1 Nipembha mnilimbile mtima ata pang'ono, atangati nioneka sabobwa! Nikupembhani muendekele kunilimbila mtima pang'ono. 2 Nikulondani kupunda, ngati umo wakulondelani Mnungu, anyiimwe muli ngati mwali mbeta uyo namchumbila kwa wammuna mmojhipe nde Kilisito. 3 Nambho niopa kuti, ngati njoka umo ida mnyengela Hawa kwa kuchenjela, maganizo yanu yakhoza kuwanangidwa, mwakusiya kukhulupika kwanu kwa uzene wa Kilisito. 4 Mundhu waliyonjhe uyo wakujha kwanu nikulalikilani uthenga wa Yesu mwina uyo sitidamlalikile, kapina mkaulandila mzimu wina uwo simudaulandile, kapina kukulalikilani Uthenga Wabwino wina kulekana ni ujha tidakulalikilani.
5 Sinijiona kuti ine wamng'ono kusiyana achameneo, "Atumwi wakulu." 6 Ata ngati sinikoza kukamba bwino, nambho nijhiwa vindhu vambili. Chindhu ichi tachilangiza kwanu ndhawi yonjhe ni kila pamalo.
7 Bwanji, nidachita kuipa? Ine nidauzila Uthenga Wabwino wa Mnungu kwanu, popande kudai mkokolo nidajhichicha nikukwezeni anyiimwe. 8 Yapo nimakuchitilani njhito anyiimwe, nidalandila mthandizo wa vofunika vanga kuchokela kwa wandhu wina adamkhulupilila Yesu. Nidalanda chuma chao kukutumikilani anyiimwe. 9 Yapo nidali pamojhi namwe sinida mchauche waliyonjhe yapo nimafuna ndalama, okhulupilila anjanu akumujhi wa Makedonia anipacha kila icho nifuna. Nimapenyechecha dala sinidakuchauchani ni siniendekele kuchitanchimwecho. 10 Palibe mundhu ata mmojhi wa mumujhi wa Akaya, ambayo siwanichekeleze kujhielekela nghani imeneyo, nikamba chimwecho pakuti uzene wa Kilisito uli mkati mwanga. 11 Nikamba chimwecho ndande yanji? Ndande sinikukondani? Mnungu wajhiwa kuti nikukondani. 12 Siniendekele kuchita ngati umo nichitila chipano, dala yao afunafuna malo sadapata, malo yojhielekela kuti apota njhito ngati ife. 13 Achameneo atumwi amthila, anyiyao anyenga njhito zao, yao niajhichita achinawene kuti atumwi auzene a Kilisito. 14 Simdadabwa, pakuti ata satana mwene wadajhichita mtumiki wa dandangalila wa kumwamba. 15 Chimwecho siidabwicha, pakuti ata atumiki asatana ajhichita kuti atumiki abwino pachogolo pa Mnungu. Pothela sapate icho afunikila kuchipata kuchatana ni vichito vao.
16 Nikambanjho chimwechi, mundhu waliyonjhe siwadaniona ine sabobwa. Nambho atangati muniganizila chimwecho, munivomele ngati sabobwa, dala nane nipate kujhielekela. 17 Icho nichikamba chipano asati agizo la Ambuye, nambho chindhu ichi nde icho nijhidamila, nambho nikambape ngati sabobwa, 18 pakuti wandhu ambili achita dama ndande ya jhiko, nanenjho sinichite dama. 19 Anyiimwe ndande anjelu nde ndande mwavomeleza asabobwa. 20 Mumlimbila mtima mbaka mundhu uyo wakuchitani kukhala akapolo, kapina mundhu uyo wakulandani vindhu vanu, wapata vindhu kwa phindu lake mwene, kapina kujhikweza mwene kapina kukunyengani. 21 Niona njhoni kukamba kuti ife tidali anyondi kuvichita vindhu vimenevo.
Nambho ngati kuli mundhu waliyonjhe waesa kujhidamila chindhu, nikamba ngati opusa nane siniese. 22 Bwanji, anyiiwo ni Ahebulania? Nanenjho ni Muhebulania. Bwanji, anyiiwo ni Aizilaeli? Nanenjho Muizilaeli. Bwanji, anyiiwo ni mbadwa wa ibulahimu? Nanenjho mbadwa wa Ibulahimu. 23 Anyiiwo ni atumiki a kilisito? Nikamba ngati wamsala, ine ni mtumiki wa Kilisito kupitilila anyiiwo. Nachita njhito yolimba kupunda, namangidwa mndende mala zambili, nabulidwa mikwapulo kupunda, nawandikilidwa ni nyifa kupitilila anyiiwo. 24 Mala kasano nabulidwa mikwapulo, nikila yapo nimabulidwa, nimabulidwa mikwapulo selasina ni tisa ni Ayahudi. 25 Nida tyapidwa katatu ni Alumi nidabulidwa myala kamojhi, sitima yaniwanangikila katatu mnyanja nchele, nidakhala chonga mmajhi usiku usana. 26 Mmaulendo mala zambili nazengedwa ni mafuliko ya majhi, nidavutika kwa kubulidwa ni anghungu, nidavutika kuchokela kwa wandhu ajhiko langa, nidavutika kuchokela kwa wandhu amaiko ina, nidavutika mmijhini, nidavutika mmatengo, nidavutika mnyanja nchele, nidavutika kuchokela kwa achabale aunami. 27 Nachita njhito ni kulaga, nachezelela mala zambili, nakhala ni njala ni lujho mala zambili, nidakosa chakudya mala zambili ni kukhala mozizila popande njhalu. 28 Kupitilila yameneyo yonjhe, siku zonjhe niganizila nghani za magulu yonjhe ya wandhu amkhulupilila Yesu. 29 Ngati mundhu waliyonjhe wali wa nyondi, nanenjho wanyondi, mundhu waliyonjhe wakachitichidwa kuchita machimo, nanenjho nikhala ni mandha. 30 Ikanifuna kujhielekela nanenjho, nijhielekele ndande ya unyondi wanga. 31 Mnungu wa Ambuye wathu Yesu jhina lake lilemekezedwe muyaya, iye wajhiwa kuti sinikamba unami. 32 Yapo nidali kumujhi wa Damasiko, wamkulu wa mujhi, uyo wamamthangatila mfumu Aleta, wadaika wandhu pavicheko va mijhi dala wanigwile. 33 Nambho, nidamthawa kwa kuchichidwa kwa kutumila mumseche waukulu, kupitila dilisha la paphupha.