1 Siku limojhi, Yesu wadali waima mbhepete mwa nyanja ya Genesaleti, wandhu ambili adamzongazonga kuvechela mawu ya Mnungu. 2 Wadaona mabwato yawili mbhepete mwa nyanja, iyo idasiidwa ni alovi yao adachoka kupita kukonja makoka yao. 3 Yesu wadalowa mubwato umojhi uwo udali wa Simoni, wadampembha Simoni kuti wambwanyizile kujhiwe, patali pang'ono ni mbhepete mwa nyanja. Wadayamba kuliyaluza gulu la wandhu uku wakhala mkati mwa ujha bwato. 4 Yapo wadamaliza kuyaluza, wadamkambila Simoni, "Peleka mabwato kujhiwe ni mponye makoka kuti mvuwe njhomba." 5 Simoni wadayangha, "Imwe Ambuye tachita njhito yolemecha usiku wonjhe nisitidapate chilichonjhe. Nambho, pakuti mwakamba, tiliponya khokha." 6 Yapo adaponya makoka yao mmajhi, adapata njhomba zambili mbaka makoka yao yadayamba kung'ambika. 7 Adakolosa achanjao yao adali mbwato wina kuti ajhe kwatangatila. Adafika ni adajhaza njhomba mmabwato yonjhe yawili mbaka mabwato yadali ziwaziwa. 8 Simoni Petulo yapo wadaona nchimwecho, wadagwada panjhi pamaso pa Yesu ni kukamba, "Ambuye chokani pamaso panga, chifuko ine ni mundhu wochimwa!" 9 Pakuti iye ni achanjake adazizwa kupunda pakupata njhomba zochuluka. 10 Chimwecho, Yakobo ni Yohana wana a Zebedayo, anyiiwo adali alovi achanjake a Simoni, adazizwa kupunda. Yesu wadamkambila Simoni Petulo, "Usadaopa, kuyambila lelo siuvuanjho njhomba, siukhale owapeleka wandhu kwa Ambuye." 11 Basi, yapo adachicha mabwato yajha pamtunda, adasiya kila kandhu nikumchata Yesu.
12 Ndhawi iyo Yesu wadali mu mujhi umojhi pakati pa mijhi yakumeneko, ni kumeneko kudali ni mundhu mmojhi uyo wadali vizunguluta thupi lambhumbhu. Yapo wadamuona Yesu wadagwada ni kumkwatamila, niwakamba, "Ambuye, mukafuna mkhoza kunilamicha kuti nikhoze kumlambila Mnungu." 13 Yesu wadatambasula jhanja lake ni kumgafya wodwalayo, nikumkambila, "Nifuna, ulame kuti ukhoze kumlambila Mnungu!" Ndhawi imweyo utenda udamchoka mundhu yujha. 14 Yesu wadamkambila, "Usadamkambila mundhu waliyonjhe, nambho upite ukajhilangize kwa wamkulu wanjhembe ni ukachoche mahoka ndande yakulama kwako ni kuvomelezeka ni kulamlambila Mnungu, kuti ukhale umboni kwa anyiiwo."
15 Nambho nghani za Yesu zidapunda kuwanda kila pamalo. Magulu ya wandhu ambili adasonghana kuti amvechele ni kulamichidwa matenda yawo. 16 Ata chimwecho, Yesu wadajhipatula pamalo payokha ni kupembhela.
17 Siku limojhi Yesuyapo wamayaluza wandhu, Afalisayo ni oyaluza a mathauko kuchokela kumijhi yonjhe ya Yudea ni Galilaya, ni Yelusalemu adajha pamwepo. Ni mbhamvu za Ambuye zidali ni iye kuti walamiche odwala. 18 Wandhu wina adajhanayo mundhu wopuwala uyo adamgoneka pachitala. Adayesa kumlovya mkati mwa nyumba ni kumgoneka pamaso pa Yesu. 19 Yapo adalepela kumlovya mkati ndande ya kuchuluka kwa wandhu, adakwela pachindu ni kufulumula chindhu apate malo ya kumchichila pamojhi ni chitala pakati pa wandhu pamaso pa Yesu. 20 Yapo Yesu wadaona chikhupililo chao, wadamkambila wodwala yujha, "Bwenji, walekeleledwa machimo yako."
