1 Yesu wadachoka mumchinje Yolodani uku wajhazidwa ni Mzimu Woyela, ni wadachogozedwa ni Mzimu Woyela mbaka ku phululu. 2 Yapo wadali kuphululu, Yesu wadayesedwa ni Satana kwa masiku alobaini. Ndhawi imeneyo yonjhe iye siwadadye kandhu, pambuyo pake wadavela njala. 3 Ndiipo Satana wadamkambila, "Ngati iwe ni mwana wa Mnungu, ng'anamula mwala uu ukhale bumunda." 4 Yesu wadamuyangha, "Yalembedwa mumalembo ya Mnungu, ‘Mundhu siwangakhale ni umoyo kwa kudya bumundape.’ "
5 Ndiipo Satana wadamtenga Yesu mbaka pamwamba ni kumalangiza kwa pamojhi maufumu yonjhe ya jhiko lapanjhi. 6 Satana wadamkambila Yesu, "Sinikupache mauufumu yaya yonjhe ni maufulu yake, pakuti napachidwa vindhu vonjhe, ni ine nikhoza kumpacha uyo nifuna ine kumpacha. 7 Chipano, vindhu vonjhevi sinikupache ni kukhala vako ngati siunigwadile ni kunilambila." 8 Yesu wadamuyangha Satana, "Yalembedwa,
‘Mgwadile Ambuye Mnungu wako,
ni kumtumikila iye yokha!’"
9 Satana wadamtenga Yesu mbaka ku Yelusalemu, wadamuika pa mnala wa Nyumba ya Mnungu ni kumkambila, "Ngati iwe ni mwana wa Mnungu, jhiponye panjhi kuchoka pano, 10 pakuti yalembedwa,
‘Mnungu siwatume atumiki wake akumwamba akudake,’
11 Yalembedwanjho,
‘Sakunyamule mmanja mwao,
kuti usadajhikhowala miyala mmyendo mwako.’" 12 Nambho Yesu wadamyangha, "Yalembedwanjho, ‘Usadamuyesa Ambuye Mnungu wako.’ " 13 Yapo Satana wadamaliza kumuyesa kwa njila zambili, wadamusiya Yesu mbaka yapo ndhawi siikwane.
14 Ndiipo, Yesu wadabwelela ku Galilaya wajhazidwa ni mbhavu za Mzimu Woyela, ni nghani zake zidaenela ku Galilaya ni mijhi yonjhe ya pafupi. 15 Nayo Yesu wamayaluza wandhu mnyumba za mapembhelo za Ayahudi, ni wandhu wonjhe amamtamanda iye.
16 Basi, Yesu wadapita ku Nazaleti kumujhi uwo wadakulila, ni Siku lo Pumulila ilo limatanidwa Sabato wadalowa mnyumba ya mapembhelo ya Ayahudi ngati umo chidali chikalidwe chake. Wadaima dala wasome. 17 Adampacha chikalakala cha mlosi Isaya, wadachivunukula, ni wadasoma pamalo yapo palembedwa,
18 "Mzimu wa Ambuye uli mkati mwanga,
pakuti wanisangha
kwaakambila wosauka uthenga wabwino.
Anituma kuti nauzile wandhu womangidwa ufulu wao,
ni wosapenya akhoze kuonanjho,
ni kwaapacha ufulu yawo aoneledwa.
19 Ni kuuzila chaka cha Ambuye icho chavomelezedwa."
20 Yapo wadamaliza kusoma chikalakala, wadachivinikila, ni wadampacha mbowa ni kukhala panjhi. Wandhu wonjhe yawo adali mnyumba ya mapembhelo, adampenyechecha. 21 Iye wadakambila, "Lelo malembo yaya yakwanila yapo mwanivela niniyasoma." 22 Wandhu wonjhe adamvechela mawu yake yabwino yayo wadakamba adadabwa. Adafunjhana, "Bwanji, uyu osati mwana wa Yusufu."
23 Yesu wadakambila, "Nijhiwa kuti simunikambile mkambo uwu, ‘Sing'anga, ujhilamiche umwene.’ Ni simukambenjho, ‘Yonjhe yayo tidavela wayachita ku Kapelinaumu kujha, uyachitenjho ni pano pamujhi wako.’ " 24 Wadaendekela kukamba, "Nikukambilani, palibe mlosi uyo wavomelezedwa mjhiko lake. 25 Nambho vechelani! Kudali ni wachikazi yawo afedwa naachamunawo mmujhi wa Izilaeli pa nyengo ya Eliya. Ndhawi imeneyo, vula idachekelezedwa siidanya kwa vyaka vitatu ni miyezi sita, ni kudali ni njala yaikulu mujhiko lonjhe. 26 Ata chimwecho, Eliya siwadatumidwe kwa wamkazi waliyonjhe uyo wafedwa ni mmunake, nambho kwa wamkazi yujha wafedwa ni mmunake, wa ku mujhi wa Selepta, mjhiko la Sidoni. 27 Naponjho kudali wandhu ambili avizunguluta mujhiko la Izilaeli nyengo za mlosi Elisha. Ndiipo padalibe mundhu uyo wadalamichidwa, nambho Naamani yokha wa kumujhi wa Siliya." 28 Wandhu wonjhe yawo adali mnyumba ya mapembhelo ya Ayahudi, yapo adavela chimwecho adakwiya kupunda. 29 Adaima adamgwila ni kumguguzila kubwalo kwa mujhi wao uwo udamangidwa pamwamba pa phili, ni kumpeleka mmbhepete mwa phili lijha kuti amponye panjhi pa ghombe. 30 Nambho Yesu wadapita ni waenda pakatikati pao.
31 Ndiipo Yesu wadachika ku Kapelinaumu, mmujhi wa Galilaya, ni Siku lo Pumulila wadayamba kwayaluza wandhu. 32 Wadazizwicha wandhu kupunda kwa mayaluzo yake, pakuti wamayeluza kwa ulamulilo. 33 Mkati mwa nyumba ijha apezana Ayahudi mudali mundhu uyo wazamwa ni viwanda, wadabula pokhoso lalikulu, niwakamba, 34 "Ufuna kutichita chiyani Yesu wa ku Nazaleti! Bwanji, wajha kuno kuti utiyomweche? Nikujhiwa kuti iwe ni yani. Iwe ni Woyela wa Mnungu." 35 Ndiipo Yesu wadachinyindila chijha chiwanda, wadakamba, "Khala chete! Mchoke mundhu uyu!" Ndiipo chiwanda chijha chidamgwecha panjhi mundhu mmeneyo pamaso pao wonjhe, ni kumchoka popande kumpweteka. 36 Wandhu wonjhe adazizwa ni adakambilana, "Ili ni yaluzo la mtundu wanji? Mundhu uyu wali ni ulamulilo ni mbhavu za kuvikambila viwanda vimchoke, navo vimchoka!" 37 Nghani za Yesu zidaenela madela yonjhe yozungulila malo yajha.
38 Yesu wadachoka mnyumba yokomana Ayahudi ni kupita ku kukhomo kwa Simoni. Apongozi wake wakazi a Simoni amadwala matenda yayakulu kupunda, nianyiiwo adampembha Yesu wamulamiche maeyo. 39 Iye Yesu wampitila mae yujha wadamkwatamila wamkazi yujha ni kuulamula utenda kuti umusiye, ni ujha utenda udamsiya. Ndhawi imweyo wadauka ni kuyamba kwatumikila alendo.
40 Ni jhuwa yapo limabila, wandhu wonjhe yao adali ni matenda yosiyanasiyana adajhanao kwa Yesu, ni iye wadaika manja yake kwa kila odwala, ni wadalamicha. 41 Viwanda vidaachoka wandhu ambili, vidachita pokoso ni kukamba, "Iwe ni Mwana Wa Mnungu!" Nambho Yesu wadavinyindila ni kuvikaniza kukamba, pakuti vidamujhiwa kuti iye ni Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu.
42 Umawamawa, Yesu wadapita kumalo yobisika. Wandhu amamfunafuna, ni yapo adafika malo yayo wadali, adayesa kumchekeleza siwadachoka. 43 Nambho Yesu wadaakambila, "Nifunikanjho niwauzile wandhu Uthenga wabwino wa ufumu wa Mnungu kumijhi yinanjho, pakuti natumidwa ni Mnungu kuti nichite chimenecho." 44 Chimwecho wadaendekela kulalikila wandhu uthenga wa Mnungu mnyumba zopezanilana Ayahudi ku Yudea.