1 Ife sitifuna kujielekela tachinawefe. Sitifuna kalata zovomelezeka kuchokela kwanu, kapina kuchokela kwaife kujha kwanu ngati wandhu wina umo achitila. 2 Anyiimwe nde kalata yathu iyo yalembedwa mmitima yathu dala kila mundhu waijhiwe ni kuisoma. 3 Uzene ni kuti anyiimwe nde kalata yalembedwa ni Kilisito iyo yapelekedwa kupitila ife. Siidalembedwe kwa wino, nambho yalembedwa kwa Mzimu wa Mnungu uyo wali wa Moyo, siidalembedwe pa chibandhu cha mwala, nambho yalembedwa mmitima mwanu.
4 Uku nde kupilila uko tilinako pamaso pa Mnungu kwa kupitila yajha wadayachita Kilisito. 5 Ife sitikhoza kalikonjhe kwa mbhavu zathu tachinawefe, nambho mbhavu zathu zichoka kwa Mnungu. 6 Iye nde uyo watikhozecha ife kukhala wotumikila pangano la chipano ilo osati pangano la thauko ilo lilembedwa, nambho pangano la Mzimu wa Mnungu. Pakuti thauko lalembedwa lipeleka nyifa, nambho Mzimu wa Mnungu upeleka umoyo.
7 Ikakhala thauko ilo lipeleka nyifa, thauko lijha lidalembedwa pamwamba pa vibandhu va myala lidajha kwa ulemelelo wa wake, mbaka wandhuu aku Izilaeli adalepela kuipenya nghope ya Musa ndande ya ulemelelo wa thauko limenelo. Ingakhale ulemelelo umeneo udali wofikilila, 8 utumiki wa Mzimu wa Mnungu ukhala ni ulemelelo waukulu kupunda. 9 Chimwecho, ngati kudali ni ulemelelo wa utumiki uwo uchita wandhu alangidwe, ijhiwikilatu kuti utumiki uwo uchita wandhu avomelezeke kwa Mnungu siukhale ni ulemelelo wa ukulu kupunda. 10 Chimwecho ujha ulemelelo wa Pangano la Kale lachocheka, ndande ulemelelo wa Pangano la Chipano wajha uwo uli waukulu kupunda. 11 Ikakhala chijha chidali cha ndhawi yochepape chidali ni ulemelelo wake, bwanji sichikhala ni ulemelelo kupunda icho chikhala muyaya?
12 Tili ni kulimba mtima kupunda pakuti tili ni chikhulupililo cha mtundu uwu. 13 Ife osati ngati Musa uyo wadaivinikila nghope yake kwa chitambaa dala a Izilaeli sadaona mathelo ya kung'azikila uko kumafikilila. 14 Nambho njelu zao zidabwabwazidwa. Mbaka lelo yapo lisomedwa Pangano la kale, chivuniko chimenecho chikali. Chivuniko chimenecho chichochedwape mundhu yapo walunjana ni Kilisito. 15 Yetu, mbaka lelo kila yapo lisomedwa thauko la Musa njelu zao zikhala zavinikilidwa. 16 Nambho mundhu yapo waakhulupilila Ambuye Mnungu chivinikilo chimenecho chichochedwa. 17 Yapa "Ambuye" nde Mzimu, ni yapo wali Mzimu wa Ambuye nde yapo pali ufulu. 18 Chimwecho, ife yao nghope zathu sizidavinikilidwe, tiuona ulemelelo wa Ambuye, ngati mukiyoo. Njhito ya Mzimu wa Ambuye iting'anamucha ife tilingane kupunda ni chifani chake kuchoka ulemelelo mbaka ulemelelo waukulu kupunda.