1 Yesu yapo wadapenyechecha, wadaona wandhu wopata naathila njhembe zawo mu bokosi lo sungila ndalama za nyumba ya Mnungu, 2 wadamuonanjho maye mmojhi wosauka uyo wafedwa ni mmunake niwathila senti ziwili mbokosi mujha. 3 Yesu wadakamba, "Zenedi nikukambilani, maye wosaukayu uyo wafedwa ni mmunake, wathila njhembe yochuluka kupitilila wandhu wonjhewa. 4 Pakuti wandhu wina amchochela njhembe Mnungu kuchokana ni kuchuluka kwa chuma chao, nambho maye wofedwa wammuna wachocha kuchokana ni kusauka kwake vonjhe va kumthangatila pa umoyo wake."
5 Woyaluzidwa wina a Yesu amakamba kuusu ni miyala yabwino iyo idakwadilicha Nyumba ya Mnungu ni njhembe izo wandhu amamchochela Mnungu. Nambho Yesu wadaakambila, 6 "Yonjhe yaya muyaona yapa, masiku siyafike, palibe mwala uwo siukhalile pamwamba pa unjake, ndande yonjhe siyagomeledwe ni kutaidwa panjhi."
7 Oyaluzidwa wake adamfunjha, "Oyaluza mtikambile, sivichokele chakanji vindhu vimenevi, ni vizindikilo vanji sivilangize kuti vindhu vimenevo sivichitike?"
8 Yesu wadayangha, "Chenjelani, kuti musadanyengedwa. Pakuti wandhu ambili siajhe naajhichita kuti anyiiwo nde ine, naakamba, ‘Ine nde Kilisito,’ kapina, ‘Nyengo ya yameneyo ili pafupi.’ Nambho anyiimwe simdaachata. 9 Nambho yapo simuvele nghani za nghondo ni kupanduka kwa wandhu, musadaopa ndande yameneyo yafunika yachokele poyamba, nambho mathelo siyachokela nyengo imeneyo."
10 Ndiipo Yesu wadayendekela wadakambila, "Wandhu ajhiko limojhi sabulane ni wandhu ajhiko linjake, ni ufumu umojhi siubulane ni ufumu unjake. 11 Sikukhale ni chimtingiza cha chikulu cha ndhaka, ni njala yaikulu ni matenda yoofya kila kumalo. Sikuchokele vindhu voofya ni vizindikilo vavikulu kuchokela kumwamba. 12 Nambho yakali osachokele yameyo, sakugwileni ni kukuvutichani ni sakupelekeni mmnyumba za mapembhelo ni kukuikani mundende. Simupelekedwe pachogolo pa mafumu ni amaulamulilo ndande ya kunichata ine, 13 nambho kwa anyiimwe imeneyo nde siikhale nyengo yo lalikila Uthenga wabwino kwa anyiiwo. 14 Nambho msakhala ni mandha kuti simukambe chiyani kuti mujhipulumuche, 15 Pakuti ine sinikupacheni mawu pamojhi ni njelu, palibe uyu siwakhoze kulimbana ni anyiimwe kapina kukuchuchani. 16 Obala wanu, achabale, achanjanu ni abwenji wanu sakung'anamukeni, ni wina pakati panu saphedwe. 17 Simuipilidwe ni wandhu wonjhe ndande ya kunichata ine. 18 Nambho, simpata chiwonongeko chalichonjhe icho sichikhale muyaya. 19 Nambho uyo siwalimbe mtima mbaka pothela siwakhale ni umoyo wa muyaya."
20 "Yapo simuone kuti mujhi wa Yelusalemu wazungululidwa ni asikali, jhiwani kuti masiku ya kughomoledwa kwake yawandikila. 21 Ndhawi imeneyo yawo ali ku Yudea athawile kuphili, ni yawo ali mmujhi wa Yelusalemu achoke kubwalo, ni yawo ali kumunda sadalowa mmujhi umenewo. 22 Ndande, masiku yameneyo siyakhale, ‘Masiku ya Chilango,’ dala kukwanilicha yonjhe yalembedwa Mmalembo Yoyela. 23 Savutike kupunda yawo ali ni pathupi ni yawo ayamwicha pamasiku yameneyo! Ndande sikukhale mavuto yayakulu mjhiko ni mbhwayi ya Mnungu siikhale kwa wandhu amjhiko ili la Yudea. 24 Wandhu wina siaphedwe kwa upanga, wina satengedwe ngati omangidwa ni kupelekedwa mmaiko yina. Ni mujhi wa Yelusalemu siulamulidwe ni wandhu osati Ayahudi, mbaka masiku yao yolamula yapo siyakwane."
25 "Sikukhale ni vizindikilo kujhuwa, kumwezi ni ndhondwa. Wandhu ajhiko lapanjhi saalage kupunda ni saakhale ni mandha yapo savele mtungulu ni kuyamila kwa mafunde ya nyanja yamchele. 26 Wandhu saakomoke kwa mandha yayakulu, poona vindhu ivo sivionekane pajhiko. Pakuti vindhu vonjhe va mbhavu za kumwamba sivitingizike. 27 Ndhawi imeneyo sianione ine Mwana wa Mundhu ninijha mmitambo, najhala mbhavu ni ulemelelo wochuluka. 28 Vindhu ivi yapo siviyambe kuchokela, mdaime nganganga nimkweza mitu yanu kumwamba, pakuti uomboli wanu wawandikila."
29 Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake mfano uwu, "Ganizilani mtengo wa mkuyu ni mitengo ina yonjhe. 30 Yapo uyamba kuphukila machamba, mwachinawenewake mjhiwa kuti nyengo ya mwavu yakwana. 31 Chinchijha, yapo simuone vindhu vimenevo nivichokela, mujhiwe kuti Ufumu wa Mnungu wawandikila."
32 "Kukambilani, ambadwa uwo siuvione vindhu ivi siutha mbaka yapo vindhu ivi yapo sivichokele. 33 Kumwamba ni jhiko lapanjhi sivipite, nambho mawu yanga siyapita ata pang'ono."
34 "Mchenjele, mitima yanu siidalemeledwa ni ludyo ni kulojhela ni kulaga ndande ya umoyo uno, dala siku lijha silidakuphezani anyiimwe mwachizulumukila. 35 Pakuti siku limenelo silaafikile wandhu wonjhe yao akhala pajhiko lonjhe lapanjhi. 36 Mchezelele ni kupemphela nyengo zonjhe kuti mpheze mbhavu za kupulumuka yonjhe yayo siyachokele, kuti mukhoze kuima pamaso pa Mwana wa Mundhu."
37 Yesu wadali kuyaluza wandhu mnyumba ya Mnungu ndhawi zonjhe za usana, kila ujhulo wamapita kuphili la Mizeituni ni kukhala kumeneko usiku njenjenje. 38 Wandhu wonjhe amalawila umawamawa ni kupita ku Nyumba ya Mnungu kumvechela Yesu.