siadafune nikhale mfumu, mjhenao pano kuti niwaphe pamaso panga.’ "

Yesu walowa mu Yelusalemu kwa chikondwelo

28 Yesu yapo wadamaliza kukamba chimwechio, wadachogolela kupita ku Yelusalemu. 29 Yapo wadawandikila ku mijhi ya Besifage ni Besania, pafupi ni phili ilo litanidwa phili la Mizetuni, wadatuma woyaluzidwa wake awili pakati pa oyaluzidwa wake, wadakambila, 30 "Mpite mmujhi uwo uli mchogolo mwanu. Yapo simulowe mmenemo, simumpheze phunda uyo siwadatumike ni mundhu waliyonjhe, wamangidwa mmasuleni mjhe nayo pano. 31 Mundhu uyo siwakufunjheni ndande yanji mummasula phunda, mkambileni, amfuna Ambuye."

32 Ndiipo adapita ni adakomana ngati umo adakambilidwa ni Yesu. 33 Yapo amammasula phunda yujha, mwene phunda wadaafunjha, "Ndande yanji mummasula phunda?" 34 Anyiiwo adayangha, "Ambuye amfuna." 35 Ndiipo, adampeleka kwa Yesu phunda yujha. Adayala njhalu pamwamba phunda ni kumkweza Yesu pamwamba pake. 36 Yapo wamaendekela ni ulendo, wandhu adayala njhalu zao panjila.

37 Yapo wadawandikila ku Yelusalemu, pa njila iyo ichikila pa phili la mizeituni, gulu lonjhe la wochatila wake adayamba kukondwela ni kumtamanda Mnungu pokweza mvekelo ndande ya vodabwicha vonjhe ivo adavionapo. 38 Adakamba, "Wali ni mwawi Mfumu uyo wakujha mu jhina la Ambuye. Mtendele ukhale kumwamba kwa Mnungu, ni ulemelelo kumeneko kumwamba kupunda!" 39 Afalisayo wina yawo adali mkati mwa gulu lijha, yapo adaona chimwecho, adamkambila Yesu, "Oyaluza, anyindileni oyaluzidwa wanu akhale chete!" 40 Yesu wadayangha, "Nikukambilani kuti, ngati anyiyawa saakhale chete, miyala siibule phokoso."

Yesu waulilila mujhi wa Yelusalemu

41 Yesu yapo wadawandikila ni kuuona mujhi wa Yelusalemu, wadaulilila, 42 wadakamba, "Idakakhala bwino ngati udakajhiwa lelo vindhu ivo vipeleka mtendele kwako! Nambho chipano yabisika pamaso pako. 43 Masiku yatokujha, yapo adani wako sakuzungulile ni kukuhundukila madela yonjhe. 44 Ndiipo Sakugweche panjhi iwe pamojhi ni wandhu wako onjhe. Siakusiila ata mwala uwo siukhalile pamwamba pa wina ndande siumafune kujhiwa ndhawi iyo Mnungu wakupelekela uwomboli."

Yesu mu nyumba ya Mnungu

45 Ndiipo, Yesu wadalowa mkati mwa malo ya nyumba ya Mnungu ni kuyamba kwaatopola wandhu wajha amachita malonda mmenemo, 46 wadakamba, "Yalembedwa, ‘Nyumba yanga siikhalae nyumba ya mapembhelo, nambho anyiimwe mwaichita kukhala mbhanga ya anghungu.’ "

47 Yesu wamatoyaluza mu nyumba ya mapembhelo siku ni siku. Nambho achogoleli, wakulu akulu wa ajhukulu ni oyaluza a mathauko, amafunafuna njila yakumupha Yesu, 48 Nambho sadapate njila ya kumgwila, ndande wandhu wonjhe amamvechecha.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-