21 Oyaluza a thauko ni Afalisayo adayamba kujhifunjha achinawene wake, "Mundhu uyu ni yani mbaka wamkhafule Mnungu? Palibe mundhu uyo wakhoza kwaalekelela wandhu machimo yao nambho Mnungu yokha!" 22 Nambho Yesu wadajhiwa maganizo yawo ni wadaafunjha, "Ndande yanji mujhifujha chimwecho mmitima yanu? 23 Chiti icho chili lahisi kupunda, kukamba, ‘Walekeleledwa machimo yako.’ Kapina kukamba, ‘Ima ujhiyenda?’ 24 Chipano nifuna mjhiwe kuti Mwana wa Mundhu wali ni ulamulilo wa kwalekelela wandhu machimo yao pano pajhiko." Pamwepo wadamkambila mudhu yujha wopuwala, "Ima, ni utenge chitala chako, upite kukhomo lako."
25 Ndhawi imweyo mudhu wopuwala yujha wadaima pamaso ya wandhu wonjhe, wadatenga chitala chake icho wamagonela nikupita kukhomo lake, uku niwamtamanda Mnungu. 26 Wandhu wonjhe adadabwa, adamtamanda Mnungu niakamba, "Lelo taona vindhu vodabwicha"
27 Yapo yadatha yameneyo, Yesu wadatuluka kubwalo ni kumuona mundhu mmojhi wamatenga malipilo uyo wamatanidwa Lawi, wadakhala panyumba yolipilila malipilo. Yesu wadamkambila, "Nichate." 28 Lawi wadanyakuka ni wadasiya yonjhe nikumchata Yesu. 29 Ndiipo lawi wadamlalika Yesu wajhe kudya phwando lalikulu kukhomo lake. Ni gulu lalikulu lotenga malipilo ni wandhu wina adajha kudya phwando. 30 Nambho Afalisayo ni oyaluza thauko yawo adachoka mmagulu yao, adawadandaulila oyaluzidwa a Yesu ponena, "Ndande yanji mkudya ni kumwa pamojhi ni otenga malipilo ni yawo ali ni machimo?" 31 Yesu wadaayangha, "Uyo siwadwala siwafuna sing'anga, nambho wodwala nde uyo wafuna sing'anga. 32 Sinidajhe kwatana wandhu yawo ali abwino pamaso pa Mnungu, nambho najha chifuko cha wandhu wochimwa kuti alekeleledwe machimo."
33 Wandhu wina adamkambila, "Oyaluzidwa a Yohana mbatizi atomanga kudya ni kupembhela ndhawi zonjhe, ni oyaluzidwa a Mafalisayo achita chimwecho. Nambho oyaluzidwa wako angokudya ni kumwa." 34 Yesu wadaayangha, "Bwanji, mganiza mkhoza kwachita alendo amwene ukwati kumanga kudya ndhawi iyo ali ni iye mwenewake? 35 Nambho nyengo itokujha yapo mwene ukwati siwatengedwe pakati pawo, pamenepo nde yapo samange kudya."
36 Yesu wadaakambila chifani ichi, "Palibe mundhu uyo wadang'amba chigamba kuchokela ku njhalu ya mpya ni kuchisokela ku njhalu yakale. Ngati saachite chimwecho, saing'ambe njhalu yampya ni chigamba chijha sichiendana ni njhalu yakaleyo. 37 Palibenjho mundhu uyo wathila divai mmatumba ya kale yayo yakojhedwa ni chikwetu. Ni ngati siwathile siwayachite chimwecho, divaisiwanangike ni matumba yachikwetu siyasweke. 38 Nambho divai ya mpya uthilidwa mmatumba yampya yachikwetu. 39 Ni palibenjho mundhu uyo wakonda kumwa divai ya mpya pambuyo pakumwa divai yakale, ndande wakamba, ‘Divai ijha yakale ni yabwino kupunda.’ "