1 Kano kakatatu kujha kwanu ngati umo yalembedwa mamalembo ya Mnungu, "Kila choipa sichichimikizidwe kwa umboni wa wandhu awili kapina atatu," 2 nidatho kuonyani, yapo nidali namwe pa ulendo wakawili, nikambanjho yapo nili patali, onjhe yao achita voipa popande kulapa, ni wina onjhe yapo sinijhe sinikhala ni lisungu. 3 Simuone mwachinawene Kilisito wakamba mkati mwanga. Kwathu Kilisito asati wanyondi, nambho mbhavu yake ichita njhito pakati panu. 4 Ata ngati wapachikidwa pamtanda ndande ya unyondi, nambho wakhala moyo chipano kwa mbhavu za Mnungu. Ife nafe tili anyondi kwa kulunjana nayo, nambho tikhala moyo kwa mbhavu za Mnungu izo zili kwa anyiimwe.
5 Jipenyechecheni mwachinawene mujhiwe ngati mukhulupilila. Jhichimikizeni mwachinawene. Bwanji simujhiwa kuti Kilisito wali mkati mwanu? Ngati asati chimwecho mwalepela. 6 Nambho nikhulupilila kuti anyiimwe mujhiwa kuti ife sitidalepele. 7 Timpembha Mnungu simdalakwa chalichonjhe, nambho asati ndande tioneke kwa wandhu kuti takhoza, nambho tichite vabwino, ata ngati ife tioneka kuti talepela. 8 Sitikhoza kulimbana ni uzene, nambho kuuchimikiza uzene. 9 Tikondwela kukhala ngati wandhu anyondi, nambho anyiimwe muli ni mbhavu, chimwecho timpembha Mnungu mkhale okwanila kwa kila chindhu. 10 Ndipo nakulembelani kalata iyi nili kutali, dala yapo sinifike kwanu sinidakhala wokalipa kwa mbhavu izo anipacha Ambuye, Ambuye anipacha mbhavu yomanga asati yogomola.
11 Chipano, achabale, nikulailani! Mkhale okwanila, gwilani mayaluzo yanga, mkhale chindhu chimojhi, mkhale kwa mtendele. Mnungu wa chikondi ni mtendele siwakhale pamojhi namwe.
12 Pajha mpezana mlonjelane kwa chikondi cha chikondi.
13 Wandhu wonjhe a Mnungu kumeneko akulonjelani.
14 Nikufunilani ubwino wa Ambuye Yesu Kilisito ni chikondi cha Mnungu ni umojhi wa Mzimu wa Mnungu, vikhale namwe mwaonjhe